Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 17: Amapasa Amene Anali Osiyana

Nkhani 17: Amapasa Amene Anali Osiyana
Esau

ANYAMATA awiri pano ali osiyana kwambiri, kodi si choncho? Kodi mukudziwa maina ao? Mpalu’yu ndi Esau, ndi mbusa wa nkhosa’yo ndiye Yakobo.

Esau ndi Yabobo anali ana amapasa a Isake ndi Rebeka. Atate’yo, Isake, anakonda kwambiri Esau, chifukwa anali mpalu wabwino ndipo ankadza ndi zakudya za banja’lo. Koma Rebeka anakonda Yakobo kopambana, chifukwa anali mnyamata wofatsa ndi wamtendere.

Gogo Abrahamu anali akali moyo, ndipo tingayerekezere m’mene Yakobo anakondera kumumvetsera akunena za Yehova. Potsiriza Abrahamu anafa ali ndi zaka 175, mapasa’wo ali ndi zaka 15.

Esau ali ndi zaka 40 anakwatira akazi awiri a m’Kanani. Izi zinakwiyitsa kwambiri Isake ndi Rebeka, chifukwa akazi’wa sanalambire Yehova.

Tsiku lina kanthu kena kanachitika kamene kanapsyetsa mtima kwambiri Esau pa mbale wake Yakobo. Nthawi inafika yoti Isake apereke dalitso kwa mwana wake wamkulu. Pakuti Esau anali wamkulu koposa Yakobo, Esau anayembekezera kulandira dalitso’li. Koma Esau anali atagulitsa kuyenera kwa kulandira dalitso’li kwa Yakobo. Ndipo’nso, pa kubadwa kwa ana awiri’wa Mulungu anali atanena kuti Yakobo akalandira dalitso. Ndipo izi ndizo zinachitika. Isake anapereka dalitso’lo kwa mwana wake Yakobo.

Yakobo

Atamva izi Esau anakwiyira Yakobo. Anali wokwiya kwambiri kwakuti anati akapha Yakobo. Atamva izi Rebeka, anada nkhawa kwambiri. Nauza mwamuna wake Isake kuti: ‘Zidzakhala zoopsya’di ngati Yakobo naye’nso akwatira mmodzi wa akazi a Kanani’wa.

Motero anaitana Yakobo mwana wake namuuza kuti: ‘Usakwatire Mkazi wa m’Kanani. Koma upite ku mbumba ya gogo wako Betuele m’Harana. Ukakwatire mmodzi wa ana akazi a mwana wao wamwamuna Labani.’

Yakobo anamvetsera atate wake, pompo ananyamuka kumka kwa abale ake m’Harana.

Genesis 25:5-11, 20-34; 26:34, 35; 27:1-46; 28:1-5; Aheberi 12:16, 17.Mafunso

  • Kodi Esau ndi Yakobo anali ndani, ndipo kodi anali osiyana motani?
  • Kodi Esau ndi Yakobo anali ndi zaka zingati pamene agogo awo Abrahamu anamwalira?
  • Kodi Esau anachita chiyani chimene chinamvetsa chisoni kwambiri amayi ake ndi atate ake?
  • N’chifukwa chiyani Esau anakwiyira kwambiri mbale wake, Yakobo?
  • Kodi Isake anapereka malangizo otani kwa mwana wake Yakobo?

Mafunso ena