Mu October 2012, a Mboni za Yehova anatsegulira malo oonetsera zinthu zakale kulikulu lawo ku Brooklyn. Pamalowa pali zinthu zosonyeza mavuto osiyanasiyana amene Akhristu anakumana nawo komanso zimene anachita polimbana ndi mavutowo. Zinthuzi zimathandiza munthu kudziwa yekha mbiri ya Mboni za Yehova popanda kumufotokozera.

Mlungu woyamba wokha, alendo oposa 4,200, kuphatikizapo abale ndi alongo a ku Beteli anabwera kudzaona. Mlongo wina dzina lake Naomi, amene amakhala pafupi ndi malowa, anapita kukaona zinthuzi atangotsegulira kumene chionetserochi. Iye anati: “Mmene anasonyezera nthawi ya zochitika zosiyanasiyana, zinandithandiza kuti ndimvetse pamene zinthu zinazake zinachitika komanso chifukwa chake zinachitika choncho. Ndinaphunzira zambiri zokhuza gulu lathu komanso mbiri yake yamakono.”

 Kumbali yoyamba ya chionetserochi kuli zinthu zosonyeza mbiri yathu kuyambira Chikhristu chitangoyamba kumene mu 33 C.E., mpaka kudzafika m’nthawi yathu ino. Zinthuzo anazigawa m’zigawo 4 ndipo chigawo chilichonse chili ndi mutu wa m’Malemba. Munthu akafika m’chigawocho amayamba n’kuonerera kavidiyo ka m’Chingelezi kosonyeza zimene zili m’chigawocho. Ndipo angasankhe kuti aziona mawu a m’kavidiyoka m’zinenero zinanso 7.

Chigawo choyamba chili ndi mutu wakuti, “Anthu Akonda Mdima,” ndipo ukuchokera pa mawu a Yesu a pa Yohane 3:19. Baibulo linaneneratu kuti atumwi onse akadzamwalira, anthu oipa “adzayamba kulankhula zinthu zopotoka.” (Mac. 20:30) Anthu amene ankayesa kutsutsana nawo ankalangidwa koopsa.

Koma chigawo chachiwiri chili ndi mutu wakuti “Kuwala Kuunike,” wochokera pa 2 Akorinto 4:6. M’chigawo chimenechi muli zimene zinachitika kuyambira chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800 pamene ophunzira Baibulo anayamba kuphunzira Malemba  mwakhama. Ophunzirawa anasiya kutsatira zikhulupiriro zakale zomwe sizipezeka m’Baibulo ndipo molimba mtima anayamba kulalikira mfundo za choonadi. Chigawo chimenechi chikufotokozanso mmene kaguluko kanakulira komanso kuchuluka kwa mfundo za choonadi zimene anaphunzira nkhondo yoyamba ya padziko lonse isanayambe.

Kenako amasonyeza chinthu chimene chimachititsabe chidwi Mboni za Yehova mpaka lero. Mu 1914, Ophunzira Baibulo (dzina limene a Mboni za Yehova ankadziwika nalo pa nthawiyo) anayamba kuonetsa “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.” Anthu mamiliyoni ambiri anaonera seweroli, lomwe linali ndi zithunzi zosayenda komanso zinthunzi zina zoyenda zokhalanso ndi mawu. M’chigawochi mulinso zithunzi zenizeni zingapo zimene anagwiritsa ntchito popanga seweroli. Kuwonjezera pamenepa, muli kavidiyo kamene kanatengedwa m’gawo loyambirira la sewerolo komanso zithunzi zakalala zoposa 500.

 Chigawo chachitatu cha malo achionetserowa chili ndi mutu wakuti “Chinjokacho Chinakwiya,” wochokera pa Chivumbulutso 12:17, ndipo chikusonyeza mmene Satana wazunzira otsatira a Khristu. Chigawochi chikusonyeza kuti Akhristu anakhalabe olimba pokana kulowa usilikali. Mulinso kavidiyo kosonyeza zimene aboma ankachita pofuna kukakamiza atumiki a Yehova kuti achite zinthu zosemphana ndi chikumbumtima chawo. Mwachitsanzo, muli nkhani ya m’bale Remigio Cuminetti wa ku Italy, amene anakana kuvala yunifolomu ya asilikali komanso kumenya nawo nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Kavidiyo kena kakufotokoza za m’bale Alois Moser wa ku Austria. M’baleyu anakana kunena mawu akuti “Hitler Mpulumutsi Wathu!” Chifukwa cha zimenezi, iye anachotsedwa ntchito ndipo kenako anam’tumiza kundende yozunzirako anthu ya Dachau. M’chigawochi mulinso malo ena a mdima oyerekezera ndende. M’malo amenewa muli zithunzi za anthu a Mboni za Yehova omwe anamangidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira ku Greece, Japan, Poland, dziko limene linkatchedwa Yugoslavia ndi m’mayiko ena.

Chigawo chomaliza chili ndi mutu wakuti “Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse,” wochokera pa Chivumbulutso 14:6. Chigawochi chikusonyeza zochita za Mboni za Yehova masiku ano. Zithunzi zambirimbiri zimene zili pakhoma m’chigawochi zikusonyeza mmene gulu lathu lakulira mofulumira kwambiri, mmene timalalikirira mwakhama ndiponso chikondi chimene timasonyezana. Munthu akamaliza kuona zinthu zochititsa chidwizi, angapite pamalo enaake m’nyumba yomweyi pamene pali makompyuta. Pamenepo angathe kuwerenga nkhani komanso kuona zithunzi za nyumba zotchedwa Nyumba ya Baibulo komanso Chihema cha ku Brooklyn. Nyumbazi ndi zomwe a Mboni za Yehova ankagwiritsa ntchito zaka zoposa 100 zapitazo.

Malo achionetserowa ali ku 25 Columbia Heights ku Brooklyn, mumzinda wa New York. Amawatsegula kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu nthawi ya 8 koloko m’mawa mpaka 5 koloko madzulo ndipo kulowa pakhomo ndi ulere. Ngati muli mumzinda wa New York, bwerani mudzaone chionetsero chosangalatsa cha mbiri ya Mboni za Yehova.