Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 20: Dina Alowa M’bvuto

Nkhani 20: Dina Alowa M’bvuto

KODI mukuona amene Dina akukacheza nawo? Akumka kukaona atsikana ena okhala m’Kanani. Kodi atate wake akakondwera nazo? Kuti tiyankhe funso’li, tiyeni tikumbukire zimene Abrahamu ndi Isake anaganiza ponena za akazi a m’Kanani.

Dina wapita kukacheza ndi atsikana a ku Kanani

Kodi Abrahamu anafuna kuti Isake akwatire mtsikana wa M’Kanani? Ai. Kodi Isake ndi Rebeka anafuna kuti mwana wao Yakobo akwatire mtsikana wa m’Kanani? Ai. Kodi mukudziwa chifukwa chake?

N’chifukwa chakuti Akanani analambira milungu yonyenga. Iwo sanali anthu abwino kukwatiwa nawo kapena kuwakwatira, ndipo sanali anthu abwino kuyanjana nawo. Chotero tingakhale otsimikizira kuti Yakobo sakakondwera kuti mwana wake wamkazi anali kupalana ubwenzi ndi atsikana Achikanani’wa.

Ndithudi, Dina analowa m’bvuto. Kodi mukuona mwamuna Wachikanani uyo amene akuyang’ana Dina? Dzina lake ndi Sekemu. Tsiku lina pamene Dina anadza kudzacheza, Sekemu anam’nyenga nam’kakamiza kugona naye. Izi zinali zolakwa, chifukwatu ndiwo amuna ndi akazi okwatirana okha amene ayenera kugona pamodzi. Choipa chochitidwa ndi Sekemu’chi chinachititsa mabvuto ochuluka kwambiri.

Pamene abale a Dina anamva za chochitika’chi, anapsya mtima kwambiri. Awiri a iwo Simeoni ndi Levi, anakwiya kwambiri kwakuti anatenga malupanga nalowa mu mzinda’wo natulukira amuna’wo modzidzimutsa. Iwo ndi abale ao anapha Sekemu ndi amuna ena onse. Yakobo anapsya mtima chifukwa chakuti ana ake anachita choipa’chi.

Kodi bvuto lonse’li linayamba bwanji? N’chifukwa chakuti Dina anapalana ubwezi ndi anthu osamvera malamulo a Mulungu. Sitidzafuna kupanga mabwenzi otero’wo kodi si choncho?

Genesis 34:1-31.Mafunso

 • N’chifukwa chiyani Abrahamu ndi Isake sanafune kuti ana awo akwatire anthu a m’dziko la Kanani?
 • Kodi Yakobo anasangalala kuti mwana wake wamkazi azicheza ndi atsikana achikanani?
 • Kodi mwamuna amene akuyang’ana Dina m’chithunzichi ndi ndani, ndipo kodi anachita chinthu choipa chotani?
 • Kodi azichimwene a Dina, Simeoni ndi Levi, anachita chiyani atamva zimene zinachitikazo?
 • Kodi Yakobo anagwirizana ndi zimene Simeoni ndi Levi anachita?
 • Kodi mavuto onse a m’banjali anayamba bwanji?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Genesis 34:1-31.

  Kodi nthaŵi imene Dina anakacheza ndi atsikana a m’dziko la Kanani inali yokhayo basi? Fotokozani. (Gen. 34:1)

  N’chifukwa chiyani tinganene kuti Dina mbali ina anachita kuziputa dala kuti agonedwe ndi mwamuna? (Agal. 6:7)

  Kodi achinyamata masiku ano angasonyeze bwanji kuti aphunzirapo kanthu pa chitsanzo chochenjeza cha Dina? (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33; 1 Yoh. 5:19)