Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016

England: Abale ndi alongo akulandira alendo omwe abwera kumsonkhano wa mayiko

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Europe

Europe
  • MAYIKO 47

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 743,421,605

  • OFALITSA 1,614,244

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 842,091

Anakumbatira Munthu Wina Poganiza Kuti ndi wa Mboni

Msonkhano wa mayiko womwe unachitikira mumzinda wa London ku England, unali wosangalatsa kwambiri kwa alendo komanso anthu okhala mumzindawo. M’bale Andrew ndi mkazi wake Elizabeth anapita ku hotela ina mumzinda wa London komwe kunkafikira alendo ochokera kumayiko ena n’cholinga choti akawapatse moni. Mlongo Elizabeth ataona mayi wina yemwe anavala bwino kwambiri, anaganiza kuti ndi wa Mboni ndipo anapita pamene anali n’kukamukumbatira  mwansangala. Mayiyo anadabwa ndi zimenezi, ndipo mlongoyo atazindikira kuti si wa Mboni, anamupepesa. Mlongoyo ananena kuti: “Pepani kwambiri, ndimaganiza kuti ndinu mmodzi wa anthu amene abwera kumsonkhano.”

Kenako mayiyo anamufunsa kuti: “Msonkhano wake uti?”

Mlongoyo analoza chikwangwani chomwe chinali pamalo olandirira alendo kuhotelako, chomwe analembapo kuti a Mboni za Yehova akulandiridwa kumsonkhano. Mayiyo ataona chikwangwanicho ananena kuti: “N’zosangalatsa bwanji! Ndiye kuti ndikuoneka ngati ndine wa Mboni eti?”

Anthuwa atacheza kwa kanthawi ndithu, Mlongo Elizabeth anadziwa kuti mayiyo dzina lake ndi Vivien, ndipo kwawo kwenikweni ndi ku Nigeria. Anazindikiranso kuti pa nthawiyi ankakhala nyumba zoyandikana. Mlongoyo atamupempha kuti aziphunzira naye Baibulo, mayiyo anavomera ndipo ananenanso kuti akufuna kuti ana ake aziphunzira nawo limodzi. M’bale Andrew ndi Mlongo Elizabeth anapita kunyumba kwa mayi Vivien ndipo anawalandira mwansangala. Zimene zinachitika ku hotela kuja zinachititsa kuti mayi Vivien akhale ndi mtima wofuna kuphunzira Baibulo. Banjali litasonyeza mayiyo buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, iye ananena kuti anali nalo kale ndipo ankaliwerenga ndi ana ake 4. Kenako banjalo linamufotokozera kuti buku limeneli ndi limene a Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo ndi anthu kwaulere. Pamenepo mayiyo ananena mosangalala kuti: “Tiyeni tiyambe pompano kuphunzira.”

Kalata Yochokera kwa M’bale Woyankhula Chiromane

Mu November 2014, mpingo woyamba wachinenero cha Chiromane unakhazikitsidwa m’dziko la Slovakia. Pamsonkhano wadera umene unachitika posachedwapa, ofalitsa 21 oyankhula Chiromane anabatizidwa ndipo onse anali ochokera m’mudzi umodzi. Komanso anthu 495 anapezeka pamwambo wa  Chikumbutso womwe unachitika m’Chiromane. M’bale wina amene anabatizidwa pamsonkhanowu analemba m’kalata yake kuti:

Slovakia: Ofalitsa awiri akulalikira uthenga wabwino kwa mzimayi wolankhula Chiromane

“Ndimakhala m’mudzi wotchedwa Žehra, m’dziko la Slovakia, ndipo ndimayankhula Chiromane. Kumene ndimakhala, anthu ena omwe si a mtundu wathu amatisala ndipo amaona kuti ndife anthu auve, akuba komanso onama. Tsiku lina nditapita kutchalitchi chinachake anakandibweza pakhomo n’kundiuza kuti siine woyenera kulowa m’tchalitchimo. Zimene anachitazi zinandikhumudwitsa kwambiri moti kungoyambira pamenepo, sindinkagwirizana kwenikweni ndi anthu a mitundu ina. Kenako ndinakumana ndi a Mboni za Yehova omwe anandiitanira ku Nyumba ya Ufumu. Ngakhale kuti ndinavomera, koma popita ndinkangoganiza kuti a Mboni adzachitanso zimene akutchalitchi china chija anandichitira. Ndiye nditangolowa m’Nyumba ya Ufumu, ndinadabwa kuona munthu wina wochokera mu mtundu womwe anthu ake anandichitira zatsankho uja, akundipatsa moni wapamkono ndipo anandilandira bwino kwambiri. Kunena zoona, sindinamvetsere bwinobwino nkhani yomwe inkakambidwa chifukwa mumtima ndinkangodzifunsa kuti, ‘Zikutheka bwanji kuti aliyense azisangalala nane chonchi?’

