Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala

 MUTU 4

Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama

Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama

“Zolinga zimakhazikika anthu akakambirana.”—Miyambo 20:18

Tonsefe timafuna ndalama zogulira zinthu zofunika m’banja lathu. (Miyambo 30:8) Paja “ndalama zimatetezera.” (Mlaliki 7:12) Mabanja ambiri amavutika kuti akambirane nkhani za ndalama. Koma musalole kuti ndalama zisokoneze banja lanu. (Aefeso 4:32) Mwamuna ndi mkazi ayenera kukhulupirirana ndiponso kukambirana mmene angagwiritsire ntchito ndalama zawo.

 1 MUZIKHALA NDI BAJETI

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?” (Luka 14:28) N’zofunika kwambiri kuti muzigwirizana mmene mudzagwiritsira ntchito ndalama zanu. (Amosi 3:3) Muyenera kusankha zinthu zofunika kugula komanso kuchuluka kwa ndalama zimene mungawononge. (Miyambo 31:16) Komanso ngati muli ndi ndalama zokwanira kuti mugule chinachake sikuti muyenera kuchigula basi. Yesetsani kupewa ngongole. Muzingogwiritsa ntchito ndalama zimene muli nazo.—Miyambo 21:5; 22:7.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Mukatsala ndi ndalama pa mapeto pa mwezi, muzikambirana zimene mungachite nazo

  • Ngati ndalama zanu zimakhala zoperewera, kambiranani zimene mungachite kuti musamawononge zambiri. Mwachitsanzo, m’malo mophika chakudya chambiri n’kutaya chotsala, muzingophika chokwanira bwinobwino banja lanulo

 2 MUZIKAMBIRANA MOMASUKA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Timasamalira zinthu zonse moona mtima, osati pamaso pa Yehova pokha ayi, komanso pamaso pa anthu.” (2 Akorinto 8:21) Muziuza mwamuna kapena mkazi wanu ndalama zonse zimene mumalandira komanso mmene mumazigwiritsira ntchito.

Muzikambirana kaye musanagwiritse ntchito ndalama zambiri. (Miyambo 13:10) Kukambirana bwinobwino nkhani za ndalama kungathandize kuti muzikhala mwamtendere. Muzionanso kuti ndalama zimene mumapeza ndi za banja lonse osati zanokha.—1 Timoteyo 5:8.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzikambirana n’kuona kuchuluka kwa ndalama zimene aliyense angagwiritse ntchito popanda kuuza mnzake

  • Musamadikire kuti pakhale vuto kaye kuti mukambirane za ndalama

Onaninso

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi Baibulo Lingathandize pa Nkhani ya Mavuto Azachuma Ndiponso Ngongole?

Ndalama sizingakuthandizeni kukhala wosangalala koma pali mfundo za m’Baibulo zinayi zimene zingakuthandizeni pa mavuto azachuma.

GALAMUKANI!

Kodi Mungatani Kuti Musamawononge Ndalama Zambiri?

Musadikire mpaka ndalama zanu kutha musanayambe kuganizira njira yoyenera yogwiritsira ntchito ndalama. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti muzigwiritsa ntchito ndalama mosamala.

NSANJA YA OLONDA

Kodi Ndibwerekedi Ndalama?

Mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita.