Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 5: Moyo Wobvuta Uyamba

Nkhani 5: Moyo Wobvuta Uyamba

KUNJA kwa munda wa Edene, Adamu ndi Hava anali ndi mabvuto ambiri. Anayenera kugwira ntchito zolimba kuti apeze chakudya. M’malo mwa mitengo ya zipatso yokongola, anaona minga ndi mitula zikumera ponse-ponse. N’zimene zinachitika pamene Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu ndipo sanakhale’nso mabwenzi Ake.

Adamu akugwira ntchito mwakhama ndi mwana wake

Koma choipa kwambiri, iwo anayamba kufa. Pajatu, Mulungu anawachenjeza kuti akafa ngati akadya zipatso za mtengo wina. Tsiku lomwe anadya anayamba kufa. Kunali kopusa chotani kwa iwo kuti sanamvere Mulungu!

Ana ao onse anabadwa Mulungu atawathamangitsa m’munda wa Edene. Zikutanthauza kuti ana’wo nawo’nso akalamba ndi kufa.

Adamu ndi Hava akanamvera Yehova, moyo ukanakhala wachimwemwe kwa iwo ndi ana ao. Iwo akanakhala ndi moyo kosatha m’chimwemwe pa dziko lapansi. Palibe akanakalamba, kudwala ndi kufa.

Mulungu amafuna kuti anthu akhale ndi moyo kosatha m’chimwemwe, ndipo akulonjeza kuti tsiku lina adzatero. Dziko lonse silidzangokongola kokha, koma anthu onse adzakhala athanzi. Ali yense pa dziko adzakhala bwenzi labwino kwa ali yense ndi Mulungu.

Hava ndi ana ake

Koma Hava sanali’nso bwenzi la Mulungu. Tsono pobala ana ake, sikunali kosam’bvuta. Anamva ululu. Kusamvera Yehova kunam’dzitsera’di chisono chochuluka, kodi si choncho?

Adamu ndi Hava anali ndi ana amuna ndi akazi ambiri. Atabadwa mwana wao wamwamuna woyamba, anam’cha Kaini. Wachiwiri anam’cha Abele. Kodi n’chiani chimene chinawachitikira? Kodi mukudziwa?

Genesis 3:16-23; 4:1, 2; Chivumbulutso 21:3, 4.Mafunso

 • Kodi moyo wa Adamu ndi Hava unali wotani kunja kwa munda wa Edene?
 • N’chiyani chinayamba kuchitikira Adamu ndi Hava, ndipo n’chifukwa chiyani?
 • N’chifukwa chiyani ana a Adamu ndi Hava anali oti adzakalamba ndi kufa?
 • Ngati Adamu ndi Hava akanamvera Yehova, kodi iwowo ndi ana awo akanakhala ndi moyo wotani?
 • Kodi kusamvera kunamubweretsera bwanji ululu Hava?
 • Kodi maina a ana aamuna aŵiri oyambirira a Adamu ndi Hava anali ndani?
 • Kodi ana enawo m’chithunzichi ndi ndani?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Genesis 3:16-23 ndi 4:1, 2.

  Kodi moyo wa Adamu unakhudzidwa bwanji ndi kutembereredwa kwa nthaka? (Gen. 3:17-19; Aroma 8:2022)

  Kodi dzina loti Hava, lotanthauza kuti “Wamoyo,” linali loyenerera chifukwa chiyani? (Gen. 3:20)

  Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anali kuganizira Adamu ndi Hava ngakhale atachimwa? (Gen. 3:721)

 • Ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4.

  Kodi ndi zinthu ‘zoyamba’ ziti zimene mukufunitsitsa kudzaona zitachotsedwa?