Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 2: Munda Wokongola

Nkhani 2: Munda Wokongola

ONANI pa dziko’pa! N’chokongola chotani nanga m’mene chiri chonse chiriri! Onani udzu ndi mitengo, maluwa n’zinyama zonse. Kodi njobvu ndi mikango ziripo?

Nyama zili m’munda wa Edeni

Kodi munda wokongola’wu unakhalapo motani? Tiyeni tione.

Mulungu, anayamba wapanga nsipu wokuta dziko. Napanga’nso mitundu yonse ya tomera. Zomera’zi zimakongoletsa dziko. Zimatipatsa’nso zakudya zokoma.

Anapanga’nso nsomba zisambire m’madzi ndi mbalame ziuluke m’mwamba. Anapanga agalu, amphaka ndi akavalo, zinyama zazikulu n’zazing’ono. Kodi n’ziti zimene ziri pafupi ndi nyumba yanu? Kodi sitimakondwera kuti Mulungu anatipangira zonse’zi?

Potsiriza, anapanga mbali ina ikhale malo apadera kwambiri. Anawacha munda wa Edene. Anali abwino’di kotheratu. Chiri chonse chowazungulira chinali chokongola. Mulungu anafuna kuti dziko lonse likhale ngati munda wakongola’wu.

Koma onani’nso chithunzi cha munda’wu. Kodi mukudziwa chimene Mulungu anaona kukhala chikusowamo? Tiyeni tione.

Genesis 1:11-25; 2:8, 9.Mafunso

 • Kodi Mulungu anakonza bwanji dziko lapansi kuti likhale malo athu okhalamo?
 • Tchulani mitundu yosiyanasiyana ya zinyama zimene Mulungu anapanga. (Onani chithunzi.)
 • N’chifukwa chiyani munda wa Edene unali wapadera?
 • Kodi Mulungu anafuna kuti dziko lonse lapansi likhale chiyani?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Genesis 1:11-25.

  Kodi Mulungu analenga chiyani pa tsiku lachitatu lolenga zinthu? (Gen. 1:12)

  Kodi n’chiyani chinachitika pa tsiku lachinayi lolenga zinthu? (Gen. 1:16)

  Kodi Mulungu anapanga zinyama zamitundu yotani pa tsiku lachisanu ndi lachisanu ndi chimodzi? (Gen. 1:20, 2125

 • Ŵerengani Genesis 2:8, 9.

  Kodi Mulungu anaika mitengo iŵiri yapadera yotani m’mundamo, ndipo kodi inaimira chiyani?