Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 4: Chifukwa Chake Anataya Malo Ao

Nkhani 4: Chifukwa Chake Anataya Malo Ao

ONANI zimene zikuchitika tsono. Adamu ndi Hava akuthamangitsidwa mu Edene’mo. Kodi mukudziwa chifukwa chake?

Adamu ndi Hava akuchotsedwa m’munda wa Edeni

Chifukwa anachita kanthu koipa kwambiri. Chotero Yehova akuwalanga. Kodi mukudziwa choipa chimene Adamu ndi Hava anachita?

Iwo anachita chimene Mulungu anawaletsa kuchita. Iye anawauza kuti angadye zipatso za m’mitengo ya m’mundamo. Koma Mulungu anati asadye za mtengo umodzi, akazidya adzafa. Uwo unali wake. Tikudziwa kuti n’kolakwa kutenga kanthu ka munthu wina, eti? Nangano, chinachitika n’chiani?

Tsiku lina Hava ali yekha m’mundamo, njoka inalankhula naye. Taganizirani! Inauza Hava kudya chipatso cha mu mtengo woletsedwa ndi Mulungu. Pamene Yehova anapanga njoka sanazipanga kuti zidzilankhula. Chotero zikungotanthauza kuti wina wake anali kulankhulitsa njoka’yo. Kodi iye anali yani?

Sanali Adamu. Chotero anayenera kukhala mmodzi wa anthu amene Yehova anawapanga dziko lisanalengedwe. Anthu amene’wo ndiwo angelo, ife sitingawaone. Mngelo mmodzi’yu anakhala wonyada kwambiri. Anayamba kuganizira kukhala wolamulira wonga Mulungu. Anafuna kumveredwa ndi anthu koposa kumvera Yehova. Iye anali mngelo amene analankhulitsa njoka.

Mngelo’yu anakhoza kupusitsa Hava. Atauzidwa kuti akakhala ngati Mulungu ngati adya chipatso’cho, anakhulupirira. Chotero anadya, nadya’nso Adamu. Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, ndicho chifukwa chake anataya munda wao wokhalamo wokongola’wo.

Koma tsiku lina Mulungu adzachititsa dziko lonse kukhala lokongola ngati munda wa Edene. Kenako tidzaphunzira m’mene mungathandizire kulipanga kukhala lotere. Tsono, tiyeni tione chimene chinawachitikira.

Genesis 2:16, 17; 3:1-13, 24; Chivumbulutso 12:9.Mafunso

  • M’chithunzichi, kodi n’chiyani chikuchitikira Adamu ndi Hava?
  • N’chifukwa chiyani Yehova anawalanga?
  • Kodi njoka inamuuza chiyani Hava?
  • Kodi ndani anachititsa njokayo kulankhula ndi Hava?
  • N’chifukwa chiyani Adamu ndi Hava anataya malo awo okhala a Paradaiso?

Mafunso ena