• CHAKA CHOBADWA 1960

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1974

  • MBIRI YAKE Anayamba umishonale mu 1992. Watumikira ku Guinea ndi ku Senegal. Panopa akutumikira ku Sierra Leone.

NDITANGOKHALA milungu iwiri yokha ku Sierra Leone ndinayamba kulikonda kwambiri dzikoli. Ndinkachita chidwi ndikaona anthu atadendekera katundu wolemera. M’madera osiyanasiyana munkangokhala anthu balalabalala. Ana ankakonda kusewera komanso kuvina mumsewu kwinaku akuwomba m’manja. Ndinkachita chidwi ndi zimene anthu ankachita komanso nyimbo zawo.

Koma chimene chimandisangalatsa kwambiri kunoko ndi kulalikira. Anthu a ku Sierra Leone amalandira bwino alendo. Amalemekeza Baibulo ndipo amamvetsera kwambiri. Nthawi zambiri amandiitanira m’nyumba zawo. Ndikamachoka, ena amandiperekeza mpaka kukandifikitsa kumsewu. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizipirira mavuto ang’onoang’ono amene ndimakumana nawo monga kusowa kwa madzi komanso magetsi.

Chifukwa chakuti sindili pabanja, nthawi zina anthu amandifunsa ngati ndimasowa wocheza naye. Koma zoona zake n’zakuti, ndimakhala ndi zochita zambiri moti sindikhala ndi nthawi yomaonanso ngati ndilibe wocheza naye. Ndine wosangalala chifukwa ndimakhala ndi zochita zambiri.