Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 12: Anthu Amanga Chinsanja

Nkhani 12: Anthu Amanga Chinsanja

ZAKA zambiri zinapitapo. Ana a Nowa anali ndi ana Ochuluka. Ana ao anakula nakhala ndi ana ochuluka. Posapita nthawi panali anthu ochuluka pa dziko lapansi.

Mmodzi wa amene’wa anali chidzukulu cha Nowa chochedwa Nimrode. Iye anali woipa amene anasaka ndi kupha nyama ndi anthu omwe. Nimrode anadzipanga’nso kukhala mfumu kulamulira pa anthu ena. Mulungu sanakonde Nimrode.

Anthu onse pa nthawi’yo analankhula chinenero chimodzi. Nimrode anafuna kuwasonkhanitsa pamodzi kuti adziwalamulira. Chotero kodi mukudziwa chimene anachita? Anauza anthu’wo kumanga mzinda ndi chinsanja. Mukuwaona m’chithunzi’cho akuumba njerwa.

Yehova sanali wokondwa ndi kumanga’ku. Iye anafuna kuti anthu abalalike ndi kukhala pa dziko lonse lapansi. Koma anthu’wo anati: ‘Tiyeni! timange mzinda ndi nsanja yaitali kwambiri yoti nsonga yake idzafike kumwamba. Pompo tidzadzipangira dzina! Anthu’wo anadzifunira ulemu, osati Mulungu.

Chotero Mulungu analetsa anthu’wo kumanga nsanja. Kodi mukudziwa kuti anakuchita motani? Mwa kulankhulitsa anthu zinenero zosiyana mwadzidzidzi. Omanga’wo sanamvane’nso. Ndicho chifukwa chake mzinda’wo unachedwa Ba’bele. kapena Babulo, kutanthauza ”Chisokonezo.”

Anthu’wo tsopano anayamba kubalalika pa Ba’bele. Timagulu timene tinalankhula chinenero chimodzi tinamkera limodzi ku mbali ina ya dziko lapansi.

Genesis 10:1, 8-10; 11:1-9.

Anthu akumanga nsanja yaikulu


Mafunso

  • Kodi Nimrode anali ndani, ndipo kodi Mulungu ankamuona bwanji munthu ameneyu?
  • M’chithunzichi, n’chifukwa chiyani anthu anali kuumba njerwa?
  • N’chifukwa chiyani Yehova sanakondwere ndi ntchito yomangayo?
  • Kodi Mulungu analetsa bwanji ntchito yomanga chinsanjayo?
  • Kodi mzindawo unatchedwa chiyani, ndipo kodi dzina limenelo linatanthauza chiyani?
  • Kodi n’chiyani chinachitikira anthuwo Mulungu atasokoneza zinenero zawo?

Mafunso ena