Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 14: Mulungu Ayesa Abrahamu

Nkhani 14: Mulungu Ayesa Abrahamu

KODI mukuona zimene Abrahamu akuchita pano? Iye ali ndi mpeni, ndipo akuonekera ngati akufuna kupha mwana wake. Kodi n’chifukwa ninji akanachita izi? Tiyeni choyamba, tione m’mene iye ndi mkazi wake Sara anakhakira ndi mwana wao’yo.

Abulahamu akupereka nsembe Isaki

Mulungu anawalonjeza kuti adzakhala ndi mwana wamwamuna. Koma zinaonekera kukhala zosatheka, chifukwa iwo anali okalamba kwambiri. Abrahamu, anakhulupirirabe kuti Mulungu akatha kuchita zooneka kukhala ngati zosatheka. Chotero kodi n’chiani chinachitika?

Mulungu atalonjeza, chaka chinapitapo. Ndiyeno, Abrahamu ali ndi zaka 100, Sara ali ndi zaka 90, iwo anali ndi mwana wotchedwa Isake. Mulungu anasunga lonjezo lake!

Isake atasinkhuka, Yehova anayesa chikhulupiriro cha Abrahamu. Anaitana kuti: ‘Abrahamu!’ Nayankha kuti: ‘Ndiri pano!’ Mulungu nati: ‘Tenga mwana wako, mmodzi yekha’yo, Isake, nupite ku phiri limene ndidzakulozera. Ukaphe mwana’yo kum’pereka nsembe.’

Anamva’di chisoni ndi mau’wo, chifukwa anakonda kwambiri mwana wake. Pajatu, Mulungu analonjeza kuti ana a Abrahamu akakhala m’dziko la Kanani. Nanga zikanachitika bwanji ngati Isake anafa? Abrahamu sanamvetsetse, koma anamverabe Mulungu.

Atafika pa phiripo, Abahamu anamanga Isake namuika pa guwa la nsembe limene anamanga. Natengamo mpeni kuti amuphe. Komano pa nthawi’yo mngelo wa Mulungu anati: ‘Abrahamu, Abrahamu!’ Nayankha Abrahamu nati: ‘Ndiri pano!’

‘Usabvulaze mnyamata’yo kapena kum’chitira kanthu,’ adatero Mulungu. ‘Tsopano ndidziwa kuti umandikhulupirira, chifukwa sinandikaniza mwana wako, mmodzi yekha.’

Ha, ndi kukhulupirira Mulungu kotani nanga kumene Abrahamu anali nako! Iye anakhulupirira kuti palibe kanthu kanali kosatheka kwa Yehova, ndi kuti Yehova akatha kuukitsa Isake. Koma sichinali kweni-kweni chifuniro cha Mulungu kuti Abrahamu aphe Isake. Chotero Mulungu anachititsa nkhosa kukodwa pa ziyango-yango zapafupipo, nauza Abrahamu kuiphera nsembe m’malo mwa mwana wake.

Genesis 21:1-7; 22:1-18.Mafunso

  • Kodi Mulungu analonjeza Abrahamu chiyani, ndipo kodi Mulungu anasunga bwanji lonjezo lake?
  • Monga momwe chithunzichi chikusonyezera, kodi Mulungu anayesa bwanji chikhulupiriro cha Abrahamu?
  • Kodi Abrahamu anachita chiyani, ngakhale kuti sanamvetsetse cholinga cha zimene Mulungu anamulamula kuchita?
  • Kodi n’chiyani chinachitika pamene Abrahamu anatenga mpeni kuti aphe mwana wake?
  • Kodi chikhulupiriro cha Abrahamu mwa Mulungu chinali cholimba motani?
  • Kodi Mulungu anapereka chiyani kwa Abrahamu kuti aphere nsembe, ndipo anachita zimenezi motani?

Mafunso ena