Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016

Canada: Mudzi wotchedwa Kangirsuk, wa anthu a mtundu wa Inuit chakumpoto kwa dera la Quebec

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Malipoti Apadera—Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana

Malipoti Apadera—Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana

Akuyesetsa Kulalikira Anthu Ambiri a ku Canada

Kavidiyo ka mutu wakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? kanamasuliridwa m’zinenero 8 zomwe anthu a ku Canada amayankhula. Mu October 2014, abale ndi alongo anakalalikira m’dera la Nunavik Arctic kwa masiku 10. Abalewa ankaonetsa kavidiyoka m’chinenero cha Chiinukituti. Anakaonetsa kwa anthu okhala m’madera 14, momwe muli anthu oposa 12,000.

Woyang’anira Sitediyamu Anayamikira a Mboni

Mu September 2014, abale ndi alongo anachita msonkhano wa mayiko musitediyamu ya Sangam, yomwe ili mumzinda wa Seoul ku South Korea. Anthu oposa 56,000 omwe anapezeka pamsonkhanowu anasangalala kwambiri. Woyang’anira sitediyamuyi anayamikira kwambiri a Mboni chifukwa cha zimene anachita pa nthawi ya msonkhanowu. Iye anati: “Aliyense  ankasonyeza khalidwe labwino kwambiri. Anthu ake ndi olimbikira ntchito moti anasesa ndiponso kukolopa sitediyamu yathu kuposa mmene antchito athu amachitira. Ndikanasangalala kwambiri antchito athuwa akanatengera chitsanzo cha a Mboniwa. A Mboni za Yehova amayesetsa kuchita zimene amaphunzira. Zingakhale bwino ngati anthu a m’zipembedzo zinanso atamachita zimenezi.”

South Korea: Msonkhano wa mayiko wa mu 2014 womwe unachitikira mumzinda wa Seoul

Yehova Ndi Amene Anatithandiza

M’mwezi wa May 2012, boma la Sweden, linakana pempho la Mboni za Yehova loti azilandira thandizo la ndalama kuchokera ku boma ngati mmene zilili ndi zipembedzo zina zonse. Choncho Bungwe Lolamulira linapereka chilolezo choti abale akachite apilo nkhaniyi ku khoti lalikulu la m’dzikoli.

Abale atachita apilo, akuluakulu a khotili ananena kuti akufuna kumva kaye maganizo a Mboni za Yehova asanapereke chigamulo  pa mlanduwo. Zimenezi zinachititsa kuti abale ochokera m’mayiko osiyanasiyana akumane n’cholinga choti akambirane mmene angakayankhire mafunso. Abalewa anakumana pa Nyumba ya Ufumu ina mumzinda wa Stockholm kuti akayeserere mmene angakayankhire mafunsowo.

Pamene abalewa ankachita zimenezi, anamva kugogoda pachitseko cha Nyumba ya Ufumuyo. M’bale mmodzi atatsegula chitsekocho anaona atsikana awiri, wina wazaka 13 ndipo wina wazaka 14. Atsikanawa anauza m’baleyo mayina awo ndipo ananena kuti akufuna atafunsa a Mboni za Yehova mafunso angapo. M’baleyu anati: “Ndinkafuna kuwauza kuti adzabwerenso tsiku lina chifukwa pa tsikuli sitikanatha kupeza nthawi yoti n’kucheza nawo bwinobwino.”

Komabe, m’baleyu anaganiza zochezabe ndi atsikanawo omwe anali ndi mafunso ambiri. Mafunso ena anali okhudza zimene a Mboni amachita komanso chifukwa chake savota nawo pachisankho. Atamaliza kucheza nawo, analowanso m’Nyumba ya Ufumuyo ndipo anafotokozera anzake aja mafunso amene atsikanawo anamufunsa komanso mmene anawayankhira.

Abalewo atapita kukhoti tsiku lotsatira, anadabwa kwambiri chifukwa anafunsidwa mafunso ofanana kwambiri ndi amene atsikana aja anawafunsa. M’bale amene ankaimira gulu lathu ananena kuti: “Pamene ankatifunsa mafunsowa, ndinali wodekha ngakhale kuti anthu amene ankatifunsawo anali maloya otchuka kwambiri m’dziko lonse la Sweden. Ndinkaona kuti Yehova anali kumbali yathu ndipo ndi amene anatithandiza pogwiritsa ntchito atsikana aja kuti tisadzavutike kuyankha mafunso m’khoti.”

