PAMENE chaka cha 1916 chinkayamba, n’kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse itachitika pafupifupi kwa zaka ziwiri. Anthu ambiri a m’mayiko amene ankamenyana, anafa pa nkhondoyi.

Nsanja ya Olonda ya January 1, 1916, inanena kuti: “Nkhondoyi ikuchititsa kuti anthu azikhulupirira kwambiri Mulungu komanso kuti aziganizira za tsogolo lawo. Choncho tiyeni tiziyesetsa kugwiritsa ntchito mwayi umene tili nawo komanso zinthu zimene tili nazo kuti tikhale ndi chikhulupiriro champhamvu komanso kuti tizikonda Mulungu ndiponso ntchito imene watipatsa.”

Lemba la chaka cha 1916 linalimbikitsa abale ndi alongo kuti akhale “olimba m’chikhulupiriro,” ndipo linachokera pa Aroma 4:20 m’Baibulo la King James Version. Ophunzira Baibulo ambiri anachitadi zimenezi ndipo Yehova anawadalitsa kwambiri.

Oyang’anira Oyendayenda Analimbikitsa Abale

Abale omwe anatumizidwa ndi Watch Tower Society, ankayendera mipingo m’madera osiyanasiyana ndipo ankalimbikitsa komanso kupereka malangizo kwa Ophunzira Baibulo. M’chaka cha 1916, abale pafupifupi 69 anayenda makilomita oposa 800,000 akugwira ntchitoyi.

 M’bale Walter Thorn, yemwe anali woyang’anira woyendayenda, anayerekezera nkhondoyi ndi nkhondo yauzimu pamene ankakamba nkhani mumzinda wa Norfolk ku Virginia m’dziko la United States. M’baleyu anati: “Panopa pali anthu 20 kapena 30 miliyoni amene ali kunkhondo. . . . Koma palinso asilikali ena omwe anthu a m’dzikoli sakuwadziwa. Amenewa ndi asilikali a Ambuye. Mofanana ndi gulu la asilikali a Gidiyoni, nawonso akumenya nkhondo koma osati ndi zida zenizeni. Akumenyera nkhondo choonadi ndi chilungamo komanso akumenya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro chawo.”

Sanafooke Chifukwa cha Nkhondo

Pa nthawi ya nkhondo yomwe inachitika m’dera la Somme m’dziko la France, asilikali oposa 1 miliyoni anavulazidwa kapena kuphedwa. Nkhondoyi inachitika chakumapeto kwa chaka cha 1916. Ngakhale kuti anthu ankakumana ndi mavuto ambiri chifukwa cha nkhondoyi, abale omwe ankakhala m’madera ena a dzikoli sanasiye kusonkhana ndi anzawo. Mwachitsanzo, mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1916, munali kalata ya M’bale Joseph Lefèvre imene inafotokoza zimene zinachitika pa nthawi ya nkhondoyi.  M’baleyu anali wophunzira Baibulo ndipo mu 1914 anathawa mumzinda wakwawo ku Denain m’dziko la France. Pa nthawiyi asilikali a dziko la Germany anali ataukira mzindawo. Iye anathawira kum’mwera kwa mzinda wa Paris ndipo atafika kumeneko, anayamba kusonkhana ndi Ophunzira Baibulo ena. Ngakhale kuti m’baleyu ankadwaladwala, anayamba kuchititsa misonkhano yonse.

Kenako, kuderali kunabweranso m’bale wina, dzina lake Théophile Lequime, amenenso anathawa nkhondoyi ku Denain. Poyamba M’bale Lequime anathawira m’dera la Auchel m’dziko lomwelo la France, ndipo ali kumeneko ankamasulira nkhani za mu Nsanja za Olonda n’kuzitumiza kwa abale ndi alongo amene ankakhala m’madera omwe anali asanalandidwe ndi asilikali a dziko la Germany. M’baleyu anaganiza zochoka kumeneku atazindikira kuti akuluakulu a asilikali ayamba kukayikira zimene ankachita. M’bale Lequime atafika ku Paris, M’bale Lefèvre anasangalala kwambiri chifukwa anaona kuti Yehova wayankha pemphero lake pomupatsa munthu woti agwire naye ntchito.

