MOSE atabwerera ku Igupto, anauza mkulu wake Aroni zonse ponena za zozizwitsa’zo. Ndipo Mose ndi Aroni atazisonyeza kwa Aisrayeli, anthu onse akukhulupirira kuti Yehova anali nawo.

Ndiyeno Mose ndi Aroni anamka kukaonana ndi Farao. Iwo anamuuza kuti: ‘Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, “Lola anthu anga apite kwa masiku atatu, kuti akandilambire m’chipululu.” Farao anayankha nati: ‘Sindikhulupirira Yehova. Ndipo sindidzalola Israyeli apite.’

Farao anakwiya, chifukwa anthu’wo anafuna nthawi ya kusakhala pa ntchito kuti akalambire Yehova. Chotero anawaumiriza kugwira ntchito mwamphamvu koposa kale. Aisrayeli anasuliza Mose pa kuchitiridwa kwao moipa, ndipo Mose anamva chisoni. Koma Yehova anamuuza kusadera nkhawa. ‘Ndidzam’chititsa kuwalola kupita,’ anatero Yehova.

Mose ndi Aroni atapita kukaonana ndi Farao

Mose ndi Aroni anakaona’nso Farao. Nthawi ino iwo akuchita chozizwitsa. Aroni anaponya pansi ndodo yake, nikhala chinjoka. Koma amatsenga a Farao nawo’nso anaponya zao, nazionekera njoka. Koma, onani! Njoka ya Aroni ikumeza njoka za amatsenga’wo. Farao sakulolabe Aisrayeli kumuka.

Nthawi inafika kenako yoti Yehova aphunzitse Farao phunziro. Kodi mukudziwa m’mene anachitira? Kunali mwa kudzetsa miriri 10, kapena zobvuta zazikulu, pa Igupto.

Miriri yambiri itachitidwa, Farao akuitana Mose, nati: ‘Letsa mliri’wo, ndipo ndidzawalola amuke.’ Koma utaleka mliri’wo, Farao ankasintha maganizo ake. Sankalola anthu’wo kumuka. Koma, kenako, utatha mliri wa 10, Farao akulola Aisrayeli kumuka.

Kodi mukudziwa uli wonse wa miriri 10’yo? Tiyeni tione.

Ekisodo 4:27-31; 5:1-23; 6:1-13, 26-30; 7:1-13.Mafunso

  • Kodi zozizwitsa zimene Mose ndi Aroni anachita zinawakhudza motani Aisrayeli?
  • Kodi Mose ndi Aroni anauza Farao chiyani, ndipo kodi Farao anayankha kuti chiyani?
  • Monga momwe asonyezera pachithunzipa, kodi Aroni ataponya ndodo yake pansi chinachitika n’chiyani?
  • Kodi Yehova anaphunzitsa bwanji Farao phunziro, ndipo kodi Farao anachitapo chiyani?
  • Kodi chinachitika n’chiyani mliri wachikhumi utatha?

Mafunso ena