Okondedwa Antchito Anzathu:

Ndife osangalala kwambiri kukulemberani kalata kumayambiriro kwa chaka chapaderachi. Pofika chakumapeto kwa chaka cha 2014, Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu yathu adzakhala atakwanitsa zaka 100 kuchokera pamene anayamba kulamulira pakati pa adani ake.—Sal. 110:1, 2.

Kumayambiriro kwa chaka cha utumiki chino, pa Msonkhano Wapachaka, Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano, inatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi lokonzedwanso. Baibulo limeneli lamasuliridwa bwino kwambiri kuposa lina lililonse. Yehova anagwiritsa ntchito Akhristu odzozedwa kuti amasulire Baibulo la Dziko Latsopano. (Aroma 8:15, 16) Mfundo imeneyi payokha imachititsa kuti Baibuloli likhale lapadera kwambiri.

Kwa zaka zambiri, Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku ya  Bungwe Lolamulira yakhala ikuika patsogolo ntchito yomasulira Baibulo. Panopa, Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu kapena mbali yake chabe, lamasuliridwa m’zinenero 121. Tikukulimbikitsani kuti muzisonyeza kuti mumayamikira Yehova chifukwa chokupatsani Baibulo limeneli. Muziliwerenga ndiponso kusinkhasinkha tsiku lililonse. Mukatero, mudzayandikira kwambiri Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlembi Wamkulu.—Yak. 4:8.

Timakhudzidwa kwambiri tikamva mavuto amene abale ndi alongo athu akukumana nawo. Chifukwa cha mavutowa, ena amalephera kusangalala ndi Akhristu anzawo. Mwachitsanzo, banja lina la ku Asia linakumana ndi vuto lamwadzidzidzi. Mlongo wam’banjali anafa ziwalo ndipo madokotala analephera kumuthandiza. Izitu n’zomvetsa chisoni kwambiri. Mwamuna wake amafunika kumusamalira usana ndi usiku. Ana awo, wamwamuna m’modzi ndi aakazi awiri, amaperekanso chitsanzo chabwino pothandiza makolo awowa. Nonse amene mukupirira mavuto osiyanasiyana, kuphatikizapo banja limeneli, mukhoza kukhala osangalala podziwa kuti mukukwanitsa kupirira zinthu zimene zikuyesa chikhulupiriro chanu. (Yak. 1:2-4) Yehova amatsimikizira odzozedwa komanso a nkhosa zina kuti adzasangalala kwambiri ngati apitiriza kupirira mavuto awo chifukwa adzalandira moyo wosatha.—Yak. 1:12.

Chaka chatha, anthu 19,241,252 anafika pa Chikumbutso. N’zolimbikitsa kwambiri kuona anthu ochuluka chonchi akulemekeza Yehova ndi Yesu pofika pa mwambo wofunika kwambiriwu. Pa nyengo ya Chikumbutsoyi, Yehova anatamandika kwabasi. Tikutero chifukwa chakuti anthu mamiliyoni anachita upainiya wothandiza m’miyezi ya March ndi April. Zimenezitu  n’zosangalatsa kwambiri. Zinalinso zosangalatsa kumva kuti anthu amene akuchita upainiya wothandiza pa mwezi umene woyang’anira dera akuyendera mpingo wawo akhoza kukhala nawo pa msonkhano wonse wa apainiya. Izi zikuchitika ngakhale kuyenderako kutachitika m’miyezi ina osati March ndi April yokha. Anthu amene akutsogoleredwa ndi nzeru yochokera kwa Mulungu amadziwa ubwino wotanganidwa ndi ntchito yolalikira komanso zinthu zina zokhudza kulambira. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti tisapatutsidwe ndi Mdyerekezi amene akufunitsitsa kufooketsa chikhulupiriro chathu.—1 Akor. 15:58.

Talimbikitsidwanso kwambiri kudziwa kuti chaka chathachi, anthu 277,344 anabatizidwa posonyeza kudzipereka kwa Mulungu. Anthu amenewa ayamba kuyenda panjira yolowera kumoyo limodzi ndi abale ndi alongo awo padziko lonse. (Mat. 7:13, 14) Tiyenera kuthandiza anthu atsopanowa kuti akhale ‘okhazikika m’chikhulupiriro.’ (Akol. 2:7) Tiyeni tipitirize kulimbikitsana kuti tipirire mpaka mapeto. (Mat. 24:13) Paja Malemba amati: “Lankhulani molimbikitsa kwa amtima wachisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.” (1 Ates. 5:14) Pomaliza, tiyeni tonse ‘tizipemphera mosalekeza’ kuti: “Ufumu wanu ubwere.”—1 Ates. 5:17; Mat. 6:10.

Tikudziwa kuti mumakonda Yehova ndipo musangalala ndi Buku lapachaka limeneli. Dziwani kuti timakukondani kwambiri.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova