Yakobo ndi ana ake aamuna

TANGOYANG’ANANI pa banja lalikulu’li. Awa ndiwo ana amuna 12 a Yakobo. Iye anali’nso ndi ana akazi. Kodi mukudziwa maina ao? Tiyeni tiphunzire ena a iwo.

Leya anabala Rubeni, Simeoni, Levi ndi Yuda. Rakele poona kuti sanali kubala ana, anali wachisoni kwambiri. Chotero anapereka mdzakazi wake Biliha kwa Yakobo, ndipo Biliha anabala Dani ndi Nafitali. Naye’nso Leya anapereka mdzakazi wake Zilipa kwa Yakobo, Zilipa nabala Gadi ndi Aseri. Kenako Leya anabala ana amuna ena awiri, Isakara ndi Zebulono.

Kumapeto Rakele anabala mwana. Anam’cha Yosefe. Kenako timaphunzira zochuluka ponena za Yosefe, chifukwa anakhala wofunika kwambiri. Awa ndiwo ana 11 amene Yakobo anabala ali ndi atate wa Rekele Labani.

Yakobo anali’nso ndi ana akazi, koma Baibulo limachula dzina la mmodzi yekha. Ndiye Dina.

Inafika nthawi yakuti Yakobo alekane ndi Labani ndi kubwerera ku Kanani. Chotero anasonkhanitsa banja lake lalikulu’lo ndi zifuyo zake zonse nkhosa ndi ng’ombe, nayamba ulendo wautali’wo.

Iye ndi banja lake atakhala kanthawi m’Kanani. Rakele anabala mwana wina wamwamuna. Zinachitika ali pa ulendo. Rakele anabvutika, ndipo potsirizira pake anafa akubala. Koma kamwana’ko kanali bwino. Yakobo anam’cha Benjamini.

Tikufuna kukumbukira maina a ana 12 a Yakobo chifukwa chakuti mtundu wonse wa Israyeli unachokera mwa iwo. Mafuko 12 a Israyeli akuchedwa maina a ana 10 a Yakobo ndi awiri a Yosefe. Isake anakhala zaka zambiri anyamata onse’wa atabadwa, ndipo ziyenera kukhala zitam’pangitsa kukhala wokondwa kukhala ndi zidzukulu zambiri. Koma tiyeni tione zimene zinachitikira mdzukulu wake Dina.

Genesis 29:32-35; 30:1-26; 35:16-19; 37:35.Mafunso

 • Kodi ana aamuna sikisi amene mkazi woyamba wa Yakobo, Leya, anamuberekera mayina awo anali ndani?
 • Kodi Zilipa, mdzakazi wa Leya, anaberekera Yakobo ana aamuna aŵiri ati?
 • Kodi ana aamuna aŵiri amene mdzakazi wa Rakele, Biliha, anaberekera Yakobo mayina awo anali ndani?
 • Kodi Rakele anabereka ana aamuna aŵiri ati, ndipo n’chiyani chinachitika pamene anali kubereka mwana wamwamuna wachiŵiriyo?
 • Malinga ndi chithunzichi, kodi Yakobo anakhala ndi ana aamuna angati, ndipo n’chiyani chinachokera mwa iwo?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Genesis 29:32-35; 30:1-26; ndi 35:16-19.

  Malinga ndi mmene zinachitikira ndi ana aamuna a Yakobo khumi ndi aŵiri, kodi anyamata achihebri kale ankawatcha maina motani?

 • Ŵerengani Genesis 37:35.

  Ngakhale kuti ndi Dina yekha amene watchulidwa m’Baibulo, kodi tikudziŵa bwanji kuti Yakobo anali ndi ana ena aakazi? (Gen. 37:34, 35)