PAFUPI-FUPI miyezi iwiri atatuluka mu Igupto, Aisrayeli akufika pa Phiri la Sinai, limene likuchedwa’nso Horebi. Ndi pa malo omwewa pamene Yehova analankhulapo ndi Mose m’chitsamba choyaka moto. Anthu anamanga mahema pano nakhalapo kwa kanthawi.

Anthu akuyembekezera pansipo, Mose akukwera m’phirimo. Pamwambapo, Yehova akuuza Mose kuti Iye akufuna kuti Aisrayeli amvere Iye ndi kukhala anthu Ake apadera. Pamene Mose akutsika, akuuza Aisrayeli zimene Yehova wanena. Anthu’wo akuti adzamvera Yehova, chifukwa akufuna kukhala anthu ake.

Yehova tsopano akuchita chinthu chodabwitsa. Akuchititsa pamwamba pa phiri’lo kuchita utsi, ndi mphezi. Iye akulankhula’nso ndi anthu’wo kuti: ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani m’dziko la Igupto.’ Nawalamula kuti: ‘Musamalambira milungu ina koma ine ndekha.’

Miyala iwiri

Iye akupatsa Aisrayeli malamulo ena asanu ndi anai. Anthu’wo akuopa kwambiri. Iwo akuuza Mose kuti: ‘Inu mulankhule nafe, chifukwa tiopa kuti ngati Mulungu alankhula nafe tingafe.’

Kenako Yehova akuuza Mose kuti: ‘Kwera ku phiri kuno. Ndidzakupatsa miyala iwiri yaphanthi-panthi imene ndalembapo malamulo amene ndikufuna kuti anthu awasunge.’ Chotero Mose akukwera’nso ku phiri. Akukhalako kwa mausana ndi mausiku 40.

Mulungu ali ndi malamulo ochuluka kwambiri kaamba ka anthu ake. Mose akulemba malamulo’wa. Mulungu akum’patsa’nso miyala iwiri’yo. Mulungu mwini walembapo malamulo 10 amene iye ananena ndi anthu onse. Iwo akuchedwa Malamulo Khumi.

Mose ali pa Phiri la Sinai

Iwo ali malamulo ofunika. Chimodzi-modzi’nso malamulo ena ambiri’wo amene Mulungu anapatsa Israyeli. Limodzi la malamulo’wa ndiro: ‘Udzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, maganizo ako onse, moyo wako wonse ndi nyonga yako yonse.’ Lina ndiro: ‘Udzikonda mnansi wako monga momwe umadzikondera.’ Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anati awa ndiwo malamulo awiri akulu kopambana amene Yehova anapatsa anthu ake Israyeli. Kenako tidzaphunzira zinthu zambiri ponena za Mwana wa Mulungu ndi ziphunzitso zake.

Ekisodo 19:1-25; 20:1-21; 24:12-18; 31:18; Deuteronomo 6:4-6; Levitiko 19:18; Mateyu 22:36-40.Mafunso

  • Pafupifupi miyezi iŵiri chichokereni ku Igupto, kodi Aisrayeli akumanga kuti mahema awo?
  • Kodi Yehova akunena kuti akufuna kuti anthuwo achite chiyani, ndipo anthuwo akuyankha chiyani?
  • N’chifukwa chiyani Yehova akupatsa Mose miyala iŵiri yaphanthiphanthi?
  • Kupatulapo Malamulo Khumi, kodi ndi malamulo ena ati amene Yehova anapatsa Aisrayeli?
  • Kodi ndi malamulo aŵiri ati amene Yesu Kristu ananena kuti ndi aakulu kupambana ena onse?

Mafunso ena