Ntchito imene abalewa anagwira ku Paris inathandiza kwambiri. M’kalata imene M’bale Lefèvre analemba ija anati: “Panopa tili ndi kagulu ka anthu pafupifupi 45. . . . Ambiri mwa anthuwa amaona kuti kusonkhana n’kofunika ndipo akuchita zinthu mwakhama potumikira Yehova. Pafupifupi anthu 45 onsewa, amabwera mlungu uliwonse pamsonkhano umene timakambirana zinthu zimene takumana nazo.”

Sanalowerere Nkhondo

Pamene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inkafika pampondachimera, abale ambiri ankakakamizidwa kuti apite kunkhondo. Mwachitsanzo, ku Britain, boma linakhazikitsa lamulo loti mwamuna aliyense wazaka 18 mpaka 40 ayenera kukalembetsa kuti akamenye nawo nkhondo. Koma Ophunzira Baibulo ambiri sanachite nawo zimenezi.

Mwachitsanzo, mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1916, munalembedwa kalata ya M’bale W. O. Warden wa ku Scotland. Iye anati: “Mwana wanga wina wangokwanitsa kumene zaka 19. Ndikuona kuti mwanayu wasankha bwino kwambiri chifukwa wakana kulembetsa usilikali. Ndikukhulupirira kuti Yehova amuthandiza kuti akhalebe wokhulupirika ngakhale atauzidwa kuti aphedwa chifukwa chokana kukamenya nawo nkhondoyi.”

 Nayenso James Frederick Scott wa mumzinda wa Edinburgh ku Scotland, yemwe anali kopotala kapena kuti mpainiya, anaimbidwa mlandu chifukwa chokana kulembetsa usilikali. Khoti litamvetsera mlanduwu linagamula kuti m’baleyu ndi wosalakwa chifukwa “malamulo a dziko la Scotland amalola kuti munthu asakamenye nawo nkhondo pa zifukwa zina.”

Komabe, abale ambiri sanaloledwe kukagwira ntchito zina. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya October 15, 1916, inanena zimene zinachitika pofika mu 1916. Inanena kuti pa abale 264 amene anapempha kuti asakamenye nawo nkhondoyi, abale 23 okha ndi amene anapatsidwa ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali. Ndipo ena otsalawo, “omwe poyamba anazunzidwa ndi asilikali,” anauzidwa kuti azikagwira “ntchito zina zachitukuko monga kumanga misewu ndi kuphwanya miyala.” Abale 5 okha ndi amene anauzidwa kuti malamulo akuwalola kuti asamenye nawo nkhondoyo.

Imfa ya Charles Taze Russell

Pa 16 October  1916, M’bale Charles Taze Russell, yemwe ankatsogolera Ophunzira Baibulo, ananyamuka pa ulendo wopita chakumadzulo kwa dziko la United States kuti akakambe nkhani m’madera osiyanasiyana. Koma n’zomvetsa chisoni kuti m’baleyu anamwalira ali pa ulendowu, chakumasana kwa Lachiwiri pa 31 October. M’bale Russell anamwalira ali m’sitima m’dera la Pampa ku Texas ali ndi zaka 64.

Abale atamva za nkhaniyi anasokonezeka kwambiri moti sankadziwa munthu amene angalowe m’malo mwa M’bale Russell. Zimene M’bale Russell analemba mu wilo yake zinasindikizidwa mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1916. Mu wiloyi analembanso zokhudza ntchito imene anakhala akuitsogolera kwa zaka zambiri. Komabe funso linali lakuti: Kodi ndani amene ayambe kutsogolera ntchitoyi?

Yankho la funso limeneli linadziwika pamsonkhano wa pachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, womwe unachitika chakumayambiriro kwa chaka cha 1917. Anthu amene anali pamsonkhanowu anauzidwa kuti avotere munthu amene akufuna kuti akhale pa udindowu, ndipo ambiri anavotera munthu mmodzi. Koma patangopita miyezi yochepa zinthu zinasintha kwambiri ndipo abale anayamba kukumana ndi mayesero aakulu.