Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 10: Chigumula Chachikulu

Nkhani 10: Chigumula Chachikulu

KUNJA kwa chingalawa, anthu anachitabe zochita zao monga kale. Iwo sanakhulupirirebe kuti Chigumula chikadza. Iwo angakhale ataseka koposa kale. Koma posapita nthawi analeka kuseka.

Anthu omwe ali ndi mantha ndiponso zinyama ali m’madzi achigumula

Mwadzidzidzi mvula inayamba kubvumba. Inakhuthuka kumwamba monga m’mene mumakhuthulira madzi m’ndowa. Nowa anali atanena zoona! Koma kunali kochedwa tsopano kwa ali yense kulowa m’chingalawa. Khomo linali litatsekedwa zolimba ndi Yehova.

Posapita nthawi madambo onse anamizidwa, Madzi anakhala ngati mitsinje yaikulu. Anakhwekhweretsa mitengo nagubuduza zimiyala, ndi kupanga phokoso lalikulu. Anthu anaopa. Anakwera m’zitunda. O, analaka-lakatu ngati akanamvetsera Nowa ndi kulowa m’chingalawa pamene khomo linali lowatsegukira! Koma tsopano kunali kochedwa.

Madzi anali kumakwera-kwera. Kwa mausana 40 ndi mausiku 40 madzi anakhuthuka kumwamba. Anakwera m’mbali mwa mapiri, ndipo posakhalitsa mapiri atali koposa anamizidwa. Chotero monga momwe ananenera Mulungu, anthu ndi zinyama zomwe kunja kwa chingalawa anafa. Koma ali yense m’kati anali bwino lomwe.

Nowa ndi ana ake anachita ntchito yabwino kukhoma chingalawa. Madzi anachinyamula, ndipo chinayandama pamwamba pa madzi. Tsiku lina, italeka mvula’yo, dzuwa linayamba kuwala. Ha, ndi kaonekedwe kokongola chotani! Panali chinyanja chimodzi konse-konse. Chokha chimene chikanatha kuonedwa chinali chingalawa choyandama’cho.

Chingalawa chikuyandama pamadzi

Zimphona zija zinali zitapita tsopano. Sizinapezeke’nso kuti zibvulaze anthu. Zonse zinali zitafa, limodzi ndi amai ao ndi anthu ena onse oipa. Koma kodi n’chiani chinachitikira atate ao?

Atate a zimphona’zo sanali anthu kweni-kweni ngati ife. Iwo anali angelo amene anadza kudzakhala ngati anthu pa dziko. Tsono chitadza Chigumula, sanafere kumodzi ndi anthu ena onse. Iwo sanagwiritsire’nso ntchito mafupi aumunthu amene anapanga’wo, nabwerera kumwamba monga angelo. Koma sanaloledwe’nso kukhala mbali ya banja la angelo a Mulungu. Chotero anakhala angelo a Satana. M’Baibulo akuchedwa ziwanda.

Tsopano Mulungu anachititsa mphepo kuomba, ndipo madzi’wo anayamba kuphwa. Pambuyo pa miyezi isanu chingalawa’cho chinatera pa phiri. Masiku ena ambiri anapitapo, okhala m’katimo ankatha kuyang’ana panja ndi kuona nsonga za mapiri. Madziwo anali kutsika-tsika.

Kenako Nowa anatulutsa khungubwi m’chingalawa. Ankauluka kwa kanthawi kumka cha uko n’kubwerera’nso, chifukwa cha kusapeza malo abwino oterapo. Anatero nthawi zonse ndipo pobwerera pali ponse, ankakhala pa chingalawa.

Nkhunda

Nowa anafuna kudziwa ngati madzi anali ataphwa pa dziko, chotero kenako anatulutsa nkhunda. Koma nkhunda’yo inabwerera’nso chifukwa sinapeze malo okhala. Nowa anaitumiza kachiwiri, ndipo inadza ndi tsamba la mtengo wa azitona kukamwa. Chotero Nowa anadziwa kuti madzi anali ataphwa. Nowa anatumiza nkhunda kachitatu, potsiriza inapeza malo ouma okhala.

Mulungu tsopano analankhula ndi Nowa. Anati: ‘Tuluka m’chingalawa. Tuluka nalo banja lako lonse ndi zinyama.’ Iwo anali atakhala m’chingalawa’cho koposa chaka chimodzi. Chotero tingayerekezere m’mene analiri achimwemwe kutuluka ndi kukhala ali moyo!

Genesis 7:10-24; 8:1-17; 1 Petulo 3:19, 20.Mafunso

 • N’chifukwa chiyani sizikanatheka kuti munthu wina aliyense aloŵe m’chingalawa pamene mvula inayamba kugwa?
 • Kodi Yehova anachititsa mvula kugwa kwa mausana ndi mausiku angati, ndipo madziwo anakwera mpaka kufika pati?
 • Kodi n’chiyani chinachitikira chingalawa pamene madzi anayamba kumiza dziko lapansi?
 • Kodi zimphona zinapulumuka pa Chigumula, nanga n’chiyani chinachitikira atate awo a zimphonazo?
 • Kodi n’chiyani chinachitikira chingalawa patatha miyezi isanu?
 • N’chifukwa chiyani Nowa anatulutsa khungubwi m’chingalawamo?
 • Kodi Nowa anadziŵa bwanji kuti madzi aphwa padziko?
 • Kodi Mulungu ananena chiyani kwa Nowa, iye ndi banja lake atakhala m’chingalawa kwa nthaŵi yopitirira chaka chimodzi?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Genesis 7:10-24.

  Kodi kuwonongedwa kwa zinthu zamoyo padziko lapansi kunali kwakukulu bwanji? (Gen. 7:23)

  Kodi zinatenga nthaŵi yaitali bwanji kuti madzi a Chigumula aphwere? (Gen. 7:24)

 • Ŵerengani Genesis 8:1-17.

  Kodi lemba la Genesis 8:17 limasonyeza bwanji kuti cholinga cha Yehova choyambirira cha dziko lapansi sichinasinthe? (Gen. 1:22)

 • Ŵerengani 1 Petulo 3:19, 20.

  Kodi angelo opanduka atabwerera kumwamba anaweruzidwa motani? (Yuda 6)

  Kodi nkhani ya Nowa ndi banja lake imalimbitsa bwanji chikhulupiriro chathu choti Yehova angathe kupulumutsa anthu ake? (2 Pet. 2:9)

Onaninso

ZITHUNZI

Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Nowa?

Koperani kapena sindikizani chithunzichi ndipo onani mmene mungatsanzirire chitsanzo cha Nowa pa nkhani yomvera.

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

Nowa “Anayenda Ndi Mulungu Woona”

Kodi Nowa ndi mkazi wake anakumana ndi mavuto otani polera ana awo? Kodi anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro pomanga chingalawa?