Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016

Israel: Akulalikira za Ufumu wa Mulungu pogwiritsa ntchito tabuleti

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Ku Asia ndi ku Middle East

Ku Asia ndi ku Middle East
  • MAYIKO 49

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 4,409,131,383

  • OFALITSA 718,716

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 766,364

Analalikira Maola 100 Pokumbukira Zaka 100 Zimene Yesu Wakhala Akulamulira

M’dziko lina la ku Asia, mayi wina wotchuka pa nkhani ya mafilimu komanso mafashoni, anavomera kuti aziphunzira Baibulo ndi a Mboni. Atayamba kuphunzira, mayiyo anayamba kutsatira zimene ankaphunzirazo moti anataya mabuku a zamatsenga komanso mafano a chipembedzo chake chachibuda.

Mnzake wina wa mayiyu anadabwa kwambiri ndi zimenezi moti anamuuza  kuti: “Bwanji osasiya kaye kuphunzira Baibulo kwa zaka zitatu zokha kuti ugwire kaye ntchito yako? Kenako ukhoza kudzapitiriza kuphunzirako.”

Koma mayiyo anayankha kuti: “Ndakhala ndikufuna kuphunzira za Yehova kwa zaka 24. Ndiye ukundiuza kuti ndisiye kuphunzira kwa zaka zinanso zitatu? Chifukwa chiyani?”

Mayiyu anapitirizabe kuphunzira komanso kufika pamisonkhano ndipo analembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Koma mlungu womwe ankafunika kukamba nkhani yake yoyamba, akuluakulu a kampani ina yopanga mafilimu anamuimbira foni. Akuluakuluwo anamuuza kuti amulemba ntchito ya ndalama zambiri kwa zaka 4. Anamuuzanso kuti amulemba ntchito pokhapokha ngati atavomera kuti adzachita mbali iliyonse imene angamupatse m’filimuyo. Koma mayiyu anakana ntchitoyo. Pofika m’mwezi wa May 2014, anakhala wofalitsa wosabatizidwa ndipo pamene mwezi wa August unkayandikira, anaganiza zoti adzalalikire maola 100 m’mwezi umenewu. Anthu ena atamufunsa chifukwa chake akufuna kudzachita zimenezi, mayiyu anati: “Ndikuchita zimenezi pokumbukira nthawi imene Yesu wakhala akulamulira. Popeza Yesu wakhala akulamulira zaka 100, nanenso ndilalikira maola 100. Ndikachita zimenezi ndikhala ngati ndalalikira ola limodzi chaka chilichonse.” Mweziwo utafika, anakwanitsadi kulalikira maola 100. Mayiyu anabatizidwa m’mwezi wa January 2015, ndipo panopa ndi mpainiya wothandiza.

Analalikira Atatsekeredwa M’ndende

M’dziko la Sri Lanka, alongo 4 anakwera basi n’kupita kukalalikira kudera lina lomwe kulibe mpingo womwe umalalikirako. Kuderali kuli Abuda ambiri. Tsiku lachiwiri limene alongowa ankalalikira m’derali, anakumana ndi munthu wina wachibuda wodzipereka kwambiri komanso munthu wina woyendetsa takisi. Anthuwa anayamba kukalipira alongo athuwa. Kenako gulu la anthu pafupifupi 30, omwe anali atakwiya kwambiri, linafika pamalowo n’kuwazungulira. Pasanapite nthawi, kunabwera apolisi ndipo anagwira alongowo n’kupita nawo kupolisi. Apolisiwo  anatsekera alongowo m’ndende ngakhale kuti sanawapeze ndi mlandu uliwonse. Alongowo anaikidwa m’ndende ya zigawenga zoopsa zimene zinkawaopseza komanso kuwatukwana. Komabe kumangidwa kwa alongowa kunathandiza kuti anthu ena omwe anali m’ndendemo alalikidwe. Mlongo mmodzi anati: “Ngakhale kuti ananditsekera m’ndende ya zigawenga, sindinadandaule kwambiri chifukwa zinandipatsa mpata woti ndiwathandize kudziwa za Yehova. Anthuwo ankadabwa kwambiri kuti andimangiranji, ndipo ankafuna kudziwa zimene ndimakhulupirira. Munthu wina anandifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani ukuoneka wosangalala?’”

