Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Chigawo 2: Chigumula Mpaka pa Kulanditsidwa ku Igupto

Chigawo 2: Chigumula Mpaka pa Kulanditsidwa ku Igupto

Anthu asanu ndu atatu okha anapulumuka Chigumula, koma m’kupita kwa nthawi anaonjezeka kukhala zikwi zambiri. Ndiyeno, zaka 352 pambuyo pa Chigumula, anabadwa Abrahamu. Tikuphunizra m’mene Mulungu anasungira lonjezo lake mwa kupatsa Abrahamu mwana wochedwa Isake. Kenako, mwana mmodzi mwa ana awiri a Isake, Yakobo anasankhidwa ndi Mulungu.

Yakobo anali ndi banja lalikulu la ana amuna 12 ndi ana ena akazi. Ana a Yakobo 10 anada m’ngono wao Yosefe nam’gulitsa mu ukapolo m’Igupto. Pambuyo pake, Yosefe anakhala wolamulira wofunika wa Igupto. Pamene njala yoipa inadza, Yosefe anayesa abale ake kuti aone ngati anasintha mtima. Potsiriza, banja lonse la Yakobo, Aisrayeli, anasamukira ku Igupto. Izi zinachitika zaka 290 pambuyo pa kubadwa kwa Abrahamu.

Kwa zaka 215 Aisrayeli anakhala m’Igupto. Atafa Yosefe, iwo anakhala akapolo kumene’ko. M’kupita kwa nthawi, Mose anabadwa, Mulungu nam’gwiritsira ntchito kulanditsa Aisrali ku Igupto. Zonse pamodzi, zaka 857 za mbiri zikulowetsedwamo m’Mbali YACHIWIRI.

Yakobo ndi banja lake akusamukira ku Iguputo