Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2014

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Kuyambira mu 1945 mpaka 1990 ‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kukhala Olungama—Dan. 12:3. (Gawo 3)

Kuyambira mu 1945 mpaka 1990 ‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kukhala Olungama—Dan. 12:3. (Gawo 3)

Kulimbana ndi Gulu Lotchedwa Poro

Amuna ambiri a mtundu wa Kisi anali m’gulu la Poro, lomwe linkachita kwambiri zamizimu. Koma m’mudzi wina wapafupi ndi tauni ya Koindu, munali amuna ena a m’gululi omwe ankaphunzira Baibulo komanso kupita ku misonkhano. Iwo anali oyamba kuukiridwa ndi gululi. M’bale James Mensah, amene anali mmishonale wochokera ku Ghana anati: “Anthu amene ankaphunzira Baibulowo atakana kuchita nawo miyambo yokhudzana ndi kukhulupirira mizimu, mtsogoleri wa gululi anakwiya kwambiri. Mtsogoleriyu ndi anthu ake anamenya ophunzirawo, kuwabera katundu wawo, kutentha nyumba zawo, kuwamanga ndi matcheni n’kuwasiya pathengo kuti afe ndi njala. Mfumu yaikulu inalimbikitsa gululi kuti lipitirize kuchita nkhanzazi. Ngakhale kuti ophunzirawo ankazunzidwa choncho, sanabwerere m’mbuyo.”

 Abale ku Koindu anakanena nkhaniyi kupolisi, ndipo mtsogoleri uja, anthu ake komanso mfumu yaikulu ija anamangidwa. Iwo anadzudzulidwa kwambiri ndipo mfumu yaikuluyo anaiimitsa pa udindo wake kwa pafupifupi chaka chimodzi. Zimenezi zinadziwika m’dera lonselo ndipo zinalimbitsa mtima anthu ambiri moti anayamba kupezeka pa misonkhano. Patapita nthawi mfumu yaikulu ija inasintha ndipo inayamba kuchita chidwi ndi uthenga wabwino. Msonkhano wadera utachitikira m’dera lawo, mfumuyi inapereka ng’ombe yaikulu komanso nyumba yoti mugone alendo.

Atsogoleri ena a gulu la Poro anayamba kugwiritsa ntchito njira zina polimbana ndi abalewo. Iwo ‘ankayambitsa mavuto mwa kupanga malamulo.’ (Sal. 94:20) Aphungu a m’gululi anapempha Nyumba ya Malamulo kuti ikhazikitse lamulo loletsa Mboni za Yehova. Charles Chappell anati: “Koma mfumu yaikulu ija inatsutsa zimenezi, ndipo inauza Nyumba ya Malamuloyo kuti iye wakhala akuphunzira ndi Mboni kwa zaka ziwiri. Ananenanso kuti gulu lathu sililowerera ndale koma limaphunzitsa anthu ndi kuwathandiza kukhala ndi makhalidwe abwino. Kenako anauza anthu onse m’nyumbayo kuti iyenso akufuna kukhala Wamboni. Ndiyeno phungu wina, amene anaphunziranso ndi Mboni, atagwirizana ndi zimene mfumuyo inanena, nkhaniyi inathera pomwepo.”

Ankamunena kuti, “Ukadya kwa Mulungu komweko”

Anthu amene ankatuluka m’gulu la Poro ankatsutsidwa kwambiri ndi achibale awo. Mwachitsanzo, azigogo a mnyamata wina ku Koindu, dzina lake Jonathan Sellu anali ansembe a m’gululi ndipo anthu ankafuna kuti nayenso adzakhale wansembe. Koma atayamba kuphunzira Baibulo anasiya kuchita nawo miyambo komanso kupereka nsembe zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu. Achibale ake ankamutsutsa kwambiri ndipo anamusiyitsa sukulu. Akapita ku misonkhano ya mpingo, ankamumana chakudya ndipo ankamunena kuti: “Ukadya kwa Mulungu komweko.” Koma Jonathan sanabwerere m’mbuyo. Sankasowa chakudya komanso anaphunzira kuwerenga ndi kulemba. Kenako anakhala  mpainiya wokhazikika ndipo anasangalala kwambiri amayi ake atayamba kuphunzira Baibulo.

Mipingo Inakhazikitsidwanso M’madera Ena

Mu 1960, ku Bo, Freetown, Kissy, Koindu, Lunsar, Magburaka, Makeni, Moyamba, Port Loko, Waterloo ndi ku Kabala n’kumene kunali mipingo ndi magulu akutali. Chaka chimenecho chiwerengero cha ofalitsa chinawonjezeka kuchoka pa 182 kufika pa 282. Apainiya apadera ochokera ku Ghana ndi ku Nigeria anabwera kudzalimbikitsa mipingoyi.

Atsopano ambiri anali a mtundu wa Kiliyo umene umapezeka ku Freetown ndi madera ozungulira, komanso mtundu wa Kisi umene umapezeka ku Eastern Province. Koma uthenga utayamba kufalikira, anthu a mitundu ina anayambanso kuphunzira Baibulo. Mitundu yake ndi monga mtundu wa Kuranko, Limba ndi Temne, ya kumpoto kwa dzikoli, mtundu wa Mende wa kum’mwera ndi mitundu ina.

Nyumba ya Ufumu ya mpingo wa Freetown East anaitsegulira m’chaka cha 1961. Kenako mpingo wa Koindu unatseguliranso Nyumba ya Ufumu yawo yokwana anthu 300 imene anamanga ndi zidina. M’nyumbayi ankachitiramonso misonkhano ikuluikulu. Pasanapite nthawi, ku Sierra Leone kunachitika Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yoyamba ndipo akulu 40 analowa sukuluyi. Chinanso chimene chinachitika m’chaka chimenechi ndi ntchito yogawira Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika.

Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Sierra Leone, mu 1961. William Nushy (mzere wakumbuyo, pakati), Charles Chappell (mzere wapakati, wachiwiri kuchokera kumanja), ndi Reva Chappell (mzere woyamba, wachitatu kuchokera kumanja)

Zinali zoonekeratu kuti Yehova akudalitsa anthu ake. Pa July 28, 1962, bungwe la Mboni za Yehova la International Bible Students Association, limene limagwiritsidwa ntchito m’mayiko ambiri, linalembetsedwa ku boma la Sierra Leone.

 Uthenga Wabwino Unafika ku Guinea

Tsopano tiyeni tikambirane za dziko la Guinea (limene kale linkadziwika kuti French Guinea). Chaka cha 1958 chisanafike, abale angapo amene ankadutsa m’dzikoli analalikira mwachidule kwa anthu ena. Koma akuluakulu aboma ochokera ku France ankatsutsa ntchito yathu. Komabe mu 1958, dziko la Guinea litalandira ufulu, mwayi unatseguka.

Chakumapeto kwa chakachi, m’bale Manuel Diogo wochokera m’dziko la Benin (limene kale linkadziwika kuti Dahomey) anafika m’tauni ya Fria. Iye anali ndi zaka zoposa 30 ndipo ankalankhula Chifulenchi. M’baleyu anabwera kudzagwira ntchito pamgodi wa mtapo wa aluminiyamu m’tauni imeneyi. Tauniyi inali pa mtunda wa makilomita 80 kuchokera kumzinda wa Conakry, womwe ndi likulu la dzikoli. M’bale Diogo ankafunitsitsa kuyamba kulalikira m’dera limeneli. Choncho analembera kalata nthambi ya ku France yopempha  kuti amutumizire mabuku komanso apainiya apadera kuti adzamuthandize. Kumapeto kwa kalatayi ananena kuti: “Ndikukhulupirira kuti Yehova adalitsa ntchito imeneyi chifukwa kuno kuli anthu ambiri amene akufuna kuphunzira Baibulo.”

Nthambi ya France inalembera M’bale Diogo kalata yolimbikitsa kwambiri ndipo inamupempha kuti ngati n’zotheka akhalebe ku Guinea. Nthambiyi inatumizanso mpainiya wapadera kuti akamuphunzitse ntchito yolalikira. Zimenezi zinamulimbikitsa kwambiri m’baleyu moti anapitiriza kulalikira mwakhama ku Fria mpaka pamene anamwalira mu 1968.

M’bale Wilfred Gooch, yemwe anali woyendera nthambi, atafika ku Conakry mu 1960, anapeza abale awiri a ku Africa konkuno akulalikira mumzindawu. M’bale Gooch anaona kuti zingakhale bwino kuti nthambi ya ku Sierra Leone iziyang’anira ntchito yathu ku Guinea m’malo mwa nthambi ya France. Zimenezi zinachitikadi pa March 1, 1961. Patapita mwezi umodzi, mpingo woyamba ku Guinea unakhazikitsidwa mumzinda wa Conakry.

Uthenga Wabwino Unafika M’madera a Kunkhalango

Uthenga wabwino unafalikiranso kum’mwera kwa dziko la Guinea. Mtsogoleri wa mtundu wa Kisi, dzina lake Falla Gbondo, amene ankakhala ku Liberia, anabwerera kumudzi kwawo ku Fodédou. Mudziwu unali pa mtunda wa makilomita 13 kumadzulo kwa mzinda wa Guékédou. Pobwera anatenga buku lakuti Kucokera ku Paradaiso Wotayika Kunka ku Paradaiso Wopezekanso. Falla sankadziwa kuwerenga, koma ankangofotokozera anzake zithunzi za m’bukuli. Iye anati: “Bukuli linachititsa kuti anthu ayambe kukambirana nkhani za m’Baibulo, ndipo ankalitchula kuti buku la Adamu ndi Hava.”

Falla anabwerera ku Liberia ndipo anabatizidwa, kenako anakhala mpainiya wapadera. Kawiri pa mwezi iye ankapita ku Fodédou kukaphunzira ndi gulu la anthu 30. Pasanapite nthawi, anayamba kuyendera limodzi ndi mpainiya wina  wapadera wa ku Liberia komweko, dzina lake Borbor Seysey, yemwenso anali wa mtundu wa Kisi. Abalewa anakhazikitsa kagulu kena ku Guékédou. Timagulu tonseti tinadzakhala mipingo.

Anthu ambiri a mtundu wa Kisi atakhala Mboni, mafumu awo anayamba kuona makhalidwe awo abwino. Abalewo ankagwira ntchito mwakhama, anali oona mtima komanso ankakhala mwamtendere ndi anthu ena. Choncho abalewo atapempha chilolezo kuti amange Nyumba ya Ufumu ku Fodédou, mafumuwo anawapatsa malo okwana maekala 8. Nyumba ya Ufumu imeneyi inali yoyamba m’dziko la Guinea ndipo inamalizidwa kumayambiriro kwa chaka cha 1964.

Mavuto Anayamba ku Conakry

Koma zinkaoneka kuti mavuto angayambe ku Conakry nthawi ina iliyonse. Chifukwa cha mavuto a ndale, akuluakulu a zandale anayamba kukayikira anthu ochokera m’mayiko ena. Amishonale 4 anawakaniza chilolezo chokhalira m’dzikolo ndipo anawabweza. Abale awiri a ku Ghana anamangidwa pa milandu yongowanamizira ndipo anawatsekera m’ndende pafupifupi miyezi iwiri.

Atangowatulutsa, mmodzi mwa abalewo, dzina lake Emmanuel Awusu-Ansah, anamangidwanso ndipo ankamuzunza kwambiri. Ali m’ndende yonyansa kwambiri, analemba kuti: “Ndine wolimba mwauzimu, ndipo ngakhale kuti ndikumadwala malungo pafupipafupi, ndimalalikira. Mwezi watha ndinalalikira maola 67 ndipo anthu awiri amene ndinkaphunzira nawo, anayambanso kulalikira.” Munthu mmodzi amene ankaphunzira naye Baibulo anakhala wa Mboni. Patatha miyezi 5, m’baleyu anamasulidwa ndipo anam’tumiza ku Sierra Leone. Choncho ku Conakry kunangotsala wofalitsa mmodzi yekha.

Mu 1969, mavuto a ndale aja atachepa, apainiya apadera anafika mumzinda wa Conakry. Atapempha chilolezo kuboma, anapeza nyumba n’kuisandutsa Nyumba ya Ufumu ndipo  anaikapo chikwangwani. Pasanapite nthawi, anthu pafupifupi 30 anayamba kubwera ku misonkhano.

Poyamba, abalewo ankalalikira mwamantha poopa kumangidwa. Koma kenako anayamba kulimba mtima ndipo ankalalikira mwakhama. M’chaka cha 1973, mpingo waung’onowo unagawira timapepala 6,000. Kenako ofalitsawa anayamba kugawira magazini m’maofesi komanso m’malo abizinezi. Pang’ono ndi pang’ono akuluakulu aboma komanso anthu ena anayamba kumvetsa cholinga cha ntchito yathu ndipo ankayamikira. Pa December 15, 1993, bungwe la Christian Association of Jehovah’s Witnesses of Guinea linalembetsedwa kuboma. Izi zinatheka chifukwa chakuti abalewo anali akhama komanso oleza mtima.