ZAKA pafupifupi 500 zapitazo, mtengo wa kotoni unamera pamalo amene mtsinje wa Sierra Leone umathirira m’nyanja. Kwa zaka 300, anthu akagwira akapolo ankadutsa nawo pafupi ndi mtengo umenewu. Anthu ankhanzawo anagwira amuna, akazi ndi ana pafupifupi 150,000 ndipo ankawakweza sitima zapamadzi kuti akawagulitse kumayiko ena akutali.

Mtengo wa Kotoni wa ku Freetown

 Pa March 11, 1792, anthu ambirimbiri amene anamasulidwa ku ukapolo ku America anasonkhana pansi pa mtengowu posangalalira kuti abwerera ku Africa. Chifukwa cha chisangalalo chimenechi, malo amene anafikirawa anawapatsa dzina loti Freetown. Akapolo amene anamasulidwa ankafikabe pamalowa mpaka panali anthu a mitundu pafupifupi 100. Anthu amenewa anayamba kuona kuti mtengo umene unali pamalowo ndi chizindikiro cha ufulu komanso tsogolo labwino.

Mboni za Yehova za ku Sierra Leone zakhala zikulimbikitsa anthu kwa zaka pafupifupi 100 tsopano. Zimawauza za “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu,” womwe ndi waukulu kwambiri kuposa ufulu wina uliwonse. (Aroma 8:21) Ufumu wa Mulungu ukadzabweretsa mtendere komanso Paradaiso padziko lapansi, anthu adzamasuka ku ukapolo wa uchimo ndi imfa.—Yes. 9:6, 7; 11:6-9.

Pa zaka 50 zapitazi, ofesi ya nthambi ya ku Sierra Leone yakhala ikuyang’aniranso ntchito yolalikira m’dziko la Guinea. M’dzikoli mwakhala mavuto osiyanasiyana monga azandale komanso azachuma ndipo izi zachititsa kuti anthu ambiri azimvetsera uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo.

Abale ndi alongo ku Sierra Leone ndi ku Guinea amalalikira uthenga wabwino ngakhale kuti akhala akukumana ndi mavuto ambiri. Amakumana ndi mavuto chifukwa cha zinthu ngati umphawi, kusaphunzira, miyambo ya kumeneko, ziwawa ndiponso kusiyana mitundu. Nkhani yotsatira ikusonyeza kuti iwo ndi okhulupirika ndiponso odzipereka kwambiri kwa Yehova. Tikukhulupirira kuti musangalala ndi nkhaniyi ndipo ikuthandizani kuti muzikhulupirira kwambiri “Mulungu amene amapereka chiyembekezo.”—Aroma 15:13.