Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chigawo 1: Chilengedwe Mpaka pa Chigumula

Chigawo 1: Chilengedwe Mpaka pa Chigumula

Kodi kumwamba ndi dziko lapansi zinachokera kuti? Kodi dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, ndipo’nso zinthu zochuluka za dziko lapansi’zo, zinakhalapo motani? Baibulo limapereka yankho loona pamene limati zinalengedwa ndi Mulungu. Chotero bukhu lathu lino likuyamba ndi nkhani za Baibulo za chilengedwe.

Timamva kuti, zolengedwa zoyamba za Mulungu, zinali anthu auzimu ofananirapo naye. Iwo anali angelo. Koma dziko lapansi linalengedwera anthu onga ife. Chotero Mulungu anaumba mwamuna ndi mkazi ochedwa Adamu ndi Hava nawaika m’munda wokongola. Koma iwo sanamvere Mulungu ndipo anataya kuyenera kwa kukhalabe ndi moyo.

Zonse pamodzi, kuyambira pa kulengedwa kwa Adamu mpaka pa Chigumula chachikulu, panali zaka 1656. M’nthawi’yi panali anthu ambiri oipa. Kumwamba, kunali anthu osaoneka auzimu, Satana ndi angelo ake oipa. Pa dziko lapansi panali Kaini ndi anthu ena ambiri oipa, kuphatikizapo ena amphamvu zodabwitsa. Koma panali’nso anthu abwino pa dziko lapansi—Abele, Enoke ndi Nowa. M’Chigawo CHOYAMBA tidzawerenga za anthu onse’wa ndi zochitika

Nyama zili m’munda wa Edene