Sri Lanka: Alongo 4 atsika basi ndipo akukalalikira kudera lomwe sikulalikidwa

Zimenezi zitachitika, tinakasumira apolisi aja ku khoti lalikulu kwambiri la ku Sri Lanka chifukwa chomanga anthu popanda chifukwa chomveka bwino. Khotili linavomereza kuti liweruza mlanduwu. Panopa nkhaniyi idakali kukhoti.

Analalikira Mzimayi Amene Sadzuka Pabedi

Mpainiya wina wa ku Japan, dzina lake Michiko, ankaphunzira Baibulo ndi mayi wina wachikulire yemwe anagonekedwa pachipatala china. Ankaphunzira ndi mayiyo m’chinenero chamanja. Michiko anafunsa anthu ogwira ntchito pachipatalapo ngati panali odwala enanso omwe akanatha kuwalalikira. Ndiyeno tsiku lina, Michiko anakumananso ndi mayi ena dzina lawo a Kazumi. Mayiwa ankamva bwinobwino koma anali ndi vuto losayankhula. A Kazumi anachita ngozi ya galimoto ali ndi zaka 23, ndipo anavulala kwambiri moti sadzuka pabedi, satha kudya komanso satha kumwa madzi. Mayi Kazumi anali ndi mafunso ambiri moti atacheza ndi Michiko anavomera kuti azimuphunzitsa Baibulo.

Japan: Mayi Kazumi akulemba makalata olimbikitsa

Akamaphunzira Baibulo, Michiko ankafunsa mafunso ndipo a Kazumi ankagwiritsa ntchito dzanja lawo kuloza pamene pali yankho la funsolo. Nthawi zina ankangolemba yankho lawo papepala. A Kazumi atapeza foni, Michiko anayamba kukambirana nawo lemba la tsiku m’mawa uliwonse. Ngakhale kuti thupi lawo  linali lofooka, a Kazumi anapitirizabe kuphunzira moti anayamba kukonda kwambiri Yehova ndipo ankafuna atakhala a Mboni za Yehova. Ataphunzira kwa zaka 13, a Kazumi anakhala wofalitsa wosabatizidwa ndipo pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka 61.

Popeza a Kazumi sadzuka pabedi lawo, abale ndi alongo anakonza zoti mayiwa azimvetsera misonkhano ya mpingo komanso ikuluikulu kudzera pafoni. Mayi Kazumi amalemba ndemanga zawo ndipo alongo osiyanasiyana amakaziwerenga pa nthawi ya misonkhano.

Mayi Kazumi amalemba makalata olimbikitsa kwambiri ndipo amatumiza makalatawo kwa ophunzira Baibulo amene amapita kumisonkhano. Amalalikiranso anthu ogwira ntchito pachipatalacho komanso kwa anthu amene amabwera kudzawaona. Amakonda kuwauza kuti: “Mukhoza kukhala osangalala ngati mutamaphunzira Baibulo.”

 Mmonke Anaphunzira Baibulo

M’dziko lina la kum’mwera chakum’mawa kwa Asia, mlongo wina anapita kukaonana ndi dokotala wamaso, ndipo ali kumeneko, anakumana ndi mmonke wina. Mlongoyo anamufunsa kuti: “Kodi mumafuna mutakhala munthu wathanzi n’kukhala ndi moyo mpaka kalekale m’dziko lopanda mavuto?” Atacheza kwa kanthawi, mlongoyo anapatsa bamboyo kabuku kakuti, Mverani Mulungu. Bamboyo anapereka nambala yake ya foni kwa mlongoyo ndipo iye anakaipereka kwa m’bale wina wa kumpingo kwawo. Pasanapite nthawi yaitali, m’baleyo anaimbira foni bamboyu ndipo anamuitanira ku Nyumba ya Ufumu kuti akamvetsere nkhani yapadera. Iye anapitadi ndipo nkhaniyo itatha, ananena kuti anasangalala kwambiri ndi msonkhanowo, makamaka kuimba nawo nyimbo za Ufumu. Ananenanso kuti anachita chidwi chifukwa anthu ake anamulandira bwino kwambiri.

