Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 13: Abrahamu—Bwenzi la Mulungu

Nkhani 13: Abrahamu—Bwenzi la Mulungu

AMODZI a malo kumene kunamka anthu chitapita Chigumula anali Uri. Anakhala mzinda wofunika kwambiri wa nyumba zabwino kwambiri. Koma anthu’wo kumene’ko analambira milungu yonyenga. Anachita’nso motero m’Ba’bele. Anthu’wo mu Uri ndi Ba’bele sanali ngati Nowa ndi mwana wake Semu, amene anatumikirabe Yehova.

Zaka 350 pambuyo pa chigumula, Nowa anafa. Panangopita zaka ziwiri zokha pamene munthu mukumuona pa chithunzi’yu anabadwa. Iye anali wapadera kwambiri kwa Mulungu. Dzina lake linali Abrahamu. Iye ndi banja lake anakhala muno mu mzinda wa Uri.

Abulahamu akuyang’ana nyenyezi

Tsiku lina Yehova anati kwa Abrahamu: ‘Siya Uri ndi abale ako, nupite ku dziko limene ndidzakulozera.’ Kodi anamvera nasiya zokondweretsa zonse za Uri? Inde. Chinali chifukwa cha kumvera Mulungu nthawi zonse uku kuti iye anadziwika kukhala bwenzi la Mulungu.

Ena a m’banja la Abrahamu anatuluka naye mu Uri. Atate wake Tera anamka naye. Mphwake Loti anamka naye. Mkazi wake Sara, anamka naye. Kenako anafika pa malo ochedwa Harana, kumene Tera anafera. Iwo anali kutali kwambiri ndi Uri.

Patapita nthawi iye ndi banja lake anachoka ku Harana nafika ku Kanani. Uko Yehova anati: ‘Iri ndiro dziko limene ndidzapatsa ana ako.’ Abrahamu anakhala m’mahema m’Kananimo.

Mulungu anayamba kuthandiza Abrahamu kwakuti anakhala ndi nkhosa ndi zifuyo zina zochuluka ndi atumiki mazana. Koma iye ndi Sara analibe ana ao ao.

Abrahamu afafika 99, Yehova anati kwa iye: ‘Ndikukulonjeza kuti udzakhala atate wa mitundu yambiri ya anthu.’ Kodi izi zikanachitika motani, pakuti Abrahamu ndi Sara anali okalamba kosati n’kubala mwana?

Genesis 11:27-32; 12:1-7; 17:1-8, 15-17; 18:9-19.Mafunso

  • Kodi mu mzinda wa Uri munkakhala anthu otani?
  • Kodi munthu amene ali m’chithunziyu ndi ndani, anabadwa liti, ndipo ankakhala kuti?
  • Kodi Mulungu anauza Abrahamu kuchita chiyani?
  • N’chifukwa chiyani Abrahamu anatchedwa bwenzi la Mulungu?
  • Kodi ndani anapita nawo ndi Abrahamu pamene anachoka ku Uri?
  • Kodi Mulungu anauza Abrahamu chiyani atafika ku dziko la Kanani?
  • Kodi Mulungu analonjeza Abrahamu chiyani pamene anali ndi zaka 99?

Mafunso ena