Azondi achiisrayeli atanyamula zipatso

TAONANI zipatso zimene amuna’wa anyamula. Taonani kukula kwa tsango la mphesa’zo. Litofunikira anthu awiri kulinyamula mopika. Ndipo taonani nkhuyu’zo ndi makangaza. Kodi chipatso chokongola’chi chinachokera kuti? Ku dziko la Kanani. Pajatu, Kanani ndiko kumene Abrahamu, Isake ndi Yakobo anakhala pa nthawi ina. Koma chifukwa cha njala kumene’ko, Yakobo ndi banja lake, anasamukira ku Igupto.

Tsopano, zaka 216 pambuyo pake, Mose akutsogolera Aisrayeli kubwerera ku Kanani. Iwo afika pa malo m’chipululu’cho ochedwa Kadesi.

Anthu oipa anakhala m’kanani. Chotero Mose akutumiza azondi 12, nawauza kuti: ‘Kaoneni kuchuluka kwa anthu kumene’ko, ndi m’mene aliri amphamvu. Kaoneni ngati dziko’lo liri la dzinthu. Ndipo katengeni zina za zipatso zake.’

Pamene azondi’wo akubwerera ku Kadesi, akuuza Mose kuti: ‘Ndi dziko labwino’di.’ Ndipo kuti asonyeze, iwo akusonyeza Mose zina za zipatso’zo. Koma 10 mwa azondi’wo akuti: ‘Anthu okhalamo ndi akulu-akulu ndi amphamvu. Tidzaphedwa ngati tiyesa kulanda dziko’lo.’

Aisrayeli akuopa pakumva izi. ‘Kukanakhala bwino kufera mu Igupto kapena ngakhale m’chipululu muno,’ iwo akutero. ‘Tidzaphedwa m’nkhondo, ndipo akazi ndi ana athu adzagwidwa. Tiyeni tisankhe m’tsogoleri watsopano m’malo mwa Mose, ndi kubwerera ku Igupto!’

Koma awiri mwa azondi’wo akudalira mwa Yehova, ndipo akuyesa kutontholetsa anthu’wo. Maina ao ndiwo Yoswa ndi Kalebi. Iwo akuti: ‘Musaope. Yehova ali nafe. Kudzakhala kosabvuta kulanda dziko’lo.’ Koma anthu’wo sakumvetsera. Akufuna kupha Yoswa ndi Kalebi.

Numeri 13:1-33; 14:1-38.Mafunso

  • Kodi zipatso za nkhuyu zimene zili m’chithunzichi zikuoneka zotani, ndipo kodi zinachokera kuti?
  • N’chifukwa chiyani Mose akutuma azondi 12 ku dziko la Kanani?
  • Kodi azondi 10 akunena chiyani atabwerera kwa Mose?
  • Kodi azondi aŵiri akusonyeza bwanji kuti anadalira Yehova, ndipo kodi maina awo ndi ndani?
  • N’chifukwa chiyani Yehova wakwiya, ndipo kodi akuuza Mose chiyani?

Mafunso ena