Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016

Russia: Akulalikira mumzinda wa Moscow

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Lipoti la Milandu

Lipoti la Milandu

Kulembetsa ku Boma

Sikuti a Mboni za Yehovafe timafunika kuchita kulembetsa ku boma kuti tizilalikira komanso tizisonkhana. Komabe, kulembetsa ku boma kumatithandiza kuti tizitha kugula malo ndiponso nyumba zochitira misonkhano. Kumatithandizanso kuti tizitha kuitanitsa mabuku athu kuchokera m’mayiko ena.

 • Mu 2004, makhoti a ku Russia anasiya kuona kuti a Mboni za Yehova ndi gulu lovomerezeka ndi boma mumzinda wa Moscow. Zimenezi zinachititsa kuti abale ndi alongo azikumana ndi mavuto ambiri. Apolisi anayamba kuwachitira zachipongwe ndipo anthu ena anayamba kuwamenya akamalalikira. Kuwonjezera pamenepo, eni ake a nyumba zimene abale ankachita lendi kuti azisonkhanamo, anawauza kuti asamuke. Zimenezi zinachititsa kuti abalewo azisowa malo osonkhana. Ataona zimenezi anakasuma ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. M’chaka cha 2010, khotili linagamula  kuti dziko la Russia linaphwanya ufulu wa a Mboni za Yehova a ku Moscow ndipo linalamula dziko la Russia kuti livomerezenso chipembedzo cha Mboni za Yehova. Ndife osangalala kukudziwitsani kuti pa 27 May, 2015, nthambi yoona zachilungamo ku Moscow, inalemba m’kaundula wake kuti yavomereza chipembedzo chatsopano cha Mboni za Yehova ku Moscow.

Kukhoma Misonkho

Mabungwe amene a Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito sayenera kulipira misonkho ku boma. Zimenezi ndi zofanananso ndi mmene zimakhalira ndi zipembedzo zina komanso mabungwe othandiza anthu. Komabe, mayiko ena amafuna kuti tizilipira msonkho ngati mmene amachitira makampani a bizinezi.

 • Ku Sweden, akuluakulu a boma ankaona kuti ofesi ya nthambi imachita bizinezi ndipo ankati imalemba abale ndi alongo ntchito. Akuluakuluwa ankatsutsa zoti abale a ku ofesi ya nthambiwo ndi ongodzipereka ndiponso kuti a Mboni za Yehova ndi gulu lachipembedzo. Chifukwa cha zimenezi, akuluakuluwo anati ofesi ya nthambiyo iyenera kumalipira msonkho ngati mmene amachitira makampani ena omwe amalemba anthu ntchito. Ananenanso kuti abale amene amatumikira pabetelipo aziwadula msonkho pa ndalama zochepa zimene amawapatsa. Pofuna kuthana ndi vutoli, abale a ku Sweden anaganiza zokasuma nkhaniyi ku khoti, moti analemba makalata 6 n’kuwatumiza ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

Kusalowerera Ndale Komanso Kusalowa Usilikali pa Chifukwa cha Chikumbumtima

A Mboni za Yehova amaona kuti n’zofunika kwambiri kumvera lamulo la m’Baibulo lakuti ‘asule malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo,’ ndiponso kuti ‘asamaphunzire nkhondo.’ (Yes. 2:4) Choncho kaya zivute zitani, salola kumenya nawo nkhondo kapena kugwira nawo ntchito zokhudzana ndi usilikali.

 • Malamulo a dziko la South Korea salola munthu kukhala ndi ufulu wokana kumenya nawo nkhondo. Kwa zaka zoposa 60 zapitazi, abale oposa 18,000, anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Pafupifupi wa Mboni aliyense m’dzikoli, ali ndi wachibale kapena mnzake amene anamangidwapo chifukwa chokana kulowa usilikali. Mu 2004 ndi mu 2011, Khoti Loona za Malamulo a Dziko  la South Korea linanena kuti malamulo a dzikolo amavomereza kumanga munthu ngati akukana kulowa usilikali. Koma mu July 2015, khotilo linafuna kumva maganizo a anthu kuti lione ngati pakufunika kukonzanso lamuloli. A Mboni za Yehova padziko lonse akupempherera nkhaniyi ndipo akuona kuti boma la South Korea lisiya kumanga abale achinyamata chifukwa choti akana kulowa usilikali pa zifukwa zachikumbumtima.

 • Abale atatu a ku Eritrea akhala m’ndende kwa zaka 21, ndipo panopa ayamba chaka cha 22. Abalewa anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Mayina a abalewa ndi Paulos Eyassu, Negede Teklemariam komanso Isaac Mogos. Boma la dzikoli silinazengebe mlandu wawo komanso siliwapatsa mwayi woti akadziteteze kukhoti. Kuwonjezera pa abalewa, palinso abale ndi alongo ena oposa 50, omwe akupitirizabe kukhala okhulupirika ngakhale kuti akuzunzidwa komanso akukhala m’ndende zoipa kwambiri. Tikukhulupirira kuti Yehova ‘amamva kuusa moyo’ kwa atumiki ake amene anamangidwa chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira. Sitikukayikira kuti apitirizabe kuwathandiza.—Sal. 79:11.

 • M’bale wina wa ku Ukraine, dzina lake Vitaliy Shalaiko, anauzidwa kuti akayambe usilikali m’mwezi wa August 2014. M’baleyu anakana kukayamba usilikaliwo chifukwa cha zimene amakhulupirira, ndipo ananena kuti akhoza kugwira ntchito iliyonse yosakhudzana ndi usilikali. Loya wa boma pa mlanduwu, anauza M’bale Shalaiko  kuti ndi wolakwa chifukwa anakana kupita ku usilikali, koma khoti linapeza kuti m’baleyu ndi wosalakwa. Khotili linanena kuti si bwino kuphwanya ufulu wa anthu pongofuna kukhwimitsa chitetezo cha m’dziko. Linanenanso kuti “n’kulakwa kumanga munthu chifukwa choti wakana kulowa usilikali pa zifukwa zachipembedzo.” Loya woimira boma uja anachitanso apilo mlanduwu kukhoti lalikulu. Ndiyeno pa 23 June, 2015, khotilo linagwirizana ndi zimene makhoti aang’ono anagamula zoti a Vitaliy Shalaiko ndi osalakwa. Khotili linanenanso kuti, ngakhale zitakhala kuti pakufunika asilikali ambiri, munthu ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali komanso wosankha kugwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali.

Ukraine: M’bale Vitaliy Shalaiko akulalikira

M’bale Shalaiko anasangalala kwambiri ndi zimene khotili linagamula moti anati: “Ndinalimbikitsidwa kwambiri ndi zimene lemba la Yeremiya 1:19 limanena. Chinthu chofunika kwambiri kwa ine chinali kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova, moti ndinali wokonzeka ngakhale kupita kundende. Ndimadziwa kuti Yehova sadzandisiya komanso kuti apitirizabe kundithandiza kukhalabe wokhulupirika. Zinandidabwitsa kuti makhoti onse atatu anagamula kuti ndine wosalakwa. Ndikuthokozanso kuti abale ndi alongo anandithandiza kwambiri pa nthawi imene mlanduwu unkaweruzidwa, moti sindinkadziona kuti ndili ndekhandekha.”

Nyimbo ya Fuko Komanso Kuchitira Sailuti Mbendera

Akhristufe sitichita nawo miyambo yosonyeza kukonda dziko lathu ndipo zimenezi zimachititsa kuti anthu azidana nafe. Mwachitsanzo, ana ambiri omwe ali pasukulu amakakamizidwa ndi aphunzitsi awo kuti aimbe nyimbo ya fuko komanso kuti achitire sailuti mbendera.

 • Mumzinda wa Karongi ku Rwanda, akuluakulu a pasukulu ina anachotsa ana a Mboni za Yehova sukulu ndipo anawo anamangidwa. Iwo ankanena kuti anawo ndi amwano komanso salemekeza nyimbo ya fuko chifukwa ankakana kuimba nawo nyimboyo. Ndiyeno pa 28 November, 2014, khoti la mumzindawo linaweruza mlanduwu ndipo linagamula kuti anawo ndi osalakwa. Linanenanso kuti kukana kuimba nawo nyimbo ya fuko sikutanthauza kuti anawo ndi amwano. Ana a Mboni a m’mayiko monga Cameroon, Democratic Republic of Congo, Equatorial Guinea, komanso Malawi, akukumananso ndi vuto lomweli ndipo nthawi zina amachotsedwa sukulu. Abale athu m’mayiko amenewa akuyesetsa kukambirana ndi akuluakulu  a boma komanso aphunzitsi kuti asamachotse ana a Mboni za Yehova sukulu chifukwa chokana kuimba nyimbo yafuko kapena kuchitira sailuti mbendera.

 • Honduras: Mirna Paz ndi Bessy Serrano analandira masatifiketi awo

  Mu December 2013, sukulu ina ya m’dera la Lepaera m’dziko la Honduras, inakana kupereka masatifiketi kwa ana awiri a Mboni za Yehova. Sukuluyi inachita zimenezi chifukwa anawo anakana kuimba nyimbo ya fuko komanso kuchitira sailuti mbendera. Pofuna kuthana ndi vutoli, maloya awiri, omwenso ndi a Mboni za Yehova, anapita kukakumana ndi mkulu wina wa ku unduna wa zamaphunziro. Abalewa anaonetsa mkuluyo zikalata za m’mayiko ena zosonyeza kuti mayikowo analola kuti ana a Mboni asamaimbe nawo nyimbo ya fuko komanso kuchitira sailuti mbendera. Mkuluyo ankaoneka kuti ndi wachifundo ndipo ananena kuti akhoza kulola kuti ana a Mboni komanso makolo alembe madandaulo awo n’kuwatumiza ku undunawo. Mkuluyo atawerenga makalatawo, pa 29 July , 2014, analamula kuti “aliyense ali ndi ufulu wolandira maphunziro mosayang’ana nkhope.” Analamulanso kuti ana a Mboni, omwe anakanizidwa kulandira masatifiketi aja, apatsidwe masatifiketi awo.

Kuopsezedwa ndi Akuluakulu a Boma

A Mboni za Yehovafe timamvera lamulo la Yesu loti tizilalikira uthenga wabwino kwa ena, tizisonkhana ndi abale athu komanso tiziphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse. Timamveranso zimene Baibulo  limanena zoti tiziphunzitsa ana athu malamulo a Yehova komanso kuti ‘tizipewa . . . magazi.’ (Mac. 15:20; Deut. 6:5-7) Koma tikamachita zimenezi, timakumana ndi mavuto ena. Mwachitsanzo, akuluakulu a boma samvetsa kuti n’chifukwa chiyani timachita zimenezi.

 • M’chigawo cha Florida ku United States, woweruza milandu anagamula kuti mayi wina yemwe sanali wa Mboni, ndi amene ali ndi udindo wolera ana ake atatu komanso kuwaphunzitsa zinthu zokhudza chipembedzo. Koma khotilo linauza bambo wa anawo yemwe anali wa Mboni kuti asamawaphunzitse zinthu zotsutsana ndi chipembedzo cha Katolika chimene mayiyo ankapita. M’baleyo atamva zimenezi anakapanga apilo ku khoti lina ndipo pa 18 August, 2014, khotilo linagamula zosiyana ndi zimene woweruza woyamba uja anagamula. Khotili linanena kuti: “Malamulo onena kuti kholo limene silikusunga anawo lilibe udindo wophunzitsa ana ake zinthu zokhudza chipembedzo, siligwira ntchito ngati palibe umboni wosonyeza kuti zimene khololo likuphunzitsa anawo ziwasokoneza.”

  Zimene khotili linagamula zinathandiza kuti anawo aziphunzitsidwa mfundo za Yehova zomwe zingawathandize kwambiri. Panopa bamboyo akupitirizabe kuphunzitsa ana akewo ndiponso amapita nawo kumisonkhano. M’baleyu anati: “Kupirira vuto limeneli kwalimbitsa chikhulupiriro changa. Ngakhale kuti ndakumana ndi mavuto ambiri pakatipa, Yehova wandithandiza kuti ndisafooke. Ndimadziwa kuti munthu akadzipereka kwa Yehova amayenera kukumana ndi mavuto.”

 • Namibia: Mlongo Efigenia Semente ali ndi ana ake atatu

  Mlongo wina wa ku Namibia, dzina lake Efigenia Semente, ali ndi ana atatu. Pa nthawi imene ankabereka mwana wachitatu, anataya magazi ambiri moti madokotala komanso achibale ake omwe si Mboni, anakatenga chilolezo kukhoti choti mlongoyu aikidwe magazi. Mlongoyu atadziwa zimenezi anakana kuikidwa magazi ndipo anakasuma kukhoti n’cholinga choti madokotala amupatse chithandizo chimene iyeyo ankafuna. Pa 24 June, 2015, khoti lalikulu la ku Namibia linapereka chigamulo chokomera mlongoyu. Khotilo linati: “Aliyense ali ndi ufulu wosankha kulandira kapena kukana chithandizo cha mankhwala chimene madokotala akufuna kumupatsa. Ngakhale makolo kapena achibale alibe ufulu wosankhira m’bale wawo chithandizo cha mankhwala.” Mlanduwu utatha, Mlongo Semente ananena kuti: “Pa nthawi imeneyi m’pamene ndinaona kuti Yehova  akundithandiza kwambiri. Ndimasangalala kukhala m’gulu lake ndipo ndimaona kuti amatisamaliradi.”

 • Abale ndi alongo a ku Switzerland akhala akusangalala kulalikira m’misewu ya m’mizinda ikuluikulu pogwiritsa ntchito njira yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri. Komabe, akuluakulu a mzinda wa Geneva analetsa kulalikira pogwiritsa ntchito “timashelefu kapena masitandi pofalitsa uthenga wokhudza chipembedzo m’malo opezeka anthu ambiri.” Abale anakasuma nkhaniyi kukhoti, ndipo anauza khotilo kuti kuletsa anthu kulalikira pogwiritsa ntchito kashelefu kapena sitandi “n’kuphwanya ufulu wachipembedzo komanso ufulu woti munthu azifotokoza maganizo ake momasuka.” Khotilo linagwirizana ndi zimenezi ndipo linalola a Mboni kumalalikira pogwiritsa ntchito njirayi. Abale anakambirana ndi akuluakulu a boma ndipo anawalola kuti akhazitse malo oti azilalikira pogwiritsa ntchito njirayi.

 • Akuluakulu a boma la Azerbaijan akuchita chilichonse chotheka kuti aletse ntchito ya a Mboni za Yehova m’dzikoli. Nthawi zambiri unduna woona zachitetezo, umaitanitsa abale ndi alongo kuti ukawafunse mafunso. Undunawu umafufuzanso m’nyumba za abale kuti uone ngati abalewo akusunga mabuku osavomerezeka ndi boma ochokera m’mayiko ena. Anthu a m’mayiko ena anakhudzidwa  kwambiri boma litamanga azimayi awiri a Mboni za Yehova chifukwa chouza anzawo zimene amakhulupirira. Alongowa anamangidwa m’mwezi wa February 2015 ndipo mayina awo ndi a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova. Ngakhale kuti zimenezi ndi zokhumudwitsa, ndife osangalala kukudziwitsani kuti abale ndi alongo a ku Azerbaijan akupitirizabe kulengeza “uthenga wabwino wa Ufumu” mwakhama komanso mopanda mantha.—Mat. 24:14.

 • Boma la dziko la Russia likupitirizabe kuletsa ntchito ya a Mboni za Yehova m’dzikolo. Pofika pano, bomali laletsa mabuku komanso zinthu zina zokwana 80 ndipo limanena kuti mabukuwa ndi oopsa kwambiri pa chitetezo cha dzikolo. Zimenezi zikutanthauza kuti kugawira komanso kusindikiza mabuku monga, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, n’kosaloleka. Kuwonjezera pamenepa, m’mwezi wa December 2014, khoti lalikulu la m’dzikoli linanena kuti webusaiti yathu ya jw.org ikuwopseza chitetezo cha dzikolo. Nawonso makampani a Intaneti anapanga zoti anthu asamathe kulowa pawebusaitiyi ndipo kulimbikitsa anthu kuti azilowa pawebusaitiyi, ndi mlandu. Kuyambira mu March 2015, anthu amene amayang’anira za katundu wolowa ndi wotuluka m’dzikoli, analetsa kuti mabuku athu asamalowe m’dzikoli. Anthuwa amakanizanso kulowetsa m’dzikoli ngakhale Mabaibulo komanso mabuku ena amene khoti linanena kuti si oopsa.

Abale ndi alongo okwana 16 a ku Taganrog, anamangidwa chifukwa chokonza komanso kuchita msonkhano wachipembedzo. Ndipo mumzinda wa Samara, akuluakulu a boma anakatenga chilolezo kukhoti ndi cholinga choti a Mboni za Yehova asamaonedwe ngati chipembedzo chovomerezeka m’dzikoli. Iwo anachita zimenezi ponena kuti a Mboni za Yehova ndi gulu loopsa. Ngakhale kuti akukumana ndi mavuto amenewa, abale ndi alongo a ku Russia salola kuti mavutowo awalepheretse kupereka zinthu “za Mulungu, kwa Mulungu.”—Mat. 22:21.