Chigamulo chimene khoti linapereka pa mlanduwu chinali chotikomera ndipo khotilo linauza boma kuti liyambe kuthandiza a Mboni ngati mmene linkachitira ndi zipembedzo zina zonse.

Ken Anapereka Ndalama Zokwana Kugula Thumba la Mpunga

Kamnyamata kena kazaka 6, dzina lake Ken, kamakhala ku Haiti. Tsiku lina Ken anamva kuti m’dera lakwawo mumangidwa Nyumba ya Ufumu kuti mpingo wawo uzisonkhanamo. Atamva  zimenezi, anaganiza zokhoma kabokosi n’kukabisa kuchipinda kwake kuti azisungiramo ndalama. Ndiye makolo ake akamupatsa ndalama yoti akadyere kusukulu, Ken ankaponya ndalamayo m’kabokosi kaja. Anachita zimenezi mpaka pa nthawi imene anthu omwe anabwera kudzamanga Nyumba ya Ufumu ija anafika. Anthuwo atafika, Ken anatenga kabokosi kaja n’kukapereka kwa omangawo ndipo munali ndalama zokwana kugula thumba lalikulu la mpunga. Abalewo anagwiritsa ntchito ndalamazo pogula thumba la mpunga ndipo anthu omwe ankabwera kudzathandiza ntchito yomanga Nyumba ya Ufumuyi ankadya mpungawo pa nthawi ya chakudya chamasana.

Mkulu wa Asilikali Anatithandiza Kwambiri

Chaka chatha, m’dziko la Sierra Leone munabuka matenda a Ebola. Zimenezi zinachititsa kuti boma liziletsa anthu kupita m’madera onse omwe anakhudzidwa ndi matendawa. Choncho, kuti oyang’anira madera kapena abale otumiza mabuku ndi makalata apite m’maderawa, ankayenera kupempha chilolezo ndipo akavomerezedwa ankapatsidwa baji ndiponso mapepala a galimoto owaloleza kupita m’maderawo. Nawonso abale a m’komiti yopereka chithandizo pakachitika ngozi zadzidzidzi anakwanitsa kutumiza mankhwala, zipangizo zoyezera matenda komanso chakudya m’maderawo. Tikuyamikira kwambiri kuti boma linkapereka zipepala zofunika kuti zimenezi zitheke.

Nthawi ina panachitika zinthu zosangalatsa kwambiri. Abale analemba kalata yopempha kuti apatsidwe mabaji 34 komanso zikalata za magalimoto zokwana 11. Komabe abalewa ankafunika kukumana ndi mkulu wa asilikali kuti avomereze pempho lawolo. Choncho abale awiri ochokera ku ofesi ya nthambi, anapita kukakumana ndi mkulu wa asilikaliyo kuti akatenge mabaji komanso makalata a magalimoto. Atafika kumeneko, anadabwa kuti kalata yopempha kuti awapatse mabaji ndi mapepala a galimoto, sikuoneka. Mkulu wa asilikaliyo anauza abalewo kuti afufuze okha kalatayo pamulu wa makalata, koma sanaipeze. Abalewo ali mkati mofufuza kalatayo, mkulu wa asilikaliyo anauza sekilitale wake kuti akutseka ofesiyo ndipo anamuuza  kuti asalandirenso makalata opempha mabaji mpaka patadutsa milungu iwiri. Abalewo atamva zimenezi, nthawi yomweyo anayamba kupemphera chamumtima kuti Yehova awathandize. Ndiyeno mkulu wa asilikaliyo anayang’ana abalewo n’kuwafunsa kuti: “Kodi mukufuna mabaji komanso zikalata zagalimoto zingati?” Mkulu wa asilikaliyo atamva zimene abalewo ananena, ananyamuka pampando umene anakhala n’kufunsa modabwa kuti: “Onsewo ndi a chiyani?”

Abalewo anamufotokozera ntchito imene ankafuna kukagwira komanso mmene zinthu zimene akapereke m’deralo zikathandizire anthu. Mkulu wa asilikaliyo anakhala kaye phee, ndipo kenako anauza sekilitale wake uja kuti: “Uwapatse chilichonse chimene angafune.”

Guinea and Sierra Leone: Akusamba m’manja pa Nyumba ya Ufumu