Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Australia: Akuonetsa kavidiyo kachingelezi ka zithunzi zamakatuni ka mutu wakuti, What’s a Real Friend?

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Oceania

Oceania
  • MAYIKO 29

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 40,642,855

  • OFALITSA 98,353

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 66,022

Yehova Anamuthandiza Kuti Alimbe Mtima

Kamtsikana kena ka zaka 12, dzina lake Emily, kamakhala m’dziko la Australia. Tsiku lina aphunzitsi ake ankawaphunzitsa kufunika kosankha bwino anthu ocheza nawo. Emily atamva zimenezi, analimba mtima n’kuonetsa aphunzitsi akewo vidiyo yachingelezi ya zithunzi za makatuni ya mutu wakuti, What’s a Real Friend? Kenako aphunzitsiwo anaonetsa vidiyoyo kalasi yonse ndipo ana onse ankaonera mwachidwi. Atamaliza kuonera, anakambirana kwa ola  lathunthu zimene anaona m’vidiyoyi. Aphunzitsiwo anaonetsanso vidiyoyi m’makalasi ena angapo. Ndiye tsiku lina kamtsikanaka kanauza aphunzitsi ake aja komanso ana a m’kalasi yake za webusaiti yathu ya jw.org. Emily anati: “Yehova anandithandiza kuti ndilimbe mtima kuuza anzanga a kusukulu za webusaiti yathu.”

Anakalalikira Kudera Lakutali Pamalo Ochitira Zionetsero Zamalonda

Ofalitsa okwana 5 a ku Timor-Leste, anayenda ulendo wa maola 9 kuti akalalikire mumzinda wa Suai, komwe kunkachitika zionetsero zamalonda. Ofalitsawa anadutsa m’misewu yovuta kwambiri ya m’mapiri. Atafika mumzindawu, anakonza malo ena n’kuikapo mabuku athu. Anthu amene anabwera kuzionetsero zamalondazo, anadabwa kwambiri kuona mabuku ofotokoza Baibulo a m’zinenero 12 zomwe zimayankhulidwa m’deralo. Anachita chidwi chifukwa pali mabuku ochepa omwe amapezeka m’zinenerozi ndipo zinenero zina zilibe n’komwe mabuku omwe anasindikizidwapo. Mayi wina ataona mutu wa kabuku kathu kena, anati: “Taonani kabuku ka m’chinenero chathu!” Aka kanali koyamba kuti mayiyu awerenge kabuku ka m’chinenero chake cha Chibunaki. Kwa masiku 4 okha, ofalitsawo anagawira mabuku okwana 4,571 ndipo anthu ambiri anawauza kuti akufuna munthu woti aziwaphunzitsa Baibulo kunyumba kwawo. Ambiri mwa anthuwa anali asanakumanepo ndi a Mboni za Yehova. Ana nawonso anaonera mavidiyo a Khalani Bwenzi la Yehova a m’chinenero cha Chitetani Dili. Ena mwa ana amenewa analoweza nyimbo za m’mavidiyowa moti ankaimba nawo mosangalala.

Timor-Leste: Ana akuonera mavidiyo a Khalani Bwenzi la Yehova

 “Ana a Sukulu Akufunikira Mabuku Ngati Amenewa”

M’bale Brian ndi Mlongo Roxanne, amachita umishonale pachilumba cha Palau. Tsiku lina banjali linaganiza zopempha chilolezo choti lizilalikira pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala pakoleji ina ya pachilumbachi. Ndiye anakumana ndi mkulu wina woyang’anira pakolejiyo n’kumuonetsa vidiyo yathu pa jw.org, yosonyeza abale akulalikira pamalo opezeka anthu ambiri. Anapatsanso mkuluyo ena mwa mabuku omwe ankafuna kuti azidzaika pakashelefu kolalikirira. Mkuluyo anauza  banjali kuti likakumane ndi munthu wina yemwe amayang’anira nkhani zokhudza ana a sukulu. Atafika kumeneko, munthuyo anawauzanso kuti akakumane ndi munthu winanso waudindo pakolejiyo.

M’bale Brian anati: “Munthu wachitatuyu anatilandira bwino ndipo tinamufotokozera zimene tinkafuna. Koma munthuyo anatiuzanso kuti tibwerere kwa mkulu woyang’anira koleji uja. Titafika kwa mkuluyo, anatiuza kuti tilembe kalata yopempha chilolezo choti tizilalikira pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala. Tinayamba kuona kuti anthuwo sakufuna kutithandiza chifukwa ankangotiyendetsa, moti zinatifooketsa kwambiri. Koma tinaganiza zongolembabe kalatayo.”

Palau: M’bale Brian ndi Mlongo Roxanne akulalikira ophunzira pakoleji pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala

 Kenako banjali linalemba kalatayo ndipo patapita masiku angapo, anapitakonso kuti akamve kuti zili pati. Komabe ankakayikira ngati angawalole kuti azilalikira pasukulupo. M’bale Brian ananena kuti: “Tinadabwa kwambiri munthuyo atatiuza kuti wawerenga mabuku omwe tinasiya aja ndipo akuona kuti ndi abwino kwambiri. Iye anatiuza kuti: ‘Ana a sukulu akufunikira mabuku ngati amenewa.’” Pomaliza akuluakulu a pasukulupo anawaloleza kumalalikira pasukulupo.

