NJIRA yaikulu imene timagwiritsa ntchito polalikira uthenga wabwino ndi kulalikira kunyumba ndi nyumba. Komabe posachedwapa tinayambanso kugwiritsa ntchito njira ina yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri pogwiritsa ntchito tebulo kapena kashelefu kamatayala. Njirayi ikuthandiza kuti tizilalikira anthu omwe sapezeka pakhomo. (Mat. 24:14) M’mbuyo monsemu abale ndi alongo akhala akugwiritsa ntchito timatebulo, tinyumba tomangidwa ngati timaokala komanso mabenchi, pogawira mabuku athu. Kuwonjezera pamenepa, abale ndi alongo a m’mipingo yosiyanasiyana analandira timashelefu tamatayala pafupifupi 250,000. Kodi zinthu zikuyenda bwanji pogwiritsa ntchito njira yatsopanoyi?

Abale ndi alongo ku Dar es Salaam m’dziko la Tanzania, anayamba kugwiritsa ntchito njira yatsopanoyi m’chaka  cha 2014. Anthu pafupifupi 700 anapempha kuti akufuna munthu woti aziwaphunzitsa Baibulo. Ena mwa anthu amenewa akufika pamisonkhano yathu ndipo ena anayamba kuphunzira. Pa chaka chimodzi chokha, abale ndi alongo m’dzikoli, anagawira mabuku komanso magazini oposa 250,000. Anthu ambiri amene ankatenga mabukuwa ndi a ku Africa komanso kumayiko ena akutali.

Ku Solomon Islands, kuli ofalitsa osapitirira 2,000 ndipo amalalikira anthu a m’zilumba zoposa 300. Popeza abale ndi alongo ali ndi dera lalikulu loti alalikire, njira yatsopanoyi ikuwathandiza kuti azilalikira anthu ochuluka. Mwachitsanzo, mumzinda wa Honiara, womwe ndi likulu la dzikoli, abale anagawira magazini oposa 104,000. Anagawiranso timabuku toposa 23,600 kwa anthu ochokera m’midzi komanso zilumba zakutali kwambiri kumene kulibe wa Mboni ndi mmodzi yemwe. Tsiku lina, abale anagawira mabuku a Baibulo Limaphunzitsa Chiyani okwana 400 masana okha ndipo anthu 60 anapempha munthu woti aziwaphunzitsa Baibulo.

A Michael komanso akazi awo a Linda akuchita upainiya wokhazikika m’dziko la Venezuela. Tsiku lina analawirira kukakonza benchi yomwe amalalikirirapo pamalo ena m’mbali mwa nyanja pachilumba cha Margarita. Kenako kunabwera mnyamata wina dzina lake Aníbal. Mnyamatayu anamugawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Iye anauza banjali kuti bambo ake anamwalira zaka 7 m’mbuyomo, m’mbali mwa nyanjayi. Anafotokozanso kuti kungochokera nthawi imeneyo, mayi ake anayamba kudwala matenda osokonezeka maganizo. Patatha mlungu umodzi, mnyamatayu anabweranso pamalowa ndipo anauza banjali kuti tsikulo ndi limene bambo ake anamwalira. Kenako anatulutsa foni n’kuimbira mayi ake ndipo anapempha a Michael kuti alimbikitse mayi akewo. Kungochokera nthawi imeneyo,  mayiwa amaimbira foni a Michael komanso a Linda ndipo amakambirana malemba olimbikitsa a m’Baibulo. Tsiku lina mnyamatayu analembera banjali meseji. Iye anati: “Zimene mwakhala mukundiuza zandilimbikitsa komanso zandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri zimene Mulungu analonjeza. Mawu anu andithandiza kuti chisoni changa chichepe.”

