Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 18: Yakobo Amka ku Harana

Nkhani 18: Yakobo Amka ku Harana

KODI mukudziwa amuna awa amene Yakobo akulankhula nawo? Atayenda masiku ambiri, Yakobo anawapeza pafupi ndi chitsime. Iwo anali kuweta nkhosa zao. Yakobo anafunsa kuti: ‘Kwanu n’kuti?’ Iwo anati, ku ‘Harana.’

Yakobo anafunsa kuti, ‘Kodi Labani mumam’dziwa?’

Iwo anayankha kuti, ‘Inde. Uyo, adza apo’yo ndi mwana wake wamkazi Rakele ndi gulu lake la nkhosa.’ Kodi mukuona Rakele akudza chauko’yo?

Pamene Yakobo anaona Rakele ndi nkhosa za malume wake Lebani, anamka nakunkuniza mwala pa chitsime kuti nkhosa zimwe. Ndiyeno Yakobo anapsyompsyona Rakele namuuza kuti iye anali yani. Anali wochititsidwa nthumanzi kwambiri, ndipo anamka kunyumba nauza atate wake Labani.

Yakobo akukumana ndi Rakele

Labani anali wokondwa kwambiri kuti Yakobo adzakhale naye. Ndipo pamene Yakobo anapempha kuti akwatire Rakele, Labani anakondwa. Komabe, anapempha Yakobo kugwira ntchito m’munda mwake kwa zaka zisanu ndi ziwiri kaamba ka Rakele.

Chifukwa anakonda Rakele kwambiri Yakobo anachita izi. Koma nthawi ya ukwati itakwana, kodi mukudziwa chimene chinachitika?

Labani anapatsa Yakobo mwana wake wamkazi wamkulu Leya m’malo mwa Rakele. Pamene Yakobo anabvomereza kugwirira ntchito Labani zaka zina zisanu ndi ziwiri, anam’patsa’nso Rakele akhale mkazi wake. M’nthawiyo Mulungu analola amuna kukhala ndi akazi oposa mmodzi. Koma tsopano, monga momwe Baibulo likunenera, mwamuna ayenera kukhala ndi mkazi mmodzi yekha.

Genesis 29:1-30.Mafunso

 • Kodi mkazi wachitsikana amene ali m’chithunzichi ndi ndani, ndipo kodi Yakobo anamuchitira chiyani?
 • Kodi Yakobo anali wokonzeka kuchita chiyani kuti akwatire Rakele?
 • Kodi Labani anachita chiyani nthaŵi yoti Yakobo akwatire Rakele itakwana?
 • Kodi Yakobo anavomera kuchita chiyani kuti akwatire Rakele?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Genesis 29:1-30.

  Ngakhale pamene Labani anamuchitira zachinyengo, kodi Yakobo anasonyeza bwanji kuti anali munthu wodzisungira ulemu, ndipo kodi tingaphunzire chiyani pa zimenezi? (Gen. 25:27; 29:26-28; Mat. 5:37)

  Kodi chitsanzo cha Yakobo chimasonyeza bwanji kusiyana kwa chikondi chenicheni ndi chikondi chonyenga? (Gen. 29:18, 2030; Nyimbo 8:6)

  Kodi ndi akazi anayi ati amene anadzakhala mbali ya banja la Yakobo kenaka n’kumuberekera ana aamuna? (Gen. 29:23, 24, 28, 29)