• CHAKA CHOBADWA 1966

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1986

  • MBIRI YAKE Ndi wolumala koma anayamba upainiya wokhazikika.

NDINABADWA wolumala kuyambira m’chiuno ndipo ndinkakhala ku Freetown limodzi ndi mayi anga komanso mabanja ena angapo osauka. Ndinkachita manyazi komanso mantha kutuluka m’nyumba moti pamene ndinkakwanitsa zaka 18 ndinali nditangotuluka kamodzi kokha.

Ndiyeno ndili ndi zaka 18, mmishonale wina dzina lake Pauline Landis anafika kwathu n’kunena kuti akufuna kundiphunzitsa Baibulo. Nditamuuza kuti sinditha kuwerenga ndi kulemba, Pauline ananena kuti andiphunzitsa. Choncho ndinavomera.

Ndinkasangalala kwambiri ndi zimene ndinkaphunzira m’Baibulo. Tsiku lina ndinafunsa Pauline ngati angandilole kupita ku misonkhano yomwe inkachitikira pafupi. Ndinamuuza kuti: “Ndiyenda ndekha. Ndikwawa pogwiritsa ntchito matabwa anga.”

Pauline atabwera kudzanditenga, mayi anga komanso anthu ena ankaona kuti ndizunzika. Koma ndinangogwira matabwawo  n’kuyamba kukwawa. Pamene tinkadutsa malo ena, aneba athu anakalipira Pauline n’kumati: “Iwee, kodi ukumuzunziranji munthu? Anayesapotu kuyenda ameneyo ndipo zinakanika.”

Ndiyeno Pauline anandifunsa mokoma mtima kuti: “Jay, tipitedi?”

Ndinayakha kuti: “Eee! Ndikufuna ndine. Tiyeni.”

Anthuwo ataona kuti ndafika pageti ndipo ndikutuluka anayamba kundichemerera.

Misonkhano ya tsiku limenelo inandisangalatsa kwabasi. Kenako ndinkafuna kukafika ku Nyumba ya Ufumu. Koma kuti ndikafike ndinafunika kuyenda mpaka kukafika kumapeto kwa msewu. Ndiyeno n’kukwera galimoto mpaka kukafika paphiri linalake. Kenako abale ankandinyamula kukafika pa Nyumba ya Ufumu. Nthawi zambiri ndinkafika zovala zitanyowa komanso zili matope okhaokha moti ndinkafunika kusintha ndikafika. Mwamwayi mlongo wina wa ku Switzerland ananditumizira njinga ndipo ndinkayenda mosavutikira.

Nditawerenga nkhani zina za abale ndi alongo olumala, ndinaganiza zochita zambiri potumikira Yehova. Mu 1988, ndinayamba upainiya wokhazikika. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kuphunzitsa Baibulo m’bale wanga mmodzi komanso munthu mmodzi m’dera lathu. Yehova anayankha pempheroli moti ndinathandiza ana awiri a mchemwali wanga komanso mayi wina amene ndinakumana naye pamsewu kukhala a Mboni za Yehova.

Panopa mikono yanga yafooka moti ndimadalira anthu ena kuti azindiyendetsa. Thupili limandiphwanyanso koopsa. Koma kuphunzitsa anthu ena kumandithandiza kuti ndisamamve ululu kwambiri. Zimenezi zimandisangalatsa komanso kundilimbikitsa. Ndimaona kuti Yehova wandithandiza ndipo ndikuchita zinthu zaphindu pa moyo wanga.