Pa June 28, 2013, pa webusaiti ya jw.org panali chilengezo chakuti tsopano LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower ikupezeka m’zinenero 100. Laibulale imeneyi imagwira ntchito mofanana ndi Watchtower Library. Anthu angathe kugwiritsa ntchito laibulale ya pa intanetiyi pa zipangizo zosiyanasiyana monga kompyuta yaikulu, kompyuta ya laputopu, kompyuta ya m’manja (kapena kuti tabuleti) ndi mafoni ena amakono. Zofalitsa zambiri zoyendera madeti zimene zili pa laibulaleyi zikuyambira chaka cha 2000. M’zinenero zambiri, palaibulaleyi pakupezekanso Baibulo la Dziko Latsopano ndi buku la Insight on the Scriptures. Mulaibulaleyi munthu angathe kufufuza pongolemba liwu limodzi kapena mawu angapo nthawi imodzi, ngati mmene timachitira mu  Watchtower Library. Pogwiritsa ntchito laibulale imeneyi, mungathe kutsegula malemba kapena nkhani inayake n’chinenero chimodzi, kenako mungatabwanye batani limene lingakutsegulireni nkhani yomweyo m’chinenero chinanso. M’munsimu muli mawu oyamikira laibulale imeneyi, omwe anthu atitumizira:

“Zikomo kwambiri chifukwa chokhazikitsa laibulale ya pa Intaneti. Nditaona laibulaleyi kwa nthawi yoyamba, ndinasangalala kwambiri. Sindidziwa chilichonse chokhudza mmene amapangira mapulogalamu a pa kompyuta kapena mawebusaiti, koma ndinganene kuti laibulale imeneyi munaipanga mwaluso zedi. N’zoonekeratu kuti mumakonda anthu ena, mumakonda abale anu komanso mumakonda Yehova. Umboni wa zimenezi tikuupeza tikaona mmene munapangira laibulale imeneyi. Kunena zoona imeneyi ndi mphatso yamtengo wapatali imene ikusonyeza kuti Atate wathu wakumwamba, Yehova, ndi wachikondi komanso woolowa manja. Zikomo kwambiri.”—A., Argentina.

“Sindikumvetsa. Madzulo omwe ano ndinatsegula laibulale ya pa intaneti ndipo ndaona kuti aikapo chinenero cha Chikiliyo cha ku Haiti. Sindinkaganiza kuti zimenezi zingachitike. Mungathe kuona nokha m’kalata ino kuti ndikusowa chonena. Yehova akudalitseni chifukwa cha ntchito imene mukugwira, ndipo mzimu wake woyera upitirize kukutsogolerani.”—D.C., United States.