“Usiku umenewo sindinagone chifukwa ndinkangoganizira mmene anthu anandilandirira ku Nyumba ya Ufumu. Choncho ndinaganiza zoti ndidzapitenso ku Nyumba ya Ufumu kuti ndikatsimikizire kuti kundilandira kumene anachita sikunangochitika mwangozi koma ndi mmene amachitira nthawi zonse. Nditapita, ndinadabwa kuona kuti ulendo umenewunso anthu anandilandira bwino kuposa ulendo woyamba uja ndipo zinkangokhala ngati tinadziwana kalekale. Kuyambira tsiku limenelo sindinasiye kupita kumisonkhano. Kenako pasanapite nthawi yaitali, ndinabatizidwa. Nditabatizidwa, abale sanasiye kundichitira zabwino ndipo zimene amandichitira zimasonyeza kuti amaona kuti ndine wofunika. Nthawi zinanso amandikonzera chakudya chabwino kwambiri kuposa chimene iwowo amadya. Ndine wosangalala kukhala m’gulu la Yehova ndipo ndikufuna kumutumikira kwa moyo wanga wonse.”

 Mulungu Anayankha Pemphero Lake Loti Athe Kulalikira

Tsiku lina Mlongo Aysel, wa m’dziko la Azerbaijan, anayenda ulendo wa pa basi kuchokera m’tauni ya Ganja kupita mumzinda wa Baku. Mlongoyu anali atapempha Yehova kuti amuthandize kupeza munthu woti amulalikire pa ulendowu. Aliyense m’basimo anapatsidwa mpando woti akhalepo. Koma pamene mlongo Aysel ankapita kuti akakhale pampando wake, mayi wina anamuchonderera kuti akhale pampando woyandikana naye. Mlongoyu atakhala pafupi ndi mayiyu, anayamba kucheza naye moti kenako anakambirana nkhani za m’Baibulo. Mayiyo anafotokoza kuti amakonda Yesu ndipo amafuna kudziwa zambiri zokhudza Yesuyo. Pamene ankasiyana, anapatsana manambala a foni ndipo anakonza zoti adzakumanenso ulendo wina. Mayiyo anapemphanso mlongoyu kuti adzamubweretsere Baibulo.

Mlongo Aysel atabwerera mumzinda wa Ganja, anayendera mayi uja ndipo anakamupeza ali kuntchito. Mayiyo anafotokoza kuti anali ndi kabuku kenakake kamapemphero kamene amawerenga tsiku lililonse. Kenako mlongoyu anadabwa ataona kuti kabuku kamene mayiyo ankanena kanali kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku ka chaka cha 2013. Mlongo Aysel anayamba kuphunzira Baibulo ndi mayiyu ndipo anasangalala kwambiri chifukwa choti Yehova anamuthandiza kuti alalikire m’basi.

Kalata Yothokoza Yochokera kwa Munthu Amene Ali Kundende

Munthu wina amene ali kundende m’dziko la Spain analemba kalata iyi:

“Poyamba ndikufuna kukuthokozani chifukwa cha khama lanu poyesetsa kufikira anthu onse ndi uthenga wa m’Baibulo.

“Ndinakumana koyamba ndi a Mboni za Yehova zaka 15 zapitazo ndili mumzinda wa Tiranë, m’dziko la Albania. Pa nthawiyo ndinadabwa kwambiri kuona wa Mboni atalimba mtima kudzayankhula nane chifukwa ndinali pa gulu la achinyamata 10 omwe anali zigawenga. Palibe munthu amene ankalimba mtima kuyankhula ndi achinyamata a m’kagulu kathuko koma m’baleyo  analimba mtima ngakhale anali ataona kuti tinali ndi zida. Iye anatifotokozera mfundo za m’Baibulo mopanda mantha. Zimene anachitazo zinandisangalatsa kwambiri.

“Zaka 4 zapitazo, wa Mboni winanso anabwera kudzacheza nane kundende kuno ndipo anandipempha kuti aziphunzira nane Baibulo. Ndinayamba kuphunzira Baibulo moti panopa ndasintha kwambiri. Sindichitanso ndewu komanso zinthu zankhanza. Tsopano papita zaka zambiri ndisanalowenso m’mavuto. Ndayamba kumudziwa Yehova ndipo zimenezi zandithandiza kumvetsa chifukwa chake ndili ndi moyo. Panopo ndimayesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu ndipo ndakhala wofalitsa wosabatizidwa kwa chaka chimodzi tsopano.

“Ndakhala m’ndende kwa zaka 12 tsopano, koma pa zaka 4 zapitazi, kuphunzira Baibulo kwandithandiza kukhala wosangalala komanso kukhala ndi mtendere wa mumtima kusiyana ndi kale lonse. Ndimathokoza kwambiri Yehova tsiku lililonse.

“Milungu ingapo yapitayi ndinaonera mavidiyo pawebusaiti ya jw.org. Nditaonera vidiyo ya m’bale wina amene anakhala m’ndende m’dziko la United States, zinandikhudza kwambiri. Mwachibadwa ndine munthu wolimba mtima moti sindimva chisoni choti mpaka n’kulira. Koma nditaona mmene m’baleyu anasinthira ndinagwetsa misozi.

 “Pemphero langa ndi lakuti, Yehova azikudalitsani kuti mupitirize kuthandiza anthu a mitundu yonse pamene mukumasulira uthenga wabwino m’zinenero zambiri. Komanso apitirize kukudalitsani chifukwa choyesetsa kulalikira anthu amene tili m’ndendefe.

“Zikomo kwambiri.”

“Tsopano Ndili Ndi Mtendere wa Mumtima”

Mayi wina wa ku Sweden, dzina lake Felicity, ali ndi zaka 68. Iye ananena kuti: “Kuyambira kale ndakhala ndikuona kuti moyo ulibe tanthauzo moti ndinalibe mfundo zenizeni zimene ndinkayendera pa moyo wanga.” Chifukwa choti sankasangalala ndi zimene ankaphunzira m’tchalitchi cha Katolika, mayiyu anayamba kufufuza zimene zipembedzo zinanso zimaphunzitsa. Kenako anayamba kukhulupirira za ufiti komanso kuyamba kuwombeza.

Ataona kuti zimene ankachitazi sizinkamuthandiza, anakhumudwa kwambiri moti anaganiza zongodzipha. Mayiyu ananena kuti: “Tsiku limene ndinkafuna kudziphalo, ndinapemphera mokweza mawu kwa Mulungu, kwinaku ndikulira ndipo ndinamupempha kuti andiuze zimene akufuna kuti ndichite. Patapita milungu iwiri ndinamva kugogoda pachitseko cha nyumba yanga. Nditatsegula chitsekocho, ndinaona kuti amene amagogodayo anali mnyamata ndipo ankamwetulira. Mnyamatayo anandipempha kuti akambirane nane Mawu a Mulungu. Pansi pa mtima ndinanena kuti, ‘Mulungu, ndinakupemphani kuti mundithandize koma osati kudzera mwa a Mboni za Yehova ayi.’”

Ngakhale kuti poyamba ankangofuna kutseka chitsekocho, anamvetsera komanso anavomera kuti ayambe kuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Mayiyu ananena kuti: “Anandifotokozera mfundo za m’Baibulo momveka bwino ndipo zimenezi zinandithandiza kwambiri.” Mayi Felicity anabatizidwa pamsonkhano wachigawo womwe unachitika m’dziko la Sweden m’chaka cha 2014. Atabatizidwa ananena kuti: “Ndakhala ndikufuna choonadi kwa moyo wanga wonse. Tsopano ndachipeza ndipo ndili ndi mtendere wa mumtima.”