Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 27: Mfumu Yoipa Ilamula Igupto

Nkhani 27: Mfumu Yoipa Ilamula Igupto

AMUNA’WA pano akuumiriza anthu kugwira ntchito. Mukuona uyo amene akumenya n’chikoti mmodzi wa antchito’wo! Antchito’wo ali a banja la Yakobo, ochedwa Aisrayeli. Oumiriza ntchito’wo ndiwo Aigupto. Aisrayeli akhala akapolo a Aigupto. Kodi zinachitika motani?

Aiguputo akuzunza Aisiraeli

Kwa zaka zambiri banja lalikulu la Yakobo linali mu mtendere mu Igupto. Yosefe, amene anali wachiwiri kwa mfumu Farao uja, anawasamalira. Komano Yosefe anafa. Ndipo Farao watsopano amene sanakonde Aisrayeli, anakhala mfumu mu Igupto.

Chotero Farao woipa’yu anapanga Aisrayeli kukhala akapolo. Naika amuna owayang’anira amene anali oipa ndi ankhanza. Iwo anakakamiza Aisrayeli kugwira ntchito zolimba kumangira Farao mizinda. Koma Aisrayeli anapitirizabe kuonjezeka. Katapita kanthawi Aigupto anaopa kuti Aisrayeli akakhala ochuluka kwambiri ndi amphamvu kwambiri.

Aiguputo akuzunza Aisiraeli

Kodi mukudziwa chimene Farao anachita? Anauza akazi othandiza amai Achiisrayeli pobala ana kuti: ‘Muzipha mwana wamwamuna ali yense wobadwa.’ Koma awa anali akazi abwino, ndipo sanaphe ana’wo.

Chotero Farao analamula anthu ake onse kuti: ‘Iphani makanda achimuna a Israyeli. Siyani ana akazi okha.’ Kodi izi sizinali zoopsya kuzilamula? Tiyeni tione m’mene mwana wamwamuna wina anapulumutsidwira.

Ekisodo 1:6-22.Mafunso

 • Pachithunzipa, kodi mwamuna amene ali ndi chikotiyo ndi ndani, ndipo kodi akumenya ndani?
 • Yosefe atamwalira, kodi chinachitika n’chiyani kwa Aisrayeli?
 • N’chifukwa chiyani Aigupto anayamba kuopa Aisrayeli?
 • Kodi Farao analamula akazi amene ankathandiza azimayi achiisrayeli pobereka kuti azichita chiyani?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Ekisodo 1:6-22.

  Kodi Yehova anayamba kukwaniritsa lonjezo lake kwa Abrahamu m’njira yotani? (Eks. 1:7; Gen. 12:2; Mac. 7:17)

  Kodi akazi achihebri othandiza azimayi pobereka anasonyeza bwanji kuti analemekeza kupatulika kwa moyo? (Eks. 1:17; Gen. 9:6)

  Kodi akazi othandiza azimayi poberekawo anadalitsidwa bwanji chifukwa cha kukhulupirika kwawo kwa Yehova? (Eks. 1:20, 21; Miy. 19:17)

  Kodi Satana anayesera bwanji kulepheretsa cholinga cha Yehova chokhudza Mbewu yolonjezedwa ya Abrahamu? (Eks. 1:22; Mat. 2:16)