KODI mukudziwa mkazi’yu m’chithunzi’chi? Dzina lake ndi Rebeka. Mwamuna amene akum’chingamira ndiye Isake. Iye adzakhala mkazi wake. Kodi izi zinachitika motani?

Atate wa Isake Abrahamu anafuna kupezera mkazi wabwino mwana wake. Sanafune kuti Isake akwatire mmodzi wa akazi a m’Kanani, chifukwa anthu’wa analambira milungu yonyenga. Chotero iye anaitana mtumiki wake nati: ‘Ndikufuna ubwerere kwa abale anga m’Harana ndi kupezera mwana wanga Isake mkazi.

Pompo mtumiki’yo anatenga ngamila khumi nayenda ulendo wautali. Ali pafupi kwa abale a Abrahamu, anaima pa chitsime. Anali masana dzuwa litapendeka, nthawi imene akazi a m’mudzimo amadzatunga madzi. Chotero mtumiki’yo anapemphera kwa Yehova nati: ‘Mkazi amene andipatsa ine madzi ndi ngamila’zi akhaletu mkazi amene mwasankhira Isake.’

Rabeka akukumana ndi Isaki

Posapita nthawi Rebeka anadza kudzatunga madzi. Mtumiki’yo atapempha madzi, anam’patsa. Napita’nso kukatunga okwanira ngamila zonse za ludzu’zo. Inalitu ntchito yaikulu chifukwa ngamila zimamwa madzi ochuluka kwambiri.

Atatha kuchita izi, mtumiki wa Abrahamu anafunsa dzina la atate wake. Iye anapempha’nso ngati angakagonere kwao. Iye anati: ‘Atate wanga ndiwo Betuele, ndipo malo tiri nao oti mukakhale nafe.’ Mtumiki’yo anadziwa kuti Betuele anali mwana wa mbale wa Abrahamu Nahori. Chotero anagwada pansi nathokoza Yehova kaamba ka kum’tsogoza kwa abale a Abrahamu.

Usiku’wo mtumiki’yo anauza Betuele ndi mlongo wa Rebeka Labani chifukwa chake anadza. Onse anabvomera kuti Rebeka anagamke naye kukakwatiwa ndi Isake. Kodi Rebeka ananenanji atafunsidwa? Anati, ‘Inde.’ akapita. Chotero m’mawa mwake anakwera pa ngamila nayamba ulendo wautali wobwerera ku Kanani.

Pofika, unali usiku. Rebeka anaona mwamuna akuyenda m’munda. Anali Isake. Iye anakondwa kuona Rebeka. Mai wake wake Sara anali atafa zaka zitatu zapita’zo ndipo anali akali ndi chisoni. Koma tsopano Isake anakonda Rebeka kwambiri, ndipo anayamba’nso kukondwa.

Genesis 24:1-67.Mafunso

  • Kodi mwamuna ndi mkazi amene ali m’chithunzichi ndi ndani?
  • Kodi Abrahamu anachita chiyani kuti apezere mwana wake mkazi, ndipo n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?
  • Kodi pemphero la mtumiki wa Abrahamu linayankhidwa motani?
  • Kodi Rebeka anayankha chiyani atamufunsa ngati akufuna kukwatiwa ndi Isake?
  • Kodi n’chiyani chinachititsa Isake kuyambiranso kukondwa?

Mafunso ena