Yehova anaonetsa Ezekieli masomphenya a galeta lalikulu lakumwamba. Galeta limeneli likuimira mbali yosaoneka ya gulu la Yehova. Ngakhale kuti galetali ndi lalikulu kwambiri, likuthamanga pa liwiro lalikulu ndipo likutha kukhotera kwina kulikonse mofulumira kwambiri. (Ezek. 1:15-28) Zinthu zosangalatsa zimene zachitika m’chaka chapitachi zikusonyeza kuti mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova Mulungu ilinso pa liwiro lalikulu.