Okondedwa Abale ndi Alongo:

Mneneri Yesaya ananena kuti Yehova ndi amene ankathandiza mtundu wa Yuda kuti zinthu ziziwayendera bwino. Lemba la Yesaya 26:12 limati: “Inu Yehova, . . . ntchito zathu zonse tazikwanitsa chifukwa cha inu.” Tikaona zinthu zonse zimene takwanitsa kuchita m’chaka cha utumiki chapitachi, nafenso tikuona kuti zonsezi zatheka chifukwa cha Yehova. Kunena zoona, Yehova akuchita ‘zinthu zodabwitsa zimene sizinachitikepo.’ (Eks. 34:10) Tiyeni tione zina mwa zinthu zimene Yehova watichitira chaka chathachi.

Webusaiti yathu ya jw.org, yatithandiza kwambiri. Panopa webusaitiyi ikupezeka m’zinenero 600 ndipo anthu akhoza kuwerenga mabuku komanso kukopera zinthu zina m’zinenero zoposa 750. Koma kodi webusaitiyi ikuthandizadi anthu kudziwa Yehova? Inde. Mwachitsanzo, banja lina linakhumudwa chifukwa cha zinthu zachinyengo zimene anthu a m’chipembedzo chawo ankachita. Banjali linayamba kufufuza chipembedzo choona ndipo linapeza adiresi ya webusaiti yathuyi. Kenako anayamba kuwerenga nkhani komanso kuonera mavidiyo athu pa webusaitiyi. Anapanganso dawunilodi kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku ndipo ankakawerenga limodzi ndi ana awo awiri. Ndiyeno tsiku lina akukambirana mfundo za m’kabukuka, a Mboni za Yehova anagogoda pakhomo lawo. Banjali linauza a Mboniwo kuti webusaitiyi yawathandiza kuti asinthe zinthu zambiri pa moyo wawo. Ananena kuti anafufuta zimene  anadzilembalemba pathupi lawo ndiponso anachotsa ndolo zambirimbiri zimene ankavala. Anachotsanso zithunzi zonse za kutchalitchi kwawo komanso anasiya kuchita nawo maholide. Banjali linasiyanso kuonera mafilimu oipa ndipo zonsezi zinachitika asanakumane ndi a Mboni. Pamene kalatayi imalembedwa, n’kuti bambo ndi mayi a m’banjali komanso mwana wawo mmodzi ali ofalitsa osabatizidwa ndipo bambo ndi mayiwo akufuna atabatizidwa posachedwapa.

Anthu ambiri akuthokozanso chifukwa cha TV yathu ya JW Broadcasting. Pulogalamu yomwe imatuluka mwezi uliwonse pa TV imeneyi, amaimasulira m’zinenero zoposa 70 ndipo posachedwapa iyamba kumasuliridwa m’zinenero zinanso. Mabanja ambiri amaonera pulogalamu imeneyi pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja. M’bale wina anati: “Gulu la Yehova likutipatsa zinthu zambiri zabwino ndipo tikutha kudziwa bwino abale a ku likulu lathu kuposa kale lonse.”

Chaka chilichonse, abale ndi alongo amasangalala kwambiri ndi misonkhano yachigawo ndipo chaka chapitachi anasangalalanso ndi msonkhanowu chifukwa unali wapadera kwambiri. Pamsonkhanowu panaonetsedwa zithunzi zokongola komanso mavidiyo okwana 42. Kwa masiku onse atatu, tinasangalalanso kumvetsera nyimbo zokoma kwambiri zomwe zinkaikidwa m’mawa komanso masana nkhani zisanayambe kukambidwa. M’bale wina amene wakhala akutumikira Yehova kwa zaka zambiri anati: “Anthu sankayendayenda msonkhano uli mkati chifukwa sankafuna kuti zina ziwadutse.” Mlongo wina yemwe ndi mmishonale anasangalalanso ndi msonkhanowu. Iye anati: “Mavidiyo omwe tinaonera pamsonkhanowu anandithandiza kumvetsa zimene ndimaphunzira komanso kuti ndisamakayikire Ufumu wa Mulungu.”

 Chaka chathachi, Yehova anatipatsanso nyimbo zingapo zatsopano. Banja lina linati: “Nyimbo zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amatikonda kwambiri chifukwa tikamaimba nyimbozi timaiwalako mavuto athu.” Pamsonkhano wa chaka chatha tinauzidwanso zimene abale ndi alongo amachita kuti nyimbozi zikonzedwe. Abale ndi alongowa amagwira ntchito mwakhama kuti ifeyo tipindule komanso kuti dzina la Yehova lilemekezedwe.

Tikukupemphani nonse kuti muzilandira bwino anthu amene akufuna kubwerera m’gulu la Yehova potengera mmene Yehovayo amachitira

Kodi mpingo wanu unayamba kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala? Kulalikira pogwiritsa ntchito njira imeneyi ndi kothandiza kwambiri. Tikutero chifukwa njirayi ikuthandiza kuti anthu ena omwe amakhala m’nyumba zokhala ndi mipanda komanso m’nyumba zosanja, nawonso azilalikiridwa. Komanso anthu ena ambiri kuphatikizapo a Mboni omwe anasiya kusonkhana, athandizidwanso ndi njirayi. Mwachitsanzo, mu January 2015, bambo wina wa ku South Korea anapita pamene abale ankalalikira pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala. Ananena kuti akufuna atamvetsa mfundo zina za m’Baibulo. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo moti m’mwezi wa February, anafika koyamba pamsonkhano wa Mboni za Yehova. Pofika mwezi wa March, munthuyo anasiya kusuta. M’mwezi wotsatira wa April, anapita kukaona ofesi ya nthambi ya ku South Korea ndipo panopa akupitirizabe kuphunzira Baibulo. Chimenechi ndi chitsanzo chimodzi chokha mwa nkhani zambiri zolimbikitsa zomwe tinalandira kuno kulikulu lathu.

Tikukhulupirira kuti malangizo amene tinalandira pamsonkhano wa chaka chatha, athandiza anthu ambiri amene anasiya kusonkhana nafe kuti abwererenso kwa atate wathu wachikondi Yehova, madzi asanafike m’khosi. Tikukupemphani nonse kuti muzilandira bwino anthu amene akufuna kubwerera m’gulu la Yehova potengera mmene Yehovayo amachitira.—Ezek. 34:16.

 Apatu n’zoonekeratu kuti Yehova watithandiza kwambiri m’chaka cha utumiki chathachi. Tikuyembekezera kuti chaka cha utumiki tachiyambachi, chiyendanso bwino. Pomaliza, tikufuna kukuuzani kuti ife a m’Bungwe Lolamulira timakukondani kwambiri komanso timakupemphererani.

Tikukufunirani zabwino zonse,

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova