Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2014

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Kuyambira mu 2002 mpaka 2013 (Gawo 1)

Kuyambira mu 2002 mpaka 2013 (Gawo 1)

 “Zikomo Yehova”

Zinthu zinayamba kuyendako bwino ndipo abale ndi alongo anayamba kubwerera kwawo. Mipingo imene inasokonekera chifukwa cha nkhondo inayambiranso, makamaka imene inali kum’mawa kwa Sierra Leone chifukwa ndi kumene nkhondo inavuta kwambiri. Apainiya apadera omwe ankatumikira m’dera lina ananena kuti: “Titayambiranso kusonkhana, tsiku loyamba tinali anthu 16, tsiku lachiwiri kunabwera anthu 36, lachitatu kunabwera anthu 56 ndipo pa Chikumbutso kunabwera anthu 77. Tinasangalala kuona anthu ambiri akubwera kudzasonkhana nafe.” Panapangidwanso mipingo ina yokwana 9, zomwe zinachititsa kuti mipingo yonse ikwane 24. Kunabweranso amishonale ena okwana 10 ndipo kubwera kwawoko kunalimbikitsa kwambiri ntchito yolalikira. M’chaka cha 2004, anthu amene anabwera pa Chikumbutso anali 7,594, chomwe ndi chiwerengero chapamwamba kwambiri chifukwa panali ofalitsa pafupifupi 1,500 okha. Zinthu zinayambanso kuyenda bwino ku Guinea.

Bungwe Lolamulira linatumiza ndalama zothandizira anthu amene anathawa ku Guinea pa nthawi ya nkhondo kuti akapeze poyambira akabwerera kwawo. (Yak. 2:15, 16) Magulu ongodzipereka kuthandiza anthu anamanga kapena kukonza Nyumba za Ufumu zokwana 12 komanso Nyumba ya Msonkhano ya ku Koindu. Anamanganso nyumba za njerwa zokwana 42 za mabanja amene nyumba zawo zinali zitawonongekeratu. Mmodzi mwa anthu amene anawamangira nyumbazi ndi mlongo wina wamasiye wazaka za m’ma 70. Mlongoyu ataima pambali pa nyumba yake yamalata, misozi ya chisangalalo ikutsikira m’masaya, ananena kuti: “Zikomo, Yehova. Yehova zikomo. Abale inu, zikomo kwambiri.”

 Ofesi ya nthambi inayambanso kumanga Nyumba za Ufumu pogwiritsa ntchito ndalama zothandizira mayiko osauka. M’bale wina, yemwe ndi mkulu komanso mpainiya mumpingo wa Bo West, ananena kuti: “Mlongo wina anandiuza kuti: ‘Ndikadzangomva kuti tikhala ndi Nyumba ya Ufumu yatsopano, ndidzawombera m’manja ndi kuphazi komwe.’ Nditangolengeza kuti tikhala ndi Nyumba ya Ufumu yatsopano, mlongo uja anadumpha pamene anakhala, n’kuyamba kuvina komanso kuwombera m’manja ndi kuphazi komwe.”

M’chaka cha 2010, mpingo wa Waterloo unapatulira Nyumba ya Ufumu yatsopano yomwe inali yoti akhoza kuiwonjezera n’kukhala malo a msonkhano okwana anthu 800. Tsiku limene mpingowu unagula nyumbayi, mwiniwake anali atangouzidwa kumene ndi munthu wina kuti akhoza kugula malowo pamtengo wokwererapo poyerekeza ndi umene abalewo ananena. Mwini maloyo ananena kuti: “Kuli bwino ndigulitse malo angawa kwa anthu amene aziwagwiritsa ntchito polambira kusiyana n’kuti ndiwagulitse kwa munthu woti azingochitapo malonda basi.”

Pogwiritsa ntchito ndalama zothandizira mayiko osauka, Nyumba za Ufumu 17 zinamangidwa ku Sierra Leone ndipo 6 zinamangidwa ku Guinea. Nyumbazi si zogometsa koma ndi zabwino komanso zopatsa ulemu ndipo zathandiza kuti anthu ambiri azibwera pa misonkhano yathu.

Tinapeza Nkhosa Zosochera za Yehova

Pamene anthu ambiri ankagwira mwakhama ntchito yolalikira, ofesi ya nthambi inakonza zoti kwa miyezi iwiri abale ndi alongo akalalikire m’madera amene salalikidwa kawirikawiri. Ofalitsa anagawira mabuku pafupifupi 15,000 ndipo anasangalala kwambiri ndi mmene zinthu zinayendera. Anthu ena am’deralo anafunsa ngati Mboni za Yehova zikuganiza zokhazikitsa mipingo ndipo zinachitikadi kuti panadzakhazikitsidwa mipingo iwiri. M’mudzi wina wakutali kwambiri, abale anapeza alongo awiri omwe anasiya kusonkhana chifukwa chothawa nkhondo. Nthawi yomweyo abale anakonza zoti m’mudzimo  muzichitika misonkhano ndipo anthu ambiri anayamba kuphunzira Baibulo.

M’chaka cha 2009, abale a ku ofesi ya nthambi anamva kuti m’mudzi wina womwe uli m’katikati mwa nkhalango ya ku Guinea, muli anthu amene akumanena kuti ndi a Mboni za Yehova. Abale atapita kukafufuza anapeza kuti m’bale wina yemwe anali wachikulire anasiya ntchito n’kubwerera kumudzi kwawo. Asanamwalire anaphunzira Baibulo ndi anthu angapo. Mmodzi mwa anthu amene anaphunzira Baibulowo, anakhulupirira Yehova n’kuyamba kuuza anthu ena zimene anaphunzirazo. Munthuyo ankachititsanso misonkhano pogwiritsa ntchito mabuku a m’bale amene anamwalirayo. Kwa zaka 20, kagulu kameneka kankalambira Yehova popanda wa Mboni aliyense kudziwa. Ofesi ya nthambi inatumiza abale kuti akawathandize mwauzimu. M’chaka cha 2012, anthu okwana 172 ochokera m’mudzi umenewo anapezeka pamwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Khristu.

Posachedwapa, anthu ambiri amene anali ngati ‘nkhosa zosochera’ akhala akubwerera. Panali ena omwe anafooka komanso amene nthawi inayake anachotsedwa mumpingo. Ambiri amene anali olowerera abwereranso m’choonadi ndipo anthu a Yehova akhala akuwalandira ndi manja awiri.—Luka 15:11-24.

Asilamu Aphunzira Choonadi

Polalikira kwa anthu ena, mtumwi Paulo anakhala “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana.” (1 Akor. 9:22, 23) Ndi zimenenso atumiki a Yehova a ku Sierra Leone ndi ku Guinea amachita. Iwo amasintha ulaliki wawo n’cholinga choti afike pamtima anthu osiyanasiyana amene amakumana nawo. Anthu ambiri m’mayiko awiriwa ndi Asilamu. Koma Asilamu ena amamvetsera uthenga wabwino, ndipo ofalitsa ena amapeza njira zowafikira pamtima.

Mwachitsanzo, Saidu Juanah, yemwe poyamba anali Msilamu, ananena kuti: “Asilamu amakhulupirira kuti Adamu analengedwa kuchokera ku fumbi koma amati atalengedwa anali  ku paradaiso wakumwamba. Ndiye pofuna kuwathandiza kudziwa zolondola, ndimawafunsa kuti, ‘Kodi fumbi limapezeka kuti?’

“Iwo amayankha kuti, ‘Padziko lapansi.’

“Kenako ndimawafunsanso kuti, ‘Ndiye kuti Adamu anamulengera kuti?’

“Amayankha kuti, ‘Padziko lapansi.’

“Tsopano kuti amvetse mfundoyo ndimawerenga Genesis 1:27, 28 n’kuwafunsa kuti, ‘Kodi zolengedwa zakumwamba zimakhala ndi ana?’

“Iwo amayankha kuti, ‘Ayi, chifukwa angelo si aamuna kapena aakazi.’

“Ndimawafunsanso kuti, ‘Ndiye pamene Mulungu ankauza Adamu ndi Hava kuti abereke ana, ayenera kuti anali kuti?’

“Iwo amayankha kuti, ‘Ayenera kuti anali padziko lapansi.’

“Ndimawafunsanso kuti, ‘Ndiye Mulungu akadzabwezeretsa Paradaiso, ndiye kuti Paradaisoyo adzakhala kuti?’

“Okha amayankha kuti, ‘Ndiye kuti Paradaiso adzakhala padziko lapansi pompano.’”

Saidu ananenanso kuti: “Kukambirana nawo Malemba m’njira imeneyi kumachititsa kuti Asilamu amene amafunitsitsa kudziwa zoona amvetsere ndiponso kulandira mabuku athu.”

Taganizirani zimene zinachitikira Momoh, yemwe anali Msilamu komanso anali ndi shopu. Iye ankayembekezera kuti tsiku lina adzakhala m’tsogoleri wachisilamu. Amishonale atawerenga naye Malemba angapo, Momoh anachita chidwi kwambiri. Anapita kukamvetsera mbali ina ya msonkhano wadera ndipo anasangalala kwambiri ndi zimene anamva kumsonkhanoko. Patapita masiku 4, Momoh ndi mkazi wake, Ramatu, pamodzi ndi ana awo 5, anapita kumwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Kenako Momoh anayamba kuphunzira Baibulo mwakhama. Ataphunzira kwa maulendo angapo anasiya kugulitsa fodya mushopu mwake. Anthu ofuna kugula fodya akabwera, iye ankawauza kuti fodya amawononga thupi la munthu komanso kuti Mulungu sasangalala  ndi anthu amene amasuta fodya. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo ndi banja lonse pashopu pomwepo. Makasitomala amati akabwera n’kuwapeza akuphunzira, Momoh amawauza kuti adikire kaye chifukwa phunzirolo ndi lofunika kwambiri kwa aliyense pabanjapo. Momoh ndi Ramatu anakalembetsa ukwati wawo koma abale awo ankawatsutsa kwambiri. Iwo sanafooke kapena kuchita mantha ndipo analimba mtima kuwalalikira abale awo amene ankawatsutsawo. Patapita nthawi, abale awo aja anayamba kulemekeza komanso kuyamikira makhalidwe awo abwino. Momoh anabatizidwa mu 2008 ndipo Ramatu anabatizidwa mu 2011.

Kutsatira Lamulo la Mulungu Lokhudza Magazi

Anthu a Yehova amayesetsa kutsatira mfundo za Mulungu molimba mtima. Imodzi mwa mfundo zimene amatsatira ndi yokhudza mmene Yehova amaonera magazi. (Mac. 15:29)  Chifukwa chakuti Akhristu akhala akuyesetsa kutsatira mfundo imeneyi, madokotala ambiri a ku Sierra Leone ndi ku Guinea ayambanso kuitsatira.

Abale akulimbikitsa mlongo m’chipatala

M’chaka cha 1978, abale anagawira kabuku kamutu wakuti, Jehovah’s Witnesses and the Question of Blood kwa madokotala, manesi, oyang’anira zipatala, maloya komanso oweruza onse a ku Sierra Leone. Pasanapite nthawi yaitali, mlongo wina, yemwe anali atatsala pang’ono kubereka, anayamba kukha magazi m’mimba ndipo madokotala anakana kumuthandiza popanda kugwiritsa ntchito magazi. Komabe, dokotala wina amene anawerenga kabuku kaja anavomera kuti amuthandiza. Mlongoyo anabereka mwana wamwamuna wathanzi ndipo anachira bwinobwino.

M’chaka cha 1991, dokotala wina wopanga maopaleshoni pachipatala cha Kenema, dzina lake Bashiru Koroma, anawerenga kabuku kakuti, Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu? Atakhutira ndi zimene anawerengazo anayamba kuphunzira Baibulo komanso kupezeka pa misonkhano ya Chikhristu. Mnyamata wina wazaka 9, wa Mboni, anachita ngozi n’kuvulala kwambiri. Madokotala ena anakana kumupanga opaleshoni yopanda magazi. Iwo anauza makolo ake kuti, “Mutengeni mwana wanuyo akafere kunyumba.” Makolo ake a mnyamatayo anapita kwa a Koroma ndipo anamupanga opaleshoniyo bwinobwino.

Kenako a Koroma anabatizidwa ndipo ankadzipereka kuthandiza anthu popanda kugwiritsa ntchito magazi. Chifukwa cha zimenezi, madokotala ena ankadana nawo kwambiri koma odwala onse amene m’bale Koroma ankawathandiza ankachira bwinobwino. Patapita nthawi, madokotala ena anayamba kumawafunsa akakumana ndi vuto linalake popanga opaleshoni.

Kuyambira m’chaka cha 1994, Dipatimenti Yoyang’anira Zachipatala ku nthambi ya ku Freetown inakhazikitsa Makomiti Olankhulana ndi Achipatala ku Sierra Leone ndi ku Guinea. Makomitiwa akhala akuthandiza Mboni zambiri zikadwala komanso kupempha madokotala kuti azithandiza a Mboni popanda kuwaika magazi.