Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 3: Mwamuna ndi Mkazi Oyamba

Nkhani 3: Mwamuna ndi Mkazi Oyamba

KODI chosiyana n’chiani m’chithunzi’chi? Ndicho anthu’wo. Ndiwo mwamuna ndi mkazo oyamba. Kodi anawapanga ndani? Ndiye Mulungu. Kodi mukudziwa dzina Lake? Ndiro Yehova. Ndipo iwo anachedwa Adamu ndi Hava.

Adamu ndi Hava ali m’munda wa Edeni

Yehova anapanga Adamu motere. Anatenga dothi lapansi naumba nalo thupi langwiro, la munthu wamwamuna. Anauzira mpweya m’mphuno mwake, Adamu nakhala wamoyo.

Yehova anali ndi ntchito yoti Adamu achite. Anauza Adamu kucha maina zinyama zonse. Adamu angakhale atapenda zinyama’zo kwa nthawi yaitali kuti azisankhire maina abwino kwambiri. Pocha maina zinyama’zo iye anayamba kuona kanthu kena. Kotani?

Zinyama zonse zinali ziwiriziwiri. Panali njobvu zamphongo ndi zazikazi, mikango yamphongo ndi yaikazi. Koma Adamu analibe mnzake. Chotero Yehova anam’goneka tulo tatikulu, nachotsa nthiti yake imodzi. Nthiti’yo Yehova anaipanga mkazi wa Adamu.

Ha, ndi wokondwa chotani m’mene analiri Adamu tsopano! Ganizani m’mene Hava anakondwera kuikidwa m’munda wokongola’wo! Tsopano akanatha kubala ana ndi kukhala pamodzi mwachimwemwe.

Yehova anafuna kuti iwo akhale ndi moyo kosatha. Anafuna kuti iwo akongoletse dziko lonse ngati munda wa Edene’wo. Ha, ndi okondwera nawo chotani nanga m’mene analiri Adamu ndi Hava! Kodi mukanakonda kukongoletsa nawo dziko lapansi? Koma chimwemwe chao sichinakhalitse. Tiyeni tione chifukwa chake.

Salimo 83:18; Genesis 1:26-31; 2:7-25.Mafunso

 • Kodi chithunzi chimene chili mu Nkhani 3 chikusiyana bwanji ndi chimene chili mu Nkhani 2?
 • Kodi ndani anapanga mwamuna woyamba, ndipo kodi dzina la mwamunayo linali ndani?
 • Kodi Mulungu anapatsa Adamu ntchito yotani?
 • N’chifukwa chiyani Mulungu anagonetsa Adamu tulo tatikulu?
 • Kodi Adamu ndi Hava akanakhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali bwanji, ndipo kodi Yehova anafuna kuti agwire ntchito yotani?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Salimo 83:18.

  Kodi Mulungu dzina lake ndani, ndipo ali ndi ulamuliro wapadera wotani padziko lapansi? (Yer. 16:21; Dan. 4:17)

 • Ŵerengani Genesis 1:26-31.

  Kodi Mulungu analenga chiyani pa tsiku lachisanu ndi chimodzi atafika pachimake pa ntchito yake yolenga, ndipo kodi cholengedwa chimenechi chinali chosiyana bwanji ndi zinyama? (Gen. 1:26)

  Kodi Yehova anapereka chiyani kwa anthu ndi zinyama zomwe? (Gen. 1:30)

 • Ŵerengani Genesis 2:7-25.

  Kodi Adamu anafunikira kuchita chiyani kuti akwanitse ntchito imene anapatsidwa yotcha maina zinyama? (Gen. 2:19)

  Kodi lemba la Genesis 2:24 limatithandiza bwanji kuona mmene Yehova amaonera ukwati, kupatukana, ndi kusudzulana? (Mat. 19:4-69)