• MAYIKO 57

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 982,501,976

  • OFALITSA 4,102,272

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 4,345,532

Ankapita Kumunda Kukaphunzira Baibulo Usiku

Banja lina, lomwe likuchita upainiya wapadera, linapita kukalalikira kumudzi wina umene sulalikidwa kawirikawiri, womwe uli m’dziko la Brazil. Ali kumeneko anamva za mayi wina, dzina lake Valdira, yemwe m’mbuyomo anaphunzirapo Baibulo kwa zaka 13. Kuti akumane ndi mayiyu, apainiyawa anayenda m’misewu yafumbi komanso anawoloka mitsinje yoopsa kwambiri. Kenako anafika kumene mayiyu ankakhala. Mayi Valdira ankafunitsitsa atayambiranso kuphunzira Baibulo. Koma chifukwa choti ankakhala kutali kwambiri,  apainiyawo sakanakwanitsa kuphunzira naye. Popeza mayiyu anali ndi foni, apainiyawo anakonza zoti aziphunzira naye kudzera pafoniyo. Komabe, netiweki inkavuta kwambiri m’dera limene mayiyu ankakhala, moti panali malo amodzi okha omwe netiwekiyo inkagwira. Malowa anali kumunda, komwenso kunali kutali kwambiri ndi nyumba yake. Panali vuto linanso chifukwa mayiyu akanatha kuphunzira kuyambira 9 koloko usiku basi. Ndiye tayerekezani kuti mukumuona mayiyu ali yekhayekha m’munda usiku, akuphunzira Baibulo pafoni, atayatsa kandulo.

Mayi Valdira amamvetseranso misonkhano ya Lamlungu pafoni yake yomweyo. Amapita kumunda kuja ndi Baibulo, Nsanja ya Olonda komanso nyimbo. Kukamagwa mvula, mayiyu amapitabe kumundako atafunda ambulera wake.

M’mwezi wa March, Mayi Valdira anayenda ulendo wa makilomita pafupifupi 97 kupita ku Nyumba ya Ufumu kuti akachite nawo msonkhano wapadera. Pamsonkhanowu panatulutsidwa Baibulo la Dziko Latsopano la Chipwitikizi, lomwe analikonzanso. Mayiyu anasangalala kwambiri atalandira Baibulo lake. Nthawi ina abale ndi alongo ena atamva za khama limene mayiyu amachita kuti aphunzire Baibulo, anamuyamikira kwambiri. Koma Mayi Valdira anati: “Komatu n’zosavuta, aliyense akhoza kukwanitsa.”

“Ndinkadziwa Kuti Tsiku Lina Mudzabwera”

Tsiku lina mpainiya wina wapadera, dzina lake Frank, anakonza ulendo wokalalikira anthu a mtundu wa Yukpa omwe amakhala m’mudzi wina wa m’dziko la Colombia. Asananyamuke, anthu ena anamuchenjeza kuti mfumu ya m’mudziwo ndi yovuta kwambiri. Ananena kuti mfumuyo dzina lake ndi John Jairo, ndipo inathamangitsapo magulu a zipembedzo zina zachikhristu, omwe ankafuna kulalikira m’mudzi wake. Anamuuzanso kuti tsiku lina mfumuyi itamva zoti m’busa wina akumauza anthu kuti amupatse chakhumi, inapsa mtima kwambiri. Kenako mfumuyo inayamba kuthamangitsa m’busayo kwinaku ikuwombera m’mwamba ndi mfuti, moti m’busayo analiyatsa liwiro la mtondo wadooka.

Colombia: M’bale Frank, yemwe ndi mpainiya wapadera, akuphunzira Baibulo ndi gulu lina la anthu a mtundu wa Yukpa

M’bale Frank anati: “Titafika m’mudziwo, munthu woyamba amene tinamulalikira anali mwana wina wamkazi wa mfumuyo. Tinaonetsa mtsikanayo buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa  Chiyani Kwenikweni? ndipo kenako ananena kuti, ‘Ndimafuna nditalowa chipembedzo chimenechi.’ Ndiyeno anathamanga n’kukauza bambo ake kuti kwabwera a Mboni. Mfumuyo itamva zimenezi inauza mtsikanayo kuti adzatiitane ndipo tinapita koma tikuchita mantha kwambiri. Ndiyeno tisananene chilichonse, mfumuyo inatiuza kuti: ‘Ndimadziwa kuti chipembedzo chanuchi chimaphunzitsa zoona. Zaka 8 zapitazo ndinatola buku lofanana ndi limene mwapatsa mwana wangayu padzala linalake m’tauni ya Becerril. Mfundo zimene ndinawerenga m’bukulo zinandikhudza kwambiri moti ndinkafunitsitsa nditakumana nanu. Ndinkadziwa kuti tsiku lina mudzabwera. Ndiye popeza mwabwera tsopano, ndikufuna kuti mundiphunzitse Baibulo ineyo, banja langa komanso anthu a m’mudzi wangawu. Choncho, musamangike ayi, khalani omasuka ndithu.’”

M’bale Frank ananenanso kuti: “Titangomva mawu amenewa, zinatikhudza kwambiri moti misozi inalengeza m’maso. Anthu  a m’mudzi wonsewo atasonkhana tinayamba kuwalalikira. Popeza anthuwo sankamva chinenero chimene tinkayankhula, mfumu ija inayamba kumasulira. Titatsanzika, mfumuyo inatibwereka bulu wake kuti tinyamulirepo katundu wathu. Panopa timaphunzira Baibulo ndi anthu okwana 120 a m’mudziwo, ndipo timawaphunzitsa m’magulu okwana 47. Nayonso mfumu ija komanso mwana wake wamkazi uja amaphunzira nawo.”

Munthu Amene Ankazunza a Mboni Anasintha

A José, omwe poyamba anali m’tchalitchi cha Katolika, amakhala ku Ecuador. Tsiku lina a José analemba kalata. Iwo anati: “Ndinkadana kwambiri ndi a Mboni za Yehova moti ndinakhala ndikuwazunza kwa zaka 10. Nthawi zina ndinkawamenya, kuwanamizira kuti ndi akuba komanso ndinkasonkhanitsa anthu n’kuwauza kuti azivutitsa a Mboni za Yehova. A Mboni akamangidwa n’kupita nawo kundende, ndinkapita komweko ndipo ndinkauza apolisi kuti  nditseka ndine pakhomo la ndendeyo. Ndikukumbukira kuti nthawi ina tinaphwanya galimoto ya munthu wina wa Mboni. Komanso nthawi ina tinaponya njinga yamoto ya wa Mboni wina mumtsinje.”

A José ananenanso kuti: “Mu 2010, ndinayamba kudwala matenda a chimfine cha nkhumba. Nditapita kuchipatala, dokotala anandiuza kuti ngati ndikufuna kuti ndichire, ndisamuke kwathu kudera lamapiri komwenso ndi kozizira kwambiri ndipo ndipite kudera lina lotentha la m’mbali mwa nyanja. Choncho ndinapita kufamu ina ya wachibale wanga. Patapita nthawi wachibaleyu anandisiyira udindo woyang’anira famuyo. Pa nthawiyi ndinkakhala ndekhandekha, moti ndinkasowa wocheza naye. Tsiku lina kutabwera a Mboni za Yehova, ndinacheza nawo ndipo ndinadabwa ndi mmene ankagwiritsira ntchito Baibulo. Chifukwa choti ndinkafuna kudziwa zambiri, ndinavomera kuti azindiphunzitsa Baibulo. Nditaphunzira kwa miyezi 6, ndinapita kukasonkhana ndi a Mboni kwa nthawi yoyamba. Nditafika kumisonkhanoko, ndinadabwa kwambiri ndi zimene ndinaona. Anthu ake anandilandira bwino komanso anali achikondi moti ndinayamba kuganiza kuti, ‘Mwinatu amenewa angakhale Akhristu enieni.’ Ndinapitirizabe kuphunzira Baibulo ndipo ndinabatizidwa mu April 2014.”

Anapitiriza kufotokoza kuti: “Ndinkadzimvera chisoni kwambiri chifukwa cha zankhanza zomwe ndinachitirapo a Mboni. Ndinkafuna nditapepesa anthu amene ndinawachitira zimenezi ndipo Yehova anandithandiza. Mwachitsanzo, pamsonkhano wina wadera womwe unachitika pa 4 October, 2014 ndinafunsidwa kuti ndifotokoze zimene ndinkachita ndisanakhale wa Mboni. M’bale amene anakamba nkhaniyo anandifunsa kuti: ‘Mukanakhala ndi mwayi woti mupepese kwa anthu amene munkawazunza, kodi mukanakonda kupepesa ndani?’ Ndinayankha kuti ndikanakonda kupepesa m’bale wina, dzina lake Edmundo, koma sindinkadziwa kuti ndingamupeze bwanji. Pa nthawiyi sindinkadziwa kuti woyang’anira dera anali ataitana m’baleyu moti anali kuseri kwa pulatifomu. Edmundo atabwera papulatifomu, tinakumbatirana ndipo tonse tinayamba kulira.”

“Chonde Yehova, Nditumizireni a Mboni”

Paraguay: Mayi akufunsa alongo ngati ali a Mboni za Yehova

Alongo ena ankalalikira mumzinda wa Asunción m’dziko la Paraguay. Alongowa anamaliza chakumasana kulalikira gawo limene anapatsidwa. Ngakhale kuti kunkatentha kwambiri, alongowo anagwirizana zoti apitirizebe. Mlongo wina ananena kuti: “Mwina munthu  wina akupemphera kuti tikamulalikire.” Choncho alongowo anakalalikira kunyumba zina zapafupi. Ndiyeno alongo ena atafika panyumba inayake yapakona, mayi wina anawapatsa moni kwinaku akumwetulira ndipo anawafunsa ngati anali a Mboni za Yehova. Mayiyu anafotokoza kuti poyamba ankakhala m’dziko la Bolivia, koma chifukwa cha ntchito, anasamukira m’dziko la Paraguay ndipo anali atangotha mwezi umodzi. Ananena kuti ali ku Bolivia ankaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Ndiye atafika m’derali, anafunsa anthu oyandikana nawo nyumba kuti amuthandize kukumana ndi a Mboni, koma sanawapeze. Kenako anaganiza zopempha Yehova kuti amuthandize kukumana ndi a Mboni. Anamupempha kuti: “Chonde Yehova, nditumizireni a Mboni.” Tsiku limene anapempheralo ndi limene anakumana ndi alongo aja ndipo anagwirizana nawo kuti aziphunzira Baibulo.