M’bale Brian ananenanso kuti: “Munthu amene ankayang’anira nkhani zokhudza ana a sukulu uja, anatiuza kuti Lamlungu lililonse, galimoto ya pakolejipo izinyamula ophunzira amene amagonera pakolejipo n’kukawatula kutchalitchi chilichonse chimene akufuna. Anatiuzanso kuti: ‘Ngati ana a sukulu atafuna kuti azipita kutchalitchi chanu, tikhozanso kumakawasiya.’ Zimene anatiuzazi zinatidabwitsa kwambiri. Poyamba tinkaganiza kuti atikaniza, koma anatiloleza ndipo anatiuzanso kuti azinyamula ophunzira n’kuwapititsa ku Nyumba ya Ufumu.”

Tsiku loyamba limene banjali linalalikira pakolejiyo pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala, linagawira mabuku 65, magazini 8 komanso timabuku 11. Linachezanso ndi ophunzira ambiri omwe anasonyeza chidwi. Akuluakulu a pakoleji aja anauza banjali kuti lizibwerabwera kudzalalikira pasukuluyo.

Ogula Malonda Anaonera Mavidiyo Athu

Tsiku lina M’bale Lipson, yemwe amatumikira pa ofesi ya nthambi ya ku Solomon Islands anapita kukalalikira. Chakumasana akubwerera ku ofesi ya nthambi, anamva nyimbo ya Ufumu ikuimbidwa m’sitolo ina. M’baleyu anadabwa kwambiri ndi zimenezi moti anaganiza zolowa m’sitoloyo. Atangolowa anaona ana komanso akuluakulu akuonera kavidiyo kanyimbo nambala 55 ya mutu wakuti, “Tidzapeza Moyo Wosatha!” Nyimboyi ili m’kavidiyo kena kamene kanatuluka m’timavidiyo tokhala ndi mutu wakuti, Khalani Bwenzi la Yehova. Nyimboyi itatha, mwiniwake wa sitoloyo anauza anthuwo kuti, “Ndilinso ndi kavidiyo kena kamene ndikufuna kukuonetsani.” Kenako anaika kavidiyo ka makatuni ka mutu wakuti, Kuba N’koipa. Kavidiyoka katatha, mwini sitoloyo anauza anthuwo kuti asabe katundu wa m’sitolo yakeyo.

 Anthu ambiri analowa m’sitoloyo pa nthawi imene mwiniwake ankaonetsa kavidiyo. Kenako anauza anthuwo kuti: “Tsopano ndikufuna kuti mumvetsere nyimbo imene ndimaikonda kwambiri.” Ndiyeno anaikanso nyimbo nambala 55 ija. Itatha, mwini sitoloyo anaikanso vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? komanso yakuti, Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? Mavidiyowa anali a chinenero cha Chipijini cha ku Solomon Islands.

Solomon Islands: A store owner enjoys showing videos from jw.org to shoppers

Anthu ambiri a ku Solomon Islands sagwiritsa ntchito Intaneti chifukwa ndi yodula kwambiri. Koma mwini sitoloyu, yemwe si wa Mboni, akuthandiza kwambiri kuti anthu a m’dera lake adziwe Yehova, poonetsa mavidiyo athu kwa anthu amene amabwera m’sitolo yake.

Anapeza Dzina la Mulungu M’buku Lathu

Banja lina limakonda kulalikira Lolemba lililonse pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala m’tauni ya Nouméa, yomwe ndi likulu la dziko la New Caledonia. Tsiku lina akulalikira, mayi wina  wamanyazi anafika pa kashelefu kawo. Mayiyu sananene chilichonse, koma anangotenga buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? n’kumapita. Patatha maminitsi 30, mayiyu anabweranso buku lija lili m’manja. Ndiye anafunsa banjalo kuti, “Kodi munalionapo dzina ili?” Kenako anatsegula bukulo n’kuwaonetsa pamene panali dzina la Yehova. Ndiyeno anati: “Ilitu ndiye dzina la Mulungu.” Anapitiriza kunena kuti: “Kwa milungu ingapo, ndakhala ndikufufuza kulaibulale kuti ndidziwe zambiri za Mulungu. Koma nditatenga bukuli, n’kulowa m’galimoto, chinthu choyamba chimene ndinaona nditalitsegula, ndi dzina la Mulungu lakuti, Yehova. N’chifukwa chake ndabweranso kuti ndidzakuthokozeni.” Banjalo linacheza ndi mayiyu ndipo linamuonetsa zakumapeto kwa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pamutu wakuti, “Tanthauzo la Dzina la Mulungu Ndiponso Mmene Tingaligwiritsire Ntchito.” Mayiyo anafotokoza kuti wasintha maganizo. Anati, m’malo moti azikafufuza kulaibulale zokhudza Mulungu, azibwera pamene banjali limalalikira Lolemba lililonse.