LOTI ndi banja lake anakhala ndi Abrahamu m’Kanani. Tsiku lina Abrahamu anati kwa Loti: ‘Palibe malo okwanira zifuyo zathu zonse. Tilekanetu. Ukamka uku, ine ndidzamka kwinako.’

Loti anayang’ana dziko’lo. Anaona chigawo chabwino kwambiri cha madzi ambiri ndi msipu wochuluka kaamba ka zifuyo zake. Ichi chinali Chigawo cha Yordano. Chotero Loti anasamutsira banja lake ndi zifuyo kumene’ko. Potsirizira pake anamanga nyumba yao mu mzinda wa Sodumu.

Anthu a Sodomu anali oipa kwambiri. Izi zinabvutitsa Loti chifukwa anali wabwino. Mulungu’nso anabvutika maganizo. Kenako, Mulungu anatumiza angelo awiri kukachenjeza Loti kuti akaononga Sodomu ndi Gomora chifukwa cha kuipa kwao.

Iwo anauza Loti kuti: ‘Fulumira! Tenga mkazi wako ndi ana ako akazi awiri nutuluke muno!’ Iwo anali ochedwa pang’ono, chotero angelo’wo anawagwira pa dzanja nawatulutsa mu mzinda’wo. M’modzi wa angelo’wo anati: ‘Thawitsani miyoyo yanu! Musacheuke. Thamangirani ku mapiri, kuti musaphedwe!’

Loti ndi ana ake anamvera nathawa m’Sodomu. Iwo sanaime, ndipo sanacheuke. Koma mkazi wa Loti sanamvere. Atayenda mtunda pang’ono kuchoka m’Sodomu, anaima nacheuka. Pompo anakhala chulu cha mchere. Kodi mukumuona m’chithunzi’mo?

Tikuphunziramo phunziro labwino. Zimasonyeza kuti Mulungu amapulumutsa awo amene amamvera, koma awo amene samamumvera adzataya miyoyo yao.

Genesis 13:5-13; 18:20-33; 19:1-29; Luka 17:28-32; 2 Petulo 2:6-8.

Loti akuthawa ku Sodomu


Mafunso

  • N’chifukwa chiyani Abrahamu ndi Loti analekana?
  • N’chifukwa chiyani Loti anasankha kukakhala ku Sodomu?
  • Kodi anthu a ku Sodomu anali otani?
  • Kodi angelo aŵiri anachenjeza Loti za chiyani?
  • N’chifukwa chiyani mkazi wa Loti anasanduka chulu cha mchere?
  • Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa zimene zinachitikira mkazi wa Loti?

Mafunso ena