Abale a ku United States anakonza malo ena apadera okwana 127, m’mizinda 14 kuti azilalikirapo pogwiritsa ntchito njira yatsopanoyi. M’miyezi 7 yoyambirira ya chaka cha utumiki cha 2015, abale ndi alongo anayambitsa maphunziro a Baibulo okwana 8,445. Njirayi ikuthandizanso anthu amene poyamba ankasonkhana nafe kuti abwererenso m’gulu la Yehova. Mwachitsanzo, tsiku lina bambo wina dzina lake Terry ankaona mabuku omwe anali pakashelefu, mumzinda wa Los Angeles ku California. Banja limene linkalalikira pamalowa litaona bamboyu linamufunsa ngati anawerengapo mabuku athu. Bamboyu ananena kuti ndi wa Mboni za Yehova koma anasiya kusonkhana zaka 4 zapitazo. Kenako banjali linamuwerengera lemba la Ezekieli 34:11, n’kukambirana naye. Lembali limati: “Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.” Anamuuzanso za webusaiti komanso TV yathu ya JW Broadcasting. Tsiku lotsatira, bamboyu analembera banjali imelo n’kuwauza kuti asanakumane nawo, anali atangopemphera kuti Mulungu amukhululukire chifukwa chosiya kusonkhana. Anali atapempheranso kuti ayambe kukondanso Mulungu. A Terry anati: “Nditangochita zimenezi m’pamene munkandipatsa moni. Kenako munandiwerengera lemba limene linandithandiza kuti ndibwererenso m’gulu la Yehova. Ndimaona kuti Yehova anayankha pemphero langa.”

Mumzinda wa Addis Ababa ku Ethiopia, muli malo 4 amene anamangidwa mwapadera omwe abale amalalikirapo. Pa miyezi itatu yokha, abale ndi alongo anagawira mabuku komanso magazini 37,275 ndipo anthu 629 anapempha munthu woti aziwaphunzitsa Baibulo. Bambo wina wachikulire analandira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo  atalandira, anayamba kuliwerenga nthawi yomweyo. Bamboyu anafotokoza kuti m’mbuyomo anaphunzirapo za unsembe, komabe ankadzifunsa mafunso ambirimbiri okhudza Yesu komanso Ufumu wa Mulungu. Tsiku lotsatira, bamboyu anapitanso pamalo amene abale amalalikirapo aja kuti akamuthandize kupeza mayankho a mafunso ake. Iye anavomera zoti  aziphunzira Baibulo ndipo kumapeto kwa mlungu womwewo anakasonkhana koyamba ndi a Mboni za Yehova. Panopa akupitirizabe kuphunzira komanso kufika pamisonkhano yathu.

Ethiopia: Mabuku a m’Chiamuhariki pakashelefu kamatayala ku Addis Ababa

Bambo wina wachiyuda ku Mexico anafika pa kashelefu pomwe abale awiri ankalalikira. Bamboyu anapempha abalewa ngati anali ndi buku kapena magazini iliyonse yofotokoza za imfa. Abalewa anamuuza kuti magazini amene ankafunawo anali atatha ndipo anamuuza kuti akhoza kumupatsa magazini yonena zam’tsogolo. Bamboyo anagwira dzanja la m’bale mmodzi n’kumuuza kuti: “Sindikufuna kudziwa zam’tsogolo. Ndikungofuna kudzipha basi.” Kenako anayamba kulira. Ndiyeno abale aja anamufunsa chifukwa chake ankafuna kudzipha. Iye anayankhula kwinaku akulira kuti: “Ndili ndi chisoni kwambiri chifukwa mwana wanga wamwamuna anamwalira.” Abalewo atamva zimenezi anamuonetsa mutu 7 m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kenako anawerenga naye ndime ziwiri pansi pa mutu wakuti, “Mmene Timamvera Wachibale Kapena Mnzathu Akamwalira.” Anamuwerengeranso malemba omwe ali m’bokosi la kumapeto kwa mutuwu, omwe amafotokoza zoti Mulungu adzaukitsa anthu amene anamwalira. Zimene anamvazo zinamusangalatsa kwambiri moti anagwiranso dzanja la m’baleyo n’kumufunsa kuti: “Koma zimenezi n’zoonadi?” Abalewo anamutsimikizira kuti Yehova adzachitadi zimenezi. Ndiyeno bamboyo anawafunsanso kuti: “Kodi ndingatani kuti ndidzaonanenso ndi mwana wanga?” Anapangana naye kuti adzapite kunyumba kwake kuti akayambe kuphunzira Baibulo. Abalewa atapitako, anamupeza akuwadikirira.

Woyang’anira dera wina anathandiza nawo pokonza malo ena oti azilalikirapo pogwiritsa ntchito njira yatsopanoyi ku New York. Iye anati: “Yehova wadalitsa kwambiri njira imeneyi. Njirayi ikuthandiza kuti tizilalikira anthu amene sapezeka pakhomo. Ikuthandizanso anthu amene anasiya kusonkhana komanso amene anachotsedwa omwe ali ngati ‘nkhosa zosochera’ kuti abwererenso m’gulu la Yehova.”—Ezekieli 34:15, 16.