Bamboyu anafunsa ngati a Mboni amapita kukaphunzira zaubusa. Koma abale anamuuza kuti amaphunzira Baibulo ndi anthu ndipo ngati nayenso atafuna akhoza kumaphunzira naye. Iye anavomera kuti aziphunzira moti pamene mlungu umodzi unkatha, anali atamaliza kukonzekera mutu 1 wa m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Kenako anapitirizabe kuphunzira, kupita kumisonkhano ndipo ankapereka ndemanga pa phunziro la Nsanja ya Olonda.

Nthawi ina bamboyu anapita kumsonkhano wadera ndipo amene ankaimira ofesi ya nthambi pamsonkhanowo, anamuitana kuti akacheze ku Beteli. Mlungu wotsatira, bamboyo anayenda ulendo wa maola 10 kupita ku Beteli. Atafika kumeneko, abale ndi alongo anamulandira ndi manja awiri. Chakumapeto kwa mwezi wa February 2015, bamboyu anasiya chipembedzo chake ndipo akupitirizabe kuphunzira komanso kufika kumisonkhano.

Anayambanso Kuphunzira Baibulo Patapita Nthawi Yaitali

Pa nthawi ina apainiya ena anapemphedwa kupita kumpoto chakum’mawa kwa dziko la India, kuti akalalikire kudera lomwe linali lisanalalikidwe kwa nthawi yaitali. Apainiyawa atafika kumeneku, anapeza anthu ambiri achidwi ndipo anayamba kufufuza malo oti azichitira misonkhano. Ndiye tsiku lina akupita  kukachititsa phunziro, anaona nyumba ina yomwe inali yosamaliza kumanga. Apainiyawa anaganiza zofunsa ngati zinali zotheka kuti azichitiramo misonkhano, koma ankakayikira. Atapitirira nyumbayo anaganiza zobwerera kuti akafunse. Atafika panyumbayo n’kuzungulira kuseri, anakumana ndi mayi wina wachikulire ndipo anamuuza kuti ndi a Mboni za Yehova. Mayiyo atangomva zimenezo anasangalala kwambiri. Iye anati: “Inensotu ndi wa Mboni za Yehova.” Kenako anawauza kuti alowe m’nyumba ndipo anawaonetsa mabuku amene analandira m’ma 1970 komanso m’ma 1980. Kenako anawauza kuti ankaphunzira Baibulo ndi apainiya ena zaka 30 zapitazo. Anawauzanso kuti pa nthawiyo ankasonkhana ngakhale kuti mwamuna wake ankamutsutsa kwambiri. Mayiyu ananenanso kuti pa nthawi imene ankaphunzirayo, ankaona kuti zimene akuphunzirazo n’zoona kungoti apainiya aja anachoka ndipo sanakumanenso ndi wa Mboni wina. Ana ake onse 8  analowa m’matchalitchi osiyanasiyana, koma mayiyu sankapita kutchalitchi chilichonse.

India: Mayi wachidwi akuonetsa apainiya mabuku omwe analandira m’ma 1970 komanso m’ma 1980

Posachedwapa, ana a mayiyu ankamukakamiza kuti akayambe Chikatolika n’cholinga choti akadzamwalira, mwambo wa maliro ake udzayendetsedwe ndi anthu a m’tchalitchichi. Nawonso achemwali awo a mayiyu anawauza kuti tsiku lina adzabwera kudzawatenga kuti apite kukalembetsa kutchalitchi cha Katolika. Koma atanyamuka kuti akamutenge, mumsewu munali mutadzaza magalimoto moti anaganiza zongobwerera. Ndiye achemwali akewo anamuuza kuti apitanso tsiku lotsatira. Tsikuli litafika, achemwali akewo anadwala moti sanapitekonso. Masana a tsiku limeneli ndi pamene apainiya aja anabwera kunyumba kwake. Panopa mayiyu anayambanso kuphunzira Baibulo komanso amapita kumisonkhano. Amalimbikitsanso ana komanso zidzukulu zake kuti nawonso aziphunzira Baibulo.