• MAYIKO 47

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 741,892,871

  • OFALITSA 1,601,915

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 862,555

“Kodi Kapena Mwasochera?”

Mayi wina wa ku Somalia yemwe anapita ku Sweden anaitanidwa kuti apite ku Nyumba ya Ufumu ndipo anapitadi. Koma atafika anakhumudwa ndi zimene zinachitika. Palibe munthu amene anamulandira, ndipo aliyense ankangomuyang’ana. Iye anali womangika. Munthu wina anazindikira kuti mayiyu akuoneka womangika ndipo anamufunsa kuti: “Kodi kapena mwasochera?”

 Iye anayankha kuti: “Ndikuganizadi kuti ndasochera.” Nthawi yomweyo ananyamuka n’kumapita. Mayiyu atakumananso ndi a Mboni amene anamuitanira ku misonkhano aja, anali wokhumudwa kwambiri ndipo anawauza kuti sadzapitakonso. A Mboniwo anadabwa kuti chinachitika n’chiyani chifukwa sanamuone ku Nyumba ya Ufumuyo. Atakambirana kwa kanthawi, onse anazindikira kuti sanapite ku Nyumba ya Ufumu koma anapita kutchalitchi chinachake.

A Mboniwo anamulimbikitsabe kuti adzapite ku Nyumba ya Ufumu. Mayiyo anavomera kuti adzapita, koma sadzakhalitsa akadzaona kuti sikukumusangalatsa. Koma  atangolowa m’Nyumba ya Ufumu, aliyense anamulandira ndi manja awiri. Mayiyo anasangalala kwambiri moti anali womalizira kuchoka ku Nyumba ya Ufumuyo misonkhano itatha. Kungochokera nthawi imeneyo, iye wakhala akupita ku misonkhano mokhazikika ndipo panopa anabatizidwa.

Anapeza Kapepala Koitanira Anthu ku Chikumbutso Mumsewu

Greece: Stergios amauza ena zimene anaphunzira m’Baibulo

Stergios ndi mnyamata yemwe amakhala ku Greece. Tsiku lina m’mawa akuchokera kuntchito, anaganiza zodutsa njira ina imene sakonda kudutsa. Iye anaona kanthu kena pamsewu kamene kanamukopa. Kanali kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso. Kapepalaka kanali ndi funso loti: “Kodi Yesu Mumamudziwa Kuti Ndi Ndani?” Koma Stergios anachita manyazi kutola kapepalako chifukwa panali anthu pafupi. Atafika kunyumba, anayamba kuganizira za funso limene anaona pa kapepala kaja ndipo ankafuna kudziwa yankho lake.

Stergios anali atagwirizana ndi anzake kuti masana a tsiku limenelo akamwe khofi pamalo ena. Atanyamuka kuti akakumane ndi anzakewa, anaganiza zodutsa njira imene anaona kapepala kaja ndipo ankakhulupirira kuti akakapeza kali pompo. Anakapezadi kali pompo, koma anthu anali adakali balalabalala, choncho anachitanso manyazi kukatola. Atamaliza kumwa khofi ndi anzake, anayamba ulendo wopita kwawo ndipo anadutsanso njira yomwe ija ndipo kapepalako kanali kadakali pompo. Apa tsopano anatola kapepalako n’kukawerenga. Atawerenga, anaganiza zopita ku Chikumbutso.

Chikumbutsocho chitatha, Stergios anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Kenako anayamba kupezeka pa misonkhano komanso kupita patsogolo mwauzimu. Stergios anabatizidwa pa msonkhano wapadera m’March 2013.

 Pulogalamu ya pa Wailesi Inachititsa Kuti Anthu Asiye Kudana ndi a Mboni

Mu January 2010, m’bale wina dzina lake Finn, wa mumzinda wa Copenhagen ku Denmark, anapita kokayenda ndipo anatenga magazini. Akuyenda m’kanjira kena, anaona bambo wachikulire akubwera poteropo. M’baleyu anapatsa munthuyo magazini a mwezi wa December 2009, momwe munali nkhani ya Khirisimasi. Pamene ankakambirana naye, Finn anazindikira mawu a munthuyu. Anali muulutsi wotchuka kwambiri wa pulogalamu ina ya pa wailesi. Tsiku lotsatira Finn, akumvetsera pulogalamu imene munthuyu amaulutsa, anadabwa kumva iye akunena kuti anapatsidwa magazini ndi munthu wina dzulo lake. Kenako anawerenga nkhani zina m’magaziniwo pa wailesipo. Nkhani ina imene anawerenga inali yokhudza nyenyezi imene inaonekera pa nthawi ya kubadwa kwa Yesu ndipo anavomereza mfundo yoti Satana ndiye anachititsa kuti nyenyeziyo ioneke.

