Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Burundi: Nolla akusonyeza magazini a Nsanja ya Olonda kwa azibambo awiri amene anabwera kudzapala moto

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Africa

Africa
  • MAYIKO 58

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 1,082,464,150

  • OFALITSA 1,453,694

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 3,688,959

Amalalikira Anthu Okwera Njinga

Benin: Désiré amagwiritsa ntchito kawailesi komwe anaika panjinga yake kuti azilalikira makasitomala ake uthenga wabwino

Anthu ambiri amene amakhala m’mizinda yakum’mwera kwa dziko la Benin, amakonda kuyenda panjinga zamoto zomwe zimadziwika ndi dzina lakuti zem. Nayenso M’bale Désiré, yemwe akuchita upainiya wothandiza, amanyamula anthu panjinga ndipo anaika kawailesi pafupi ndi pamene makasitomala amakhala. Kenako amaika sewero linalake la nkhani ya m’Baibulo kapena zinthu zina za m’Baibulo zongomvetsera. Anthu amachita  chidwi kwambiri moti nthawi zina amati akafika kumene akutsikira, safuna kutsika mpaka atamaliza kumvetsera. M’bale Désiré anati: “Ngakhale kuti ndimafuna kuti anthu andilipire msanga ndalama kuti ndinyamulenso munthu wina, koma ndimawalola kuti amalize kumvetsera. Ndimachita zimenezi chifukwa ndimadziwa kuti uthenga umene athuwa amamvetsera ndi wofunika kwambiri kuposa ndalama. Ndimagawiranso mabuku ambiri kwa anthu amene ndawanyamula panjinga.”

Kamtsikana Kakhama

Nolla ali ndi zaka 6 ndipo amakhala ndi makolo ake m’dera la mapiri m’dziko la Burundi. Tsiku lina mayi ake akuphika chakudya pambaula yamakala, kunafika azibambo awiri. Azibambowo ankagwira ntchito pa nyumba ina yoyandikana nawo ndipo anabwera kuti adzapale moto. Pa nthawiyo azibambowo anapeza kamtsikanaka ndipo kanawalola kuti apale motowo. Patapita nthawi yochepa, Nolla anadutsa pamene panali azibambowo koma anadabwa kwambiri ataona kuti moto umene anapala uja unali woti ayatsire ndudu. Iye anakhumudwa kwambiri moti anauza azibambo aja kuti: “Ndikanadziwa kuti mumadzapala moto kuti muyatsire ndudu, sindikanakulolani.” Kenako anakumbukira kuti anaona magazini ku Nyumba ya Ufumu omwe anali ndi chithunzi cha ndudu. Choncho nthawi yomweyo, anapita ku Nyumba ya Ufumuko n’kukatenga magazini awiri a Nsanja ya Olonda a June 1, 2014, omwe amafotokoza za kusuta. Nolla anapereka magaziniwo kwa azibambowa ndipo anawapempha kuti awawerenge. Patapita nthawi, Nolla anakumananso ndi azibambowo n’kuwaitanira kumsonkhano wachigawo. Atachita chidwi ndi khama la kamtsikanaka, azibambowa anaganiza zopita kumsonkhanoko kwa masiku  awiri. Ali kumsonkhanoko, pa nthawi ya chakudya chamasana, Nolla anaona azibambo aja ndipo anawaitana kuti adzadye nawo chakudya. Azibambowo anasangalala ndi zimene anaona komanso nkhani zimene anamva kumsonkhanoko moti onse anayamba kuphunzira Baibulo.

Amalalikira Kundende

M’dziko la Liberia, akulu amalalikira uthenga wa Ufumu m’ndende zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, M’bale Yves ndi mpainiya wapadera mumzinda wa Monrovia, womwe ndi likulu la dzikoli. Iye ananena kuti: “M’mwezi wa March akaidi atatu anavomerezedwa kukhala ofalitsa osabatizidwa. Panopa m’ndende ya Monrovia Central Prison muli ofalitsa 6.” Kodi ofalitsa amenewa amakwanitsa bwanji kuti azilalikira? M’bale Yves anati: “Ofalitsawa amakumana Lachitatu komanso Loweruka lililonse kuti akalalikire. Akakonzekera amayamba kuyenda selo iliyonse n’kumalalikira kwa akaidi anzawo.” Panopa akaidi ambiri akuphunzira Baibulo ndipo amakhala nawo pamisonkhano yomwe imachitikira m’ndendemo. Nthawi ina, m’bale wina woimira ofesi ya nthambi anakamba nkhani kundendeko ndipo anthu 79 anamvetsera nkhaniyo. Abale akuchititsanso maphunziro a Baibulo m’ndende zina 6 ndipo zimenezi zikuthandiza kwambiri anthu amene anamangidwa.

“Tikufunika Thandizo Mwamsanga”

M’dziko la Namibia, abale ndi alongo anachita khama kwambiri pofuna kuthandiza anthu omwe amakhala kumadera akutali kuti akapezeke pamwambo wa Chikumbutso. Mwachitsanzo, m’dzikoli muli anthu a mtundu wa Sani kapena kuti Bushmen omwe ndi anthu oyambirira kukhala kum’mwera kwa Africa. Poyamba anthuwa ankakhala moyo  wongoyendayenda ndipo kuti apeze chakudya ankasaka nyama komanso kudya zipatso zam’thengo. Mu 2015, M’bale Glenn, yemwe ndi mpainiya wapadera ndipo akutumikira kumpoto kwa dzikoli, anakonza zoti Chikumbutso chichitikire m’mudzi wina wa a Sani. Mudziwu uli pamtunda wa makilomita 270 chakum’mawa kwa mzinda wa Rundu. Kameneka kanali kachiwiri kuti mwambowu uchitikire m’derali. Maulendo onse awiri, akuluakulu a m’mudziwo analoleza a Mboni za Yehova kuti agwiritse ntchito khoti kuti achitiremo mwambo wa Chikumbutso koma kwaulere. Anthu okwana 232 anapezeka pamwambowu ngakhale kuti kunkagwa mvula yamphamvu. Anthu a mtundu wa Sani amayankhula chinenero chotchedwa Chikhwe, choncho nkhani ya Chikumbutso anaimasulira m’chinenerochi. Popeza palibe Baibulo la chinenerochi, abale anakonza zoti azionetsa zithunzi pakhoma pofotokoza malemba ngati Yesaya 35:5, 6. Panopa M’bale Glenn amachititsa maphunziro ambiri m’derali. Iye anati: “Ndakhala ndikubwera kuno kamodzi pa mwezi, kwa zaka ziwiri, ndipo ndimakhoma tenti n’kukhala kuno kwa masiku angapo. Komabe maphunziro sapita patsogolo kwenikweni chifukwa n’kutali komanso chifukwa cha chinenero. Choncho, tikufunika thandizo mwamsanga. Mwachitsanzo, chaka chino nditapita kukapempha chilolezo kwa akuluakulu a mudziwo kuti tichite mwambo wa Chikumbutso, mmodzi wa akuluakuluwo anandipempha kuti timange nyumba yoti tizichitiramo misonkhano. Ananenanso kuti akuluakuluwo akhoza kutipatsa malo komanso kumanga nyumbayo ndi ndalama za m’thumba mwawo. Ndipo ifeyo tingopeza ‘m’busa’ kapena tiphunzitse mmodzi mwa akuluakuluwa kuti akhale m’busa.”

Namibia: Ofalitsa awiri akulalikira uthenga wabwino kwa mayi wachihimba