Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Ndinapeza Chinthu Chamtengo Wapatali Kuposa Dayamondi

Tamba Josiah

Ndinapeza Chinthu Chamtengo Wapatali Kuposa Dayamondi
  • CHAKA CHOBADWA 1948

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1972

  • MBIRI YAKE Asanaphunzire choonadi ankagwira ntchito m’migodi ya miyala ya dayamondi. Panopa akutumikira m’Komiti ya Nthambi ya ku Sierra Leone.

MU 1970, ndinkagwira ntchito pakampani ya migodi m’tauni ya Tongo. Tauniyi ili kumpoto kwa chigawo cha Kenema ndipo mumapezeka miyala yambiri ya dayamondi. Eni ake a kampaniyi anali ochokera ku Britain. Ndikakhala kuti sindikugwira ntchito ndinkasakasakanso miyalayi. Ndikaipeza ndinkatchena n’kupita ku Kenema kuti ndikaigulitse komanso kuti ndikasangalale.

Mu 1972, ndinakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo. Patangotha miyezi 5, ndinakwanitsa zonse zofunika kuti ndibatizidwe. Chifukwa chakuti ndinalibe masiku opuma, ndinapempha mnzanga wina amene ndinkagwira naye ntchito kuti agwire m’malo mwanga. Ndinkafuna kupita ku msonkhano kuti ndikabatizidwe. Mnzangayo anavomera koma ananena kuti ndimupatse malipiro a mlungu umodzi. Popeza ndinkaona kuti kubatizidwa ndi chinthu chofunika kwambiri kuposa ndalama, ndinalolera. Nditabwerako, anandiuza kuti ndisam’patsenso ndalama zija chifukwa anaona kuti ndinasankha  kuchita chinthu chofunika kwambiri, chomwe ndi kutumikira Mulungu. Patatha miyezi 6, ndinasiya ntchito yanga yamalipiro ambiri ndipo ndinayamba kuunjika chuma kumwamba pochita upainiya wapadera.—Mat. 6:19, 20.

Kwa zaka 18, ndinakhala ndikutumikira monga mpainiya wapadera komanso ngati woyang’anira dera. Ndinakwatirana ndi Christiana, yemwe ndi wokhulupirika ndipo amandithandiza kwambiri. Tili ndi mwana mmodzi dzina lake Lynette.

Ndinkalakalaka nditapeza miyala ya dayamondi. Koma ndinapeza chinthu chamtengo wapatali kuposa dayamondi, chomwe ndi kudziwa Yehova ndi kupeza madalitso ake

Pa nthawi imene ku Sierra Leone kunali nkhondo yapachiweniweni, ine ndi Christiana tinkachita upainiya mumzinda wa Bo, womwe uli m’dera la migodi yambiri ya dayamondi. Kumeneko tinapezako miyala yambiri ya dayamondi wauzimu, omwe ndi anthu ofunitsitsa kukhala ophunzira a Khristu. Mmene zimatha zaka 4, mpingo wathu unali utakula kwambiri. Panopa, ku Bo kuli mipingo itatu ikuluikulu.

Mu 2002, ndinaitanidwa kuti ndikatumikire m’Komiti ya Nthambi ya ku Sierra Leone. Popeza nyumba yathu ili pafupi ndi Beteli, tsiku lililonse ndimayendera. Christiana akutumikira monga mpainiya wapadera ndipo Lynette akutumikira pa Beteli ku dipatimenti yomasulira mabuku mu Chikiliyo.

Ndinkalakalaka nditapeza miyala ya dayamondi. Koma ndinapeza chinthu chamtengo wapatali kuposa dayamondi, chomwe ndi kudziwa Yehova ndi kupeza madalitso ake. Ndinapezanso miyala ya dayamondi yauzimu yokwana 18, omwe ndi anthu amene ndawathandiza kukhala ophunzira a Khristu. Ndine wosangalala kwambiri chifukwa Yehova wandidalitsa kuposa mmene ndinkaganizira.