Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 6: Mwana Wabwino, ndi Woipa

Nkhani 6: Mwana Wabwino, ndi Woipa

YANG’ANANI Kaini ndi Abele tsopano. Onse akula. Kaini wakhala mlimi. Iye amalima dzinthu ndi zipatso ndi ndiwo zamasamba.

Kaini ndi Abele akupereka nsembe kwa Mulungu

Abele wakhala woweta nkhosa. Iye amakonda kusamalira ana a nkhosa. Iwo amakula kukhala nkhosa zazikulu, ndipo chotero Abele posapita nthawi akukhala ndi gulu la nkhosa loliyang’anira.

Tsiku lina Kaini ndi Abele akudza ndi mphatso kwa Mulungu. Kaini akudza ndi zakudya zimene walima. Abele akudza ndi nkhosa yake yabwino kopambana. Yehova akukondwera ndi Abele ndi mphatso yake. Koma sakukondwera ndi Kaini ndi mphatso yake. Kodi mukudziwa chifukwa chake?

Si ubwino wokha wa mphatso ya Abele koposa ya Kaini. N’chifukwa cha ubwino wa Abele. Amakonda Yehova ndi mbale wake. Koma ngwoipa; samakonda mbale wake.

Mulungu akuuza Kaini kusintha. Koma Kaini sakumvetsera. Iye wakwiya kwambiri chifukwa chakuti Mulungu anakonda kwambiri Abele. Chotero Kaini akuti ‘Tiye tipite kumunda.’ Kumene’ko ali okha, Kaini akumenya Abele. Akum’menya zolimba mpaka kumupha. Kodi izi sizinali zoopsya?

Kaini akuthawa atapha m’bale wake

Ngakhale Abele anafa, Mulungu akum’kumbukirabe. Iye anali wabwino, ndipo Yehova samaiwala munthu wabwino wonga iye. Tsiku lina Yehova adzaukitsa Abele. Pa nthawi’yo sadzafa’nso. Adzakhala pa dziko pano kosatha. Kodi sikudzakhala kwabwino kudziwa anthu onga iyeyo?

Koma Mulungu samakondwera ndi anthu onga Kaini. Chotero Kaini atapha mbale wake, Mulungu anam’langa mwakum’thamangitsa kwa abale ake. Atachoka kukakhala kwina, anatenga mmodzi wa alongo ake, nam’kwatira.

Kenako Kaini ndi mkazi wake anabala ana. Ana ena amuna ndi akazi a Adamu anakwatirana, nawo’nso anabala ana. Posakhalitsa panali anthu ambiri pa dziko. Tiyeni tiphunzire za ena a iwo.

Genesis 4:2-26; 1 Yohane 3:11, 12; Yohane 11:25.Mafunso

 • Kodi Kaini ndi Abele ayamba kugwira ntchito zotani?
 • Kodi Kaini ndi Abele abweretsa mphatso zotani kwa Yehova?
 • N’chifukwa chiyani Yehova akukondwera ndi mphatso ya Abele, ndipo n’chifukwa chiyani sakukondwera ndi mphatso ya Kaini?
 • Kodi Kaini ndi munthu wotani, ndipo Yehova akuyesera bwanji kumuthandiza kuti asinthe?
 • Kodi Kaini akuchita chiyani ali aŵiriŵiri ndi mbale wake kumunda?
 • Fotokozani zimene zinachitika kwa Kaini atapha mbale wake.

Mafunso ena

 • Ŵerengani Genesis 4:2-26.

  Kodi Yehova anafotokoza motani ngozi imene Kaini analimo? (Gen. 4:7)

  Kodi Kaini anasonyeza bwanji mtima umene anali nawo? (Gen. 4:9)

  Kodi Yehova amaona bwanji kukhetsa mwazi wa munthu wosalakwa? (Gen. 4:10; Yes. 26:21)

 • Ŵerengani 1 Yohane 3:11, 12.

  N’chifukwa chiyani Kaini anakwiya kwambiri, ndipo kodi zimenezi ndi chenjezo kwa ife masiku ano motani? (Gen. 4:4, 5; Miy. 14:30; 28:22)

  Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti ngakhale makolo ndi achibale athu onse atakhala otsutsa Yehova, tingakhalebe okhulupirika kwa iye? (Sal. 27:10; Mat. 10:21, 22)

 • Ŵerengani Yohane 11:25.

  Kodi Yehova amatilimbikitsa bwanji za anthu onse amene amafa chifukwa chochita chilungamo? (Yoh. 5:24)

Onaninso

ZITHUNZI

Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Kaini ndi Abele?

Sindikizani chithunzichi, werengani mavesi a m’Baibulo, kenako lembani mawu amene akusoweka m’mizere yopanda kanthuyo.

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

Abele​—“Ngakhale Kuti Anafa, Iye Akulankhulabe”

Kodi tingaphunzirepo chiyani pa nkhani ya Abele, ngakhale kuti Baibulo silifotokoza zambiri zokhudza iyeyo komanso chikhulupiriro chake?