Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 30: Chitsamba Choyaka Moto

Nkhani 30: Chitsamba Choyaka Moto

MOSE anali atafika ku phiri la Horebi kudzapezera nkhosa zake nsipu. Pano iye anaona chitsamba chikuyaka moto, koma chosanyeka!

Mose ali pafupi ndi chitsamba choyaka moto

‘Izi n’zodabwitsa,’ anaganiza choncho Mose. ‘Ndidzasendera pafupi ndikaonetsetse.’ Atatero, mau anachokera m’chitsamba’cho, akuti: ‘Usayandikire pano. Bvula nsapato zako, chifukwa waima pa malo oyera.’ Anali Mulungu amene analankhula mwa njira ya mngelo, chotero Mose anaphimba nkhope yake.

Ndiyeno Mulungu anati: ‘Ndaona kubvutika kwa anthu anga m’Igupto. Chotero ndidzawalanditsa, ndipo iwe ndi amene ndidzakutuma kukawatulutsa m’Igupto.’ Yehova akalowetsa anthu ake m’Kanani wokongola’yo.

Mose anati: ‘Ine ndine yani. Kodi ndingachite izi motani? Koma tiyeni titi ndapita. Aisrayeli nadzati kwa ine, “Wakutuma ndani?” pamenepo ndidzanenanji?’

‘Izi ndizo zimene ukanene,’ anayankha motero Yehova. ‘“YEHOVA Mulungu wa Abrahamu, wa Isake ndi wa Yakobo wandituma kwa inu.”’ Yehova anati’nso: ‘Iri ndiro dzina langa kosatha.’

‘Koma tiyeni titi sakundikhulupirira nditanena kuti mwandituma,’ anatero Mose.

Mulungu anafunsa kuti, ‘M’dzanja lako muli chiani?’

Mose anayankha kuti: ‘Ndodo.’

Mulungu anati, ‘Iponye pansi.’ Ataiponya inasanduka njoka. Kenako anam’sonyeza chozizwitsa china. Iye anati: ‘Ika dzanja lako mu mkanjo wako.’ Mose anachita, ndipo potulutsa dzanja lake, linali loyera ngati chipale! Dzanja linaoneka ngati linali ndi khate. Kenako Yehova anam’patsa mphamvu ya kuchita chozizwitsa chachitatu. Nati: ‘Aisrayeli akakaona zozizwitsa’zi adzakhulupirira kuti ndakutuma.’

Ndiyeno Mose anamka kwa Yetero nati: ‘Chonde ndiloleni ndimke kwa achibale anga m’Igupto ndikaone m’mene aliri.’ Yetero anayankha nati pita bwino, ndipo Mose ananyamuka kubwerera ku Igupto.

Ekisodo 3:1-22; 4:1-20.Mafunso

  • Kodi phiri limene lili pa chithunzipa dzina lake n’chiyani?
  • Fotokozani chinthu chodabwitsa chimene Mose anaona atapita kuphirili ndi nkhosa zake.
  • Kodi mawu ochokera pa chitsamba choyaka moto anati chiyani, ndipo anali mawu a ndani?
  • Kodi Mose anayankha bwanji Mulungu atamuuza kuti adzatsogolera anthu a Mulungu kuchoka ku Igupto?
  • Kodi Mulungu anauza Mose kuti akanene chiyani anthu akakamufunsa amene anamutuma?
  • Kodi Mose akanatha bwanji kupereka umboni woti Mulungu anamutuma?

Mafunso ena