Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2014

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Wa Nsanja ya Olonda

James Koroma

Wa Nsanja ya Olonda
  • CHAKA CHOBADWA 1966

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1990

  • MBIRI YAKE Ankanyamula mabuku ndi makalata pa nthawi ya nkhondo yapachiweniweni.

M’CHAKA cha 1997, zigawenga zinkamenyana ndi asilikali aboma mumzinda wa Freetown. Pa nthawi imeneyi ndinadzipereka kuti ndizikatenga makalata ku Freetown n’kukatula ku ofesi ya nthambi yomwe inali yongoyembekezera mumzinda wa Conakry, ku Guinea.

Nthawi ina ndinakwera basi ndi gulu lina la anthu. Tinamva mfuti zikuombedwa chapataliko ndipo tonse m’basimo tinachita mantha kwambiri. Titangoyenda pang’ono m’katikati mwa taunimo, bomba linaphulika pafupi ndi basiyo. Dalaivala wa basiyo anangotembenuka n’kutenga msewu wina. Titangoyenda pang’ono tinakumana ndi gulu la zigawenga ndipo linalamula kuti aliyense atsike. Anatifunsa mafunso kenako n’kutiuza kuti tizipita. Kenako tinapeza gulu lina lomwe linatiimitsanso. Chifukwa chakuti mmodzi wa anthu amene anali m’basimo ankadziwana ndi mkulu wawo, anatilola kuti tidutse. Titatsala pang’ono kutuluka m’tauni ya Freetown, tinapeza gulu lachitatu la zigawenga. Linangotifunsa mafunso n’kutilola kuti tidutse. Tinalowera chakumpoto ndipo  tinakwanitsa kudutsa malodibuloko ambiri mpaka tinakafika mumzinda wa Conakry. Tinafika chakumadzulo ndipo basiyo inali fumbi lokhalokha.

Nthawi zina ndinkanyamula makatoni a mabuku, katundu wina wa mu ofesi, mapepala a ofesi ya nthambi komanso zinthu zothandizira anthu amene akuvutika. Nthawi zambiri ndinkayenda pa galimoto komanso pa basi. Ndikamadutsa m’nkhalango ndinkapempha anyamata am’midzi kuti andinyamulire makatoniwo koma ndikamawoloka mitsinje ndinkaika makatoniwo m’mabwato.

Tsiku lina ndinatenga katundu ku Freetown ndipo ndimapita naye ku Conakry pa basi. Titafika pamalire a mayiko awiriwa zigawenga zinaimitsa basi yathu. Mmodzi mwa zigawengazo ataona chikwama changa anayamba kundifunsa mafunso osonyeza kuti akundikayikira. Kenako ndinazindikira kuti pagulu la zigawengapo panali mnzanga wina amene ndinaphunzira naye sukulu. Anzakewo ankamutchula kuti Chigandanga chifukwa pagulu lonselo anali woopsa ndi iyeyo. Ndinauza yemwe ankandifunsa uja kuti ndabwera kuti ndionane ndi Chigandanga, kenako ndinamuitana. Nthawi yomweyo Chigandanga anandizindikira n’kubwera pamene ndinali. Tinakumbatirana komanso tinaseka nkhani zingapo. Kenako anasintha nkhope n’kuyamba kuoneka molusa.

Anandifunsa kuti: “Pali vuto lililonse?”

Ndinamuyankha kuti: “Ndikufuna ndilowe m’dziko la Guinea.”

Nthawi yomweyo analamula zigawenga zinazo kuti zilole basi yathu idutse popanda kufufuza katundu wa m’basimo.

Kungoyambira nthawi imeneyo, ndinkati ndikafika pamalo amenewa, Chigandanga ankauza anzake kuti andilole ndidutse. Ndinkawagawira magazini ndipo ankasangalala nawo kwambiri moti ankangonditchula kuti Wa Nsanja ya Olonda.