Finn ataona kuti munthuyu anasangalala ndi magaziniwo, anaganiza zomuimbira foni. Atakambirana kwa kanthawi, Finn anamufunsa ngati zingatheke kuti pa wailesiyo pakhale pulogalamu ya nkhani zokhudza Baibulo. Patatha milungu iwiri anamuyankha kuti n’zotheka. Choncho anayamba kumaulutsa pulogalamu ya maola awiri yonena za Mboni za Yehova komanso Baibulo, ndipo mapulogalamu oposa 30 anaulutsidwa. Muulutsiyo limodzi ndi Finn ankakambirana mitu imene asankha ndipo ankayankha mafunso ambirimbiri amene omvera ankafunsa pa nthawi ya pulogalamuyi.

Munthu wina anaimbira foni munthu wogwira ntchito ku wailesiyi ndipo anamusiyira nambala yake ya foni. Ankafuna kuti a Mboni adzamuyendere. Nthawi yomweyo abale anakonzadi zomuyendera. Munthuyu anali atamva zabodza zokhudza Mboni kuchokera kwa achibale ake komanso anzake. Koma pulogalamuyi inachititsa kuti asiye kudana ndi Mboni za Yehova. Phunziro la Baibulo linayambika ndipo mu 2013 munthuyu anapezeka pa Chikumbutso komanso  pa nkhani yapadera. Panopa Lamlungu lililonse amasonkhana komanso amayankha mfundo zogwira mtima pa Nsanja ya Olonda. Anthu enanso am’derali anayamba kumvetsera uthenga wa m’Baibulo chifukwa cha zomwe anamva pa pulogalamu ya pawailesi ija.

Anasiya Kapepala Kowaitanira ku Msonkhano Pakhomo la Nyumba Yawo

M’bale wina, dzina lake Lucio, amakhala ku Italy, ndipo pa tsiku lomaliza la msonkhano wachigawo akutsanzikana ndi anzake, panafika banja lina. Lucio anafunsa banjalo mpingo umene amasonkhana. Iwo anayankha kuti: “Si ife a Mboni.”

Ndiyeno Lucio anawafunsa kuti: “Pali winawake amene anakuitanirani ku msonkhanowu?”

Iwo anayankha kuti: “Ayi.”

Lucio anachita chidwi kumva kuti iwo anabwera kumsonkhanowu ngakhale kuti palibe amene anawaitana. Choncho anawafunsa kuti: “Ndiye munadziwa bwanji kuti kuli msonkhano?”

Iwo anati: “Tinapeza kapepala koitanira anthu ku msonkhano pakhomo la nyumba yathu ndipo tinaganiza zoti tibwere.”

Atafotokoza za komwe amakhala, mkazi wa Lucio dzina lake Ester, anati: “Ndine ndinasiya kapepalako pakhomo lawo. Linali tsiku lomaliza kugawira timapepala ndipo tinali titamaliza gawo lonse. Choncho ndinaganiza zongosiya kapepalako pakhomo pawo, pomwe panalibe anthu, m’malo mongokataya.” Banjali litapeza kapepalaka pakhomo la nyumba yawo, anaganiza zopita ku Malo a Msonkhano Lamlungu lotsatira kuti akapezeke pa msonkhano. Atacheza kwa kanthawi, Lucio ndi Ester anaitanira banjali kunyumba kwawo kukadya chakudya ndipo anapitiriza kucheza. Banjalo linavomera kuti liyambe kuphunzira Baibulo. Nthawi zonse iwo amakonzekera phunziro lawo la Baibulo, amapezeka pa misonkhano komanso amayankha pa misonkhanopo.