Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi

Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi

LOWERUKA pa 24 January, 2015, ku Madagascar kunachitika mwambo wotsegulira ofesi ya nthambi. Anthu amene anapezeka pamwambowu anasangalala kwambiri moti mlongo wina ananena kuti: “Ndikusowa chonena chifukwa cha chisangalalo.” Mlongoyu komanso alendo ena okwana 583, anasangalala kwambiri kuona nyumba yatsopano yazipinda 19, khitchini yomwe anaikonzanso komanso malo odyera omwe anawakulitsa. Panthambiyi panamangidwanso maofesi owonjezera a Dipatimenti ya Utumiki, Dipatimenti Yoona za Ndalama komanso Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga. Anamanganso masitudiyo atsopano a Dipatimenti Yojambula Mavidiyo ndi Zinthu Zongomvetsera komanso dipatimenti yomasulira mabuku a chinenero chamanja. Panakhazikitsidwanso Dipatimenti Yosindikiza Mabuku a Anthu Omwe Ali ndi Vuto Losaona. Pamwambowu panakambidwa nkhani yomwe inafotokoza mmene ntchito yathu inayambira ku Madagascar. Nkhaniyi itatha, M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yapadera yopatulira maofesiwo.

Nyumba yogona, ya zipinda 19, pa ofesi ya nthambi, ku Madagascar

 Mumzinda wa Jakarta ku Indonesia munasefukira madzi, kutatsala masiku ochepa kuti mwambo wopatulira ofesi ya nthambi uchitike. Komabe, mitima ya abale ndi alongo inakhala pansi chifukwa pamene tsikuli linkafika, madzi osefukirawo anali ataphwera. Mwambowu unachitika pa 14 February, 2015, ndipo M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira, ndi amene anakamba nkhani yopatulira maofesiwa. Ofesi ya nthambi yatsopanoyi ili m’nyumba ina yosanjikizana ndipo ili pansanjika ya nambala 14. Maofesi ena ali m’nsanjika zina 12 za m’nyumba ina yapafupi. Madipatimenti ena a pa Beteli ali m’nyumba zina zing’onozing’ono zomwe zili pafupi. Tsiku lotsatira, M’bale Morris anakamba nkhani pabwalo lina lamasewera. Nkhaniyo inali ndi mutu wakuti, ‘Pitirizanibe Kupirira M’ntchito Yabwino.’ Anthu okwana 15,257 anamvetsera nkhaniyi pabwaloli. Enanso okwana 11,189, anamvetsera nkhaniyi ali m’madera ena okwana 41 kudzera pa Intaneti. Palibenso msonkhano wina womwe panasonkhana anthu ochuluka chonchi ku Indonesia. M’bale Ronald Jacka, yemwe ndi mmodzi wa amishonale oyambirira kufika m’dziko la Indonesia anati: “Pamene ndinkafika ku Indonesia mu 1951, kunali a Mboni okwana 26 okha. Koma taonani pamsonkhano wapaderawu tasonkhana anthu oposa 26,000. Umenewu ndi umboni woti Yehova akudalitsa kwambiri ntchito yathu kuno ku Indonesia.”