Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Pakufunika Kumanga Nyumba za Ufumu Mofulumira

Pakufunika Kumanga Nyumba za Ufumu Mofulumira

N’ZOSANGALATSA kuona kuti Yehova akutithandiza kwambiri kuti ntchito yathu iziyenda bwino. (Yes. 60:22) Zimenezi zikuchititsanso kuti mipingo ikule kwambiri moti pakufunika Nyumba za Ufumu zochuluka. Mwachitsanzo, padziko lonse lapansi, pakufunika kumanga kapena kukonzanso Nyumba za Ufumu zoposa 13,000.

Kuti ntchitoyi isakhale yoboola m’thumba, Bungwe Lolamulira lasintha mmene limayendetsera zinthu pa nkhani ya zomangamanga. Posachedwapa bungweli linakhazikitsa Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga Padziko Lonse yomwe ili ku likulu lathu ku Brooklyn. Dipatimentiyi ikugwira ntchito mwakhama pokonza njira imene ingathandize kuti ntchitoyi iyende mofulumira komanso kuti abale azisamalira bwino Nyumba za Ufumu zomwe zinamangidwa kale.  Bungwe Lolamulira linakhazikitsanso Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga M’mayiko Angapo. Dipatimentiyi ili ndi maofesi ku Australasia, ku Central Europe, ku South Africa ndiponso ku United States. Abale omwe akugwira ntchito m’dipatimentiyi amayang’anira ntchito ya m’mayiko angapo ndipo amathandiza abale omwe ali m’mayikowo kumanga Nyumba za Ufumu mofulumira koma pogwiritsa ntchito ndalama zochepa. Abale a m’dipatimentiyi amaphunzitsanso abale a ku nthambi za m’mayiko omwe amayang’anira, zimene angachite posamalira ofesi ya nthambi, malo a misonkhano komanso Nyumba za Ufumu. Bungwe Lolamulira linakhazikitsanso Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga m’dziko lililonse. Dipatimentiyi imayang’anira ntchito yomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu komanso malo a misonkhano.

Mu January 2015, akulu onse a ku United States anachita msonkhano ndipo msonkhanowu unalumikizidwa m’madera osiyanasiyana pa vidiyo kudzera pa Intaneti. Pamsonkhanowu panakambidwa nkhani yomwe inafotokoza za kusintha pa nkhani yokonza mapulani, kumanga komanso kusamalira Nyumba za Ufumu. Pamsonkhanowu anakambirana zinthu zotsatirazi.

  • Kumanga: Anakambirana kuti mapulani a Nyumba za Ufumu komanso zinthu zina, azikhala otengera dera limene zizimangidwa. Ananenanso kuti azimanga nyumbazi motsatira malangizo ochokera ku Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku ya Bungwe Lolamulira. Anakambirananso kuti azimanga nyumba zolimba kwambiri ndiponso zokongola, koma azigwiritsa ntchito ndalama zochepa.

  • Kukonza: Anakambirana kuti aziphunzitsa abale oti azisamalira nyumbazi pampingo uliwonse kuti zizigwira ntchito kwa nthawi yaitali.

Monga taonera, pakufunikadi kumanga Nyumba za Ufumu zambiri. Choncho kuti zimenezi zitheke, abale ayenera kuchita zinthu mogwirizana komanso kugwiritsa ntchito bwino ndalama zimene abale amapereka kuti zithandize pomanga nyumbazi.