Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 7: Munthu Wolimba Mtima

Nkhani 7: Munthu Wolimba Mtima
Inoki

PAMENE anthu anayamba kuchuluka pa dziko, ambiri anachita zoipa ngati Kaini. Koma mmodzi anali wosiyana. Ndiye munthu’yu Enoke. Enoke anali munthu wolimba mtima. Anthu onse om’zungungulira anali kuchita zoipa kwambiri, koma iye anatumikirabe Mulungu.

Kodi mukudziwa chifukwa chake anthu kale’lo anachita zinthu zoipa zambiri? Taganiziranitu, kodi anachititsa Adamu ndi Hava kusamvera Mulungu ndi kudya chipatso choletsedwa ndi Mulungu ndani? Inde, anali mngelo woipa. Baibulo limam’cha Satana. Iye akuyesa kuipitsa ali yense.

Wakuba akubera munthu kenako n’kumupha

Tsiku lina Yehova anauza Enoke kuuza anthu kanthu kena kamene sanafune kukamva. Ndiko: ‘Tsiku lina Mulungu adzaononga anthu onse oipa.’ Anthu’wo anaipidwa kumva izi. Iwo anayesa’di kum’pha. Chotero iye anafunikira kulimba mtima kwambiri kuti auze anthu’wo zodzachitidwa ndi Mulungu.

Mulungu sanalole kuti Enoke akhalitse pakati pa anthu oipa’wo. Iye anakhala ndi moyo zaka 365 zokha. Bwanji tikuti “zaka 365 zokha”? Chifukwa anthu m’nthawi’yo anali amphamvu kwambiri koposa tsopano ndipo anakhala ndi moyo kotalikirapo. Eya, mwana wa Enoke Metusela anakhala ndi moyo zaka 969!

Anthu akuchita zoipa

Atafa Enoke, anthu’wo anaipira-ipira. Baibulo limati ‘chiri chonse chimene analingalira chinali choipa nthawi zonse,’ n’kuti ‘dziko lapansi linadzala chiwawa.’

Kodi mukudziwa chifukwa chake panali bvuto lalikulu pa dziko m’masiku’wo? N’chifukwa chakuti Satana anali ndi njira yatsopano yochititsira anthu kuchita zoipa. Tidzaphunzira za izi kenako.

Genesis 5:21-24, 27; 6:5; Aheberi 11:5; Yuda 14, 15.Mafunso

 • Kodi Enoke anali wosiyana motani ndi anthu ena?
 • N’chifukwa chiyani anthu a m’nthaŵi ya Enoke anachita zoipa zambiri?
 • Kodi anthu ankachita zinthu zoipa zotani? (Onani chithunzi.)
 • N’chifukwa chiyani Enoke anafunika kulimba mtima?
 • Kodi m’masiku amenewo anthu ankakhala ndi moyo zaka zingati, koma kodi Enoke anakhala ndi moyo zaka zingati?
 • Kodi chinachitika n’chiyani Enoke atafa?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Genesis 5:21-2427.

  Kodi Enoke anali ndi ubwenzi wotani ndi Yehova? (Gen. 5:24)

  Malinga ndi Baibulo, kodi munthu amene anakhala ndi moyo zaka zambiri kuposa munthu wina aliyense ndi ndani, ndipo anafa ali ndi zaka zingati? (Gen. 5:27)

 • Ŵerengani Genesis 6:5.

  Kodi zinthu zinaipa motani padziko lapansi Enoke atafa, ndipo kodi zimenezi tingaziyerekezere bwanji ndi zimene zikuchitika masiku ano? (2 Tim. 3:13)

 • Ŵerengani Aheberi 11:5.

  Kodi ndi khalidwe liti la Enoke limene ‘linakondweretsa Mulungu,’ ndipo zotsatirapo zake zinali zotani? (Gen. 5:22)

 • Ŵerengani Yuda 14, 15.

  Kodi Akristu masiku ano angatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Enoke pochenjeza anthu za nkhondo ya Armagedo imene ikubwera? (2 Tim. 4:2; Aheb. 13:6)