OLANDIRA ALENDO Amene akulandira alendo ntchito yawo n’kukuthandizani. Choncho, tsatirani malangizo amene angakupatseni okhudza malo oyenera kuimika galimoto ndi njinga, njira zoyenera kuyendamo polowa ndi potuluka pamalo a msonkhano, kusunga malo okhala komanso zinthu zina.

UBATIZO Anthu amene akonzekera kubatizidwa adzakhale m’mipando yakutsogolo imene awakonzera. Ngati pali malangizo ena osiyana ndi amenewa, adzalengezedwa pasadakhale. Anthuwa ayenera kudzakhala m’mipandoyi, Loweruka m’mawa nkhani ya ubatizo isanayambe. Aliyense ayenera kubweretsa chopukutira ndi zovala zoyenera zolowera m’madzi.

ZOPEREKA Pamafunika ndalama zambiri kuti tikhale ndi malo abwino ochitira msonkhano, tikhale ndi zokuzira mawu, zipangizo zoonetsera mavidiyo komanso zinthu zina zothandiza kuti msonkhanowu ukhale wosangalatsa ndiponso utithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndalama zimene mungapereke mwakufuna kwanu pamsonkhanowu, zitithandiza kulipirira zinthu zimenezi komanso zithandiza pa ntchito ya padziko lonse. Mabokosi olembedwa bwino amene mungaponyemo zopereka zanu, aikidwa m’malo osiyanasiyana pamsonkhanowu. Timayamikira kwambiri zopereka zanu, ndipo Bungwe Lolamulira likukuyamikirani chifukwa chothandiza ndi mtima wonse pa ntchito ya Ufumu

DIPATIMENTI YOTHANDIZA PANGOZI Kumbukirani kuti dipatimenti imeneyi imathandiza pa ZAKUGWA MWADZIDZIDZI ZOKHA.

ZOTAYIKA NDI ZOPEZEKA Mukatola chinthu chilichonse, kachiperekeni ku Dipatimenti ya Zotayika ndipo ngati mwataya chilichonse, kafunseni kudipatimentiyi. Mukapeza mwana amene wasochera, kamuperekeni kudipatimenti imeneyi. Komabe dipatimentiyi siyosungirako ana, choncho samalani ana anu ndipo nthawi zonse muzikhala nawo pamodzi.

MALO OKHALA Yesetsani kuganizira ena. Kumbukirani kuti anthu okhawo oyenera kuwasungira malo ndi a m’banja lanu, amene mwabwera nawo pa galimoto imodzi kapena amene mukuphunzira nawo Baibulo. Musaike zinthu pamalo okhala, pokhapokha ngati mwasungira munthu wina malowo.

ANTCHITO ONGODZIPEREKA Ngati mukufuna kuthandiza nawo ntchito zina pamsonkhanowu, pitani ku Dipatimenti Yothandiza Anthu Ndiponso Yoyang’anira Antchito Ongodzipereka.

KUKUMANA NDI OFUNA

SUKULU YA AKHRISTU OLALIKIRA ZA UFUMU Apainiya azaka zapakati pa 23 ndi 65 amene akufuna kuwonjezera utumiki wawo, akuitanidwa kukakhala nawo pamsonkhano wa anthu ofuna kupita ku Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu, Lamlungu masana pa nthawi yopuma. Malo ndi nthawi yake yeniyeni zilengezedwa pasadakhale.

Wokonzedwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova