Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Baibulo la Dziko Lapansi Latsopano Lamasuliridwa M’zinenero Zinanso Zambiri

Baibulo la Dziko Lapansi Latsopano Lamasuliridwa M’zinenero Zinanso Zambiri

POFIKA pa 31 August 2015, Baibulo la Dziko Lapansi Latsopano linali litamasuliridwa lonse kapena mbali yake m’zinenero 129. Baibuloli likupezekanso pawebusaiti yathu ya jw.org m’zinenero zonse zimene lamasuliridwazi, kuphatizapo zinenero zamanja zokwana 7. Mwachitsanzo m’chaka cha utumiki cha 2015 chokha, Baibuloli linamasuliridwa m’zinenero